LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 2 masa. 12-13
  • 4. Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 4. Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho
  • Zofunika Kuganizila
  • Zimene Baibo Imakamba
  • Zamkati
    Galamuka!—2020
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kodi Zoipa Komanso Mavuto Zinakhalako Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Onaninso Zina
Galamuka!—2020
g20 na. 2 masa. 12-13
Banja lapita kukaceza kumapili. Iwo akudzikopa pikica ndipo kumbuyo kwawo kukuoneka mapili.

4. Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?

Cifukwa Cake Tifunika Kupeza Yankho

Yankho ya funso iyi ikhudza mmene timaonela moyo.

Zofunika Kuganizila

Kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu amene analenga zinthu zokongola angalole kuti anthufe tizivutika?

Cifukwa ca mavuto, anthu osapembedza amayamba kukaikila zolinga za Mulungu, komanso zakuti iye aliko. Iwo amakhulupilila kuti mavuto amaonetsa kuti mwina (1) Mulungu alibe mphamvu zakuti awacotsepo, (2) Mulungu sasamala za ife kuti acotsepo mavuto, kapena (3)  Mulunguyo kulibe.

Kodi zifukwa zimenezi n’zoona?

DZIŴANI ZAMBILI

Tambani vidiyo yakuti, Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona? pa jw.org.

Zimene Baibo Imakamba

Mulungu sanatilenge kuti tizivutika ayi.

Iye amafuna kuti tizikondwela nawo moyo.

“Palibe cabwino kuposa kuti [anthu] asangalale ndiponso azicita zabwino pamene ali ndi moyo, komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, cifukwa coti wagwila nchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.”—MLALIKI 3:12, 13.

Mulungu anapatsa anthu aŵili oyambilila zonse zofunikila kuti akhale na umoyo wabwino.

Iye sanafune kuti iwo kapena ana awo azivutika.

‘Mulungu anawauza kuti: Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.’ —GENESIS 1:28.

Anthu aŵili oyambilila anasankha kupandukila Mulungu.

Zotulukapo zake n’zakuti iwo anadzibweletsela mavuto ambili kuphatikizapo ana awo onse.

“Monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.”—AROMA 5:12.a

Mulungu sanatilenge na mphamvu zakuti tizidzilamulila tekha.

Sitinalengedwe kuti tizidzilamulila, monga mmene sitinalengedwele kuti tizikhala m’madzi.

“Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.”—YEREMIYA 10:23.

Mulungu safuna kuti anthufe tizivutika.

Iye amafuna kuti tikhale na umoyo wopewa mavuto.

“Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje.”—YESAYA 48:18.

a M’Baibo, liwu lakuti “ucimo” limatanthauza zoipa zimene munthu angacite, komanso mkhalidwe umene anthu onse anatengela.

Kodi tinalengedwa kuti tizivutika?

Iyai. Sicinali cifunilo ca Mulungu kuti anthufe tizivutika. Mavuto anayamba pamene anthu aŵili oyambilila anasankha kusamvela Mulungu. Koma izi sizitanthauza kuti anthu adzapitilizabe kuvutika mpaka kalekale.

Kodi mavuto athu adzatha?

Onani funso 5.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani