LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp23 na. 1 masa. 8-9
  • 2 | “Malemba . . . Amatilimbikitsa”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 2 | “Malemba . . . Amatilimbikitsa”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Tanthauzo Lake
  • Mmene Zimenezi Zingatithandizile
  • 3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2023
wp23 na. 1 masa. 8-9
Mwamuna wacikulile akusinkhasinkha zimene waŵelenga m’Baibo.

2 | “Malemba Amatilimbikitsa”

BAIBO IMATI:“Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. ­Malembawa amatipatsa ciyembekezo cifukwa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.”—AROMA 15:4.

Tanthauzo Lake

M’Baibo muli mfundo zolimbikitsa, zimene zingatithandize tikakhala na maganizo olefula. Komanso Baibo imatipatsa ciyembekezo cakuti posacedwa, zinthu zopweteka mtima zidzatha.

Mmene Zimenezi Zingatithandizile

Tonsefe nthawi zina timakhala osakondwa. Koma anthu odwala matenda opsinjika maganizo kapena ankhawa, angamakhale owawidwa mtima nthawi zonse. Kodi Baibo ingawathandize bwanji?

  • M’Baibo muli mfundo zambili zolimbikitsa zimene zingatithandize kucotsa maganizo olefula mumtima mwathu (Afilipi 4:8) Baibo ingadzaze mitima yathu na maganizo otonthoza komanso otsitsimula, amene angatikhazike mtima pansi.—Salimo 94:18, 19.

  • Baibo imatithandiza kuthetsa maganizo odziona ngati osafunika.—Luka 12:6, 7.

  • M’Baibo muli malemba ambili amene amatitsimikizila kuti sitili tokha, komanso kuti Mlengi wathu Mulungu amamvetsa mmene tikumvela.​—Salimo 34:18; 1 Yohane 3:19, 20.

  • Baibo imalonjeza kuti Mulungu adzathetsa zowawa zonse, moti sizidzakumbukilidwanso. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4) Tikakhala na nkhawa, mantha, kapena cisoni, komanso tikamavutika maganizo cifukwa ca mavuto amene tikukumana nawo, lonjezo limeneli lingatithandize kupilila.

Mmene Baibo Imathandizila Jessica

Mmene Nimavutikila na Matenda a Kupsinjika Maganizo

Jessica wagona ali na Baibo yotsegula m’manja.

“Nili na zaka 25, n’nayamba kukhala na nkhawa kwambili komanso kulephela kucita zinthu bwino-bwino. Ndipo ananipeza na matenda aakulu a kupsinjika maganizo. N’nali kuvutika cifukwa cokumbukila zinthu zoipa komanso zopweteka mtima zimene zinanicitikilapo. Zinthu zimenezo zinali kungobwela m’maganizo mwanga mosayembekezeleka. Madokotala ananithandiza kudziŵa kuti vuto langa la kupsinjika maganizo, linayamba cifukwa n’nali kungoganizila zinthu zoipa zimene zinanicitikilapo pa umoyo wanga. Kuwonjezela pakulandila mankhwala a kucipatala, n’nafunikanso mlangizi wonithandiza kuzindikila maganizo olefula na kuwathetsa.”

Mmene Baibo Imanithandizila

“Nikapsinjika kwambili maganizo, n’nali kuvutika kupuma, kuda nkhawa kwambili, komanso kusoŵa tulo. Kambili usiku, n’nali kukhala na nkhawa cifukwa cakuti maganizo osautsa anali kuniculukila. Monga mmene lemba la Salimo 94:19 limakambila, Mulungu amatitonthoza tikapanikizika maganizo cifukwa ca nkhawa. Conco, n’nali kuika Baibo na kabuku kamene n’nali kulembamo malemba olimbikitsa pafupi na bedi langa. Nikalephela kugona, n’nali kuŵelenga mavesi a m’Baibo. Kucita zimenezi kunali kuthandiza kuti Yehova anilimbikitse poseŵenzetsa Mawu ake.

“Baibo imatilimbikitsa kucotsa maganizo amene sagwilizana na zimene tidziŵa ponena za Mulungu. Kumbuyoku n’nali kuona kuti ndine wosafunika, wopanda nchito, komanso wosanunkha kanthu. Koma n’naphunzila kuti zimene n’nali kukhulupilila zinali zosiyana na zimene Baibo imakamba. Baibo imaonetsa kuti Mulungu ni Tate wacikondi komanso wacifundo amene amasamala za aliyense wa ife payekha-payekha. M’kupita kwanthawi, n’nayamba kulamulila maganizo anga m’malo mowalola kuti azinilamulila. N’naphunzila kudziona mmene Yehova amanionela. Kucita zimenezi kunanithandiza kuti niyambe kudziona moyenela.

“Niyembekezela mwacidwi nthawi pamene zopweteka zonse sizidzakumbukilidwanso, ndipo sitidzadwalanso matenda a maganizo. Kudziŵa kuti matenda a maganizo adzatha kumanithandiza kupilila vuto langa palipano. Kumanithandizanso kuyembekezela mwacidwi nthawi pamene sinidzavutikanso na matenda a kupsinjika maganizo.”

Kuti Mupeze Thandizo Lowonjezeleka:

Ŵelengani nkhani yakuti “‘Mulungu Wacitonthozo Conse’ Amathandiza” mu Galamukani! ya July 2009 pa jw.org ku Chichewa.

Ŵelengani buku la Masalimo pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani