4 | Baibo Ili na Malangizo Othandiza
BAIBO IMATI: “Malemba onse ni . . . opindulitsa.”—2 TIMOTEYO 3:16.
Tanthauzo Lake
Ngakhale kuti Baibo si buku la zacipatala, lili na malangizo amene angathandize munthu amene akudwala matenda a maganizo. Onani zitsanzo izi.
Mmene Zimenezi Zingatithandizile
“Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—MATEYU 9:12.
Baibo imaonetsa kuti nthawi zina timafunika thandizo la kucipatala. Anthu ambili odwala matenda a maganizo, apeza thandizo mwa kupita ku cipatala na kufufuza kuti adziŵe zoona zenizeni zokhudza matenda awo.
“Kucita masewela olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”—1 TIMOTEYO 4:8.
Kucita zinthu zimene zingakuthandizeni kukhala na thanzi labwino, kungacititse kuti vuto lanu la matenda a maganizo licepeko. Zinthu zimenezi zingaphatikizepo kucita maseŵela olimbitsa thupi, kudya zakudya zopatsa thanzi na kugona mokwanila.
“Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—MIYAMBO 17:22.
Kuŵelenga malemba olimbikitsa na kudziikila zolinga zimene mungathe kuzikwanilitsa kungakuthandizeni kukhala acimwemwe. Kuwonjezela apo, kuganizila zinthu zolimbikitsa komanso kukhala na ciyembekezo cakuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo, kungakuthandizeni kupilila matenda anu a maganizo.
“Nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.”—MIYAMBO 11:2.
Nthawi zina mungaone kuti panokha mukulephela kucita zonse zimene mukufuna. Conco, muzikhala okonzeka kulandila thandizo kwa ena. Anzanu komanso a m’banja lanu amafuna kukuthandizani. Koma nthawi zina sangadziŵe mmene angakuthandizileni. Cotelo, auzeni thandizo limene mukufuna. Musamayembekezele zambili kwa iwo, ndipo nthawi zonse muziyamikila thandizo lawo.
Mmene Malangizo a m’Baibo Akuthandizila Odwala Matenda a Maganizo
“N’namva kuti cinacake sicinali bwino m’thupi mwanga. Conco, n’napita kukaonana na dokotala. Dokotalayo analipeza vuto langa. Izi zinanithandiza kulidziŵa bwino vutolo komanso kupeza thandizo loyenelela lacipatala.”—Nicole,a amene ali na matenda a maganizo ocititsa munthu kusintha-sintha mmene amamvela (bipolar disorder).
“Naona kuti kuŵelenga Baibo nthawi zonse na mkazi wanga kumanithandiza kuyamba tsiku lililonse na maganizo abwino komanso olimbikitsa. Conco, nthawi zambili nikapsinjika maganizo, pamakhala vesi inayake imene imanilimbikitsa.”—Peter, amene ali na matenda a kupsinjika maganizo.
“Zinali zovuta kuuzako ena za vuto langa, cifukwa n’nali kucita manyazi kwambili. Koma mnzanga wina anali kunimvetsela mokoma mtima na kuyesetsa kumvetsa mmene n’nali kumvela. Iye ananithandiza kuti nizimvelako bwino, komanso kuti nisamadzione kuti nili nekha.”—Ji-yoo, amene ali na vuto la kadyedwe.
“Baibo yanithandiza kuti nisamagwile nchito mopitilila muyeso komanso kuti nizipeza nthawi yokwanila yopumula. Malangizo anzelu a m’Baibo anithandiza kupilila matenda anga a maganizo, amene amanisautsa nthawi zonse.”—Timothy, amene ali na matenda opangitsa munthu kucita zinthu mobweleza-bweleza (obsessive-compulsive disorder).
a Maina ena asinthidwa.