LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp23 na. 1 masa. 10-11
  • 3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Tanthauzo Lake
  • Mmene Zimenezi Zingatithandizile
  • 2 | “Malemba . . . Amatilimbikitsa”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • 4 | Baibo Ili na Malangizo Othandiza
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • 1 | Pemphelo—“Mutulileni Nkhawa Zanu Zonse”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Yehova Amakukondani Kwambili!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
wp23 na. 1 masa. 10-11
Mneneli Mose ni wovutika maganizo, ndipo akupemphela kwa Mulungu atayang’ana kumwamba.

3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni

BAIBO IMAFOTOKOZA ZA . . . Amuna na akazi okhulupilika amene anali “anthu monga ife tomwe,” ndipo anamvelapo mmene ife timamvela.—YAKOBO 5:17.

Tanthauzo Lake

M’Baibo muli nkhani zambili za amuna na akazi amene anavutikapo maganizo m’njila zosiyanasiyana. Pamene tiŵelenga nkhani zawo, tingapezemo wina amene anamvela mmene ife timamvela.

Mmene Zimenezi Zingatithandizile

Tonse timafuna kuti ena azitimvetsetsa. Zimenezi n’zofunika kwambili maka-maka ngati tikuvutika na matenda a maganizo. Tikamaŵelenga Baibo, timapezamo nkhani za anthu amene anali kuganiza na kumva mmene ife timamvela. Nkhanizi zimatithandiza kuzindikila kuti enanso anavutikapo mmene ife tikuvutikila. Ndipo timadziŵa kuti sindife tokha amene tikuvutika na nkhawa komanso maganizo osautsa.

  • M’Baibo muli mawu ambili okambidwa na anthu amene anasoŵa mtengo wogwila mpaka kutaya mtima. Kodi munaganizapo kuti, ‘Basi natopa nazo. Cili bwino kufa cabe’? Mose, Eliya, na Davide, nawonso anamvapo conco.—Numeri 11:14; 1 Mafumu 19:4; Salimo 55:4.

  • Baibo imatiuza za mayi wina dzina lake Hana, amene “anali wokhumudwa kwabasi” cifukwa analibe ana, ndipo anali kutonzedwa mwakhanza na mkazi mnzake.—1 Samueli 1:6, 10.

  • Baibo imatiuzanso za munthu wina, dzina lake Yobu, amene anamvapo mmene ife tingamvele. Ngakhale kuti anali na cikhulupililo colimba mwa Yehova, iye anasautsika mtima kwambili cifukwa ca mavuto, moti panthawi ina anati: “Moyo ndaukana. Sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Yobu 7:16.

Tikaona mmene anthu ochulidwa m’Baibo amenewa anakwanitsila kulimbana na nkhawa zawo, timapeza mphamvu zotithandiza kupilila mavuto athu.

Mmene Baibo Imathandizila Kevin

Mmene Nimavutikila na Matenda Anga a Maganizo

Kevin akumwa khofi na anzake aŵili.

“Nili pafupi kukwanitsa zaka 50, ananipeza na matenda a maganizo amene amacititsa kuti nizisintha-sintha mmene nimamvela. Nthawi zina nimakhala wosangalala, ndipo nimaona kuti ningakwanitse kuthana na vuto lililonse limene ningakumane nalo pa umoyo. Koma nthawi zina nimakhala wacisoni kwambili, moti nimaona kuti palibenso cifukwa copitilizila kukhala na moyo.”

Mmene Baibo Imanithandizila

“Mmodzi wa anthu ochulidwa m’Baibo amene anamvelapo mmene ine nimamvela ni mtumwi Petulo. Iye analakwitsapo zinthu zina zimene zinam’pangitsa kudziona wacabe-cabe. Koma m’malo momangoganizila zolakwa zake, Petulo anali kuyanjana na anzake amene anali kumukonda. Vuto langa likakula, nimadziimba mlandu kwambili cifukwa ca zolakwa zanga, cakuti nimadziona ngati wosafunika. Mofanana na Petulo, nimayesetsa kuyanjana na anzanga, amene amanithandiza kuti nipitilize kupilila.

“Munthu wina wa m’Baibo amene citsanzo cake cimanilimbikitsa kwambili ni Mfumu Davide. Nthawi zambili, iye anali kukhala wopsinjika maganizo cifukwa ca mavuto, komanso anali kudziimba mlandu cifukwa ca zolakwa zake. Nimamvetsa mmene Davide anali kumvela, cifukwa nanenso nthawi zina nimakamba kapena kucita zinthu zimene pambuyo pake nimadziimba nazo mlandu. Mawu a Davide a pa Salimo 51 amanilimbikitsa. Pa vesi 3, Davide anati: ‘Zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino, ndipo chimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.’ Vesiyi ifotokoza bwino mmene nimamvela nikapsinjika maganizo kwambili, cifukwa zimakhala zovuta kudziona moyenela panthawiyo. Koma nimakumbukilanso mawu a Davide a pa vesi 10, pamene anati: ‘Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.’ Inenso nimakamba mawu monga amenewa pocondelela Mulungu kuti anithandize kudziona moyenela. Pamapeto pake, mawu a pa vesi 17 amanitonthoza. Vesiyi imati: ‘Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.’ Mawu amenewa amanitsimikizila kuti Mulungu amanikonda.

“Kusinkhasinkha zitsanzo za m’Baibo na kuganizila zimene Mulungu wanipatsa palipano, kumalimbitsa ciyembekezo canga ca tsogolo labwino. Conco, nimaona kuti malonjezo a m’Baibo si nkhambakamwa cabe, ndipo izi zimanithandiza kupitiliza kupilila.”

Kuti Mupeze Thandizo Lowonjezeleka:

Ŵelengani nkhani yakuti “Kukhala ndi Matenda a Maganizo,” mu Galamukani! ya January 8, 2004, pa jw.org ku Chichewa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani