LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp23 na. 1 masa. 12-13
  • 4 | Baibo Ili na Malangizo Othandiza

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 4 | Baibo Ili na Malangizo Othandiza
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Tanthauzo Lake
  • Mmene Zimenezi Zingatithandizile
  • Mmene Malangizo a m’Baibo Akuthandizila Odwala Matenda a Maganizo
  • Matenda a Maganizo ni Mlili wa Padziko Lonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • 3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Mmene Tingathandizile Odwala Matenda a Maganizo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Kodi Baibo Inganithandize Bwanji mu Umoyo Wanga?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
wp23 na. 1 masa. 12-13
Mzimayi wacimwemwe akuchova njinga.

4 | Baibo Ili na Malangizo Othandiza

BAIBO IMATI: “Malemba onse ni . . . opindulitsa.”—2 TIMOTEYO 3:16.

Tanthauzo Lake

Ngakhale kuti Baibo si buku la zacipatala, lili na malangizo amene angathandize munthu amene akudwala matenda a maganizo. Onani zitsanzo izi.

Mmene Zimenezi Zingatithandizile

“Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—MATEYU 9:12.

Baibo imaonetsa kuti nthawi zina timafunika thandizo la kucipatala. Anthu ambili odwala matenda a maganizo, apeza thandizo mwa kupita ku cipatala na kufufuza kuti adziŵe zoona zenizeni zokhudza matenda awo.

“Kucita masewela olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”—1 TIMOTEYO 4:8.

Kucita zinthu zimene zingakuthandizeni kukhala na thanzi labwino, kungacititse kuti vuto lanu la matenda a maganizo licepeko. Zinthu zimenezi zingaphatikizepo kucita maseŵela olimbitsa thupi, kudya zakudya zopatsa thanzi na kugona mokwanila.

“Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—MIYAMBO 17:22.

Kuŵelenga malemba olimbikitsa na kudziikila zolinga zimene mungathe kuzikwanilitsa kungakuthandizeni kukhala acimwemwe. Kuwonjezela apo, kuganizila zinthu zolimbikitsa komanso kukhala na ciyembekezo cakuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo, kungakuthandizeni kupilila matenda anu a maganizo.

“Nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.”—MIYAMBO 11:2.

Nthawi zina mungaone kuti panokha mukulephela kucita zonse zimene mukufuna. Conco, muzikhala okonzeka kulandila thandizo kwa ena. Anzanu komanso a m’banja lanu amafuna kukuthandizani. Koma nthawi zina sangadziŵe mmene angakuthandizileni. Cotelo, auzeni thandizo limene mukufuna. Musamayembekezele zambili kwa iwo, ndipo nthawi zonse muziyamikila thandizo lawo.

Mmene Malangizo a m’Baibo Akuthandizila Odwala Matenda a Maganizo

“N’namva kuti cinacake sicinali bwino m’thupi mwanga. Conco, n’napita kukaonana na dokotala. Dokotalayo analipeza vuto langa. Izi zinanithandiza kulidziŵa bwino vutolo komanso kupeza thandizo loyenelela lacipatala.”—Nicole,a amene ali na matenda a maganizo ocititsa munthu kusintha-sintha mmene amamvela (bipolar disorder).

Mzimayi akukambilana na dokotala.

“Naona kuti kuŵelenga Baibo nthawi zonse na mkazi wanga kumanithandiza kuyamba tsiku lililonse na maganizo abwino komanso olimbikitsa. Conco, nthawi zambili nikapsinjika maganizo, pamakhala vesi inayake imene imanilimbikitsa.”—Peter, amene ali na matenda a kupsinjika maganizo.

“Zinali zovuta kuuzako ena za vuto langa, cifukwa n’nali kucita manyazi kwambili. Koma mnzanga wina anali kunimvetsela mokoma mtima na kuyesetsa kumvetsa mmene n’nali kumvela. Iye ananithandiza kuti nizimvelako bwino, komanso kuti nisamadzione kuti nili nekha.”—Ji-yoo, amene ali na vuto la kadyedwe.

“Baibo yanithandiza kuti nisamagwile nchito mopitilila muyeso komanso kuti nizipeza nthawi yokwanila yopumula. Malangizo anzelu a m’Baibo anithandiza kupilila matenda anga a maganizo, amene amanisautsa nthawi zonse.”—Timothy, amene ali na matenda opangitsa munthu kucita zinthu mobweleza-bweleza (obsessive-compulsive disorder).

a Maina ena asinthidwa.

Vidiyo yakuti “Zimene Mungacite Kuti Muyambilenso Kusangalala.”
Kuti Mupeze Thandizo Lowonjezeleka:

Onelelani vidiyo yakuti Zimene Mungacite Kuti Muyambilenso Kusangalala pa jw.org ku Chichewa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani