LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 2 masa. 6-7
  • 1. Kodi Mulungu Ndiye Amabweletsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 1. Kodi Mulungu Ndiye Amabweletsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho
  • Zofunika Kuganizila
  • Zimene Baibo Imakamba
  • Zamkati
    Galamuka!—2020
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nanga N’ndani Amapangitsa Mavuto?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
Onaninso Zina
Galamuka!—2020
g20 na. 2 masa. 6-7
Wansembe wanyamula Baibo kumanja, pamene akucititsa mwambo wamalilo m’chechi ndipo olila akumvetsela.

1. Kodi Mulungu Ndiye Amabweletsa Mavuto Amene Timakumana Nawo?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Anthu ambili safuna kutumikila Mulungu cifukwa amamuimba mlandu wakuti iye ndiye amapangitsa mavuto.

Zofunika Kuganizila

Mwacindunji kapena mwa njila ina, atsogoleli acipembedzo ambili amaphunzitsa kuti Mulungu ndiye amapangitsa mavuto amene timakumana nawo. Mwacitsanzo, ena amakamba izi:

  • Matsoka a zacilengedwe ni cilango cocokela kwa Mulungu.

  • Ana amafa cifukwa cakuti Mulungu afuna angelo ambili kumwamba.

  • Mulungu amathandiza mbali imodzi pankhondo. Ndipo izi zimabweletsa mavuto aakulu.

Kodi sizotheka kuti zimene atsogoleli acipembedzo amaphunzitsa ponena za Mulungu n’zabodza? Kodi tingaŵakhulupililebe ngati Mulungu anaŵakana cifukwa ca zimene amaphunzitsa?

DZIŴANI ZAMBILI

Tambani vidiyo yakuti: N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibo? pa jw.org.

Zimene Baibo Imakamba

Mulungu si ndiye amapangitsa mavuto amene timakumana nawo.

Kucita zimenezi kungakhale kosagwilizana na makhalidwe ake amene Baibo imakamba. Mwacitsanzo:

“Njila zake zonse [Mulungu] ndi zolungama. . . . Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”—DEUTERONOMO 32:4.

“Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono!”—YOBU 34:10.

“Wamphamvuyonse sakhotetsa cilungamo.”—YOBU 34:12.

Mulungu amakana zipembedzo zimene zimaphunzitsa zabodza zokhudza iye.

Izi ziphatikizapo zipembedzo zimene zimaphunzitsa kuti Mulungu ndiye amacititsa mavuto amene timakumana nawo, komanso amene amatengako mbali pankhondo na ciwawa.

“Aneneliwo akulosela monama m’dzina langa [Mulungu]. Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo. Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama, . . . ndi cinyengo ca mumtima mwawo.”—YEREMIYA 14:14.

Yesu anadzudzula mkhalidwe wacinyengo wa zipembedzo.

“Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akucita cifunilo ca Atate wanga wakumwamba. Ambili adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosele m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kucita nchito zambili zamphamvu m’dzina lanunso?’ Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: ‘Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Cokani pamaso panga, anthu osamvela malamulo inu!’” —MATEYU 7:21-23.

Kodi Mulungu ndiye amabweletsa mavuto amene timakumana nawo?

Tiyelekeze kuti tate ali ndi ana, ndipo amaŵapezela zofunikila. Patapita nthawi, mmodzi wa anawo wasankha kucoka pakhomo, kenako wayamba makhalidwe oipa odziwononga. Kodi atate ake ndiye anapangitsa mwanayo kuyamba makhalidwe oipa? Kodi mwanayo angaimbe mlandu atate ake pa zotulukapo zoipa zimene wakumana nazo? Mofananamo, sitingaimbe Mulungu mlandu kaamba ka mavuto athu.

Koma kodi izi zitanthauza kuti ife eni ndiye timapangitsa mavuto?

Onani funso 2.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani