LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 1 masa. 4-5
  • Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Amuna, Muzikonda Akazi Anu
  • Akazi, Muzilemekeza Amuna Anu
  • Khalani Wokhulupilika kwa Mnzanu Wam’cikwati
  • Makolo, Phunzitsani Ana Anu
  • Ana, Muzimvela Makolo Anu
  • Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Zimene Muyenela Kucita Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 1
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Galamuka!—2021
g21 na. 1 masa. 4-5
Banja la cimwemwe lili pamodzi ku msika.

Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe

Cikwati komanso ana ni mphatso zamtengo wapatali zocokela kwa Mlengi wathu. Iye amafuna kuti tizikhala acimwemwe m’banja. Conco kupitila m’buku lakale lopatulika, watipatsa malangizo amene angatithandize kukhala na mabanja abwino komanso acimwemwe. Ganizilani malangizo anzelu otsatilawa.

Amuna, Muzikonda Akazi Anu

“Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” —AEFESO 5:28, 29.

Mwamuna ndiye mutu wa banja. (Aefeso 5:23) Koma mwamuna wabwino sakhala wankhanza kapena woumitsa zinthu. Amaona kuti mkazi wake ni wofunika, ndipo amam’samalila bwino mwakuthupi na kumuonetsa cikondi. Amacitanso zonse zotheka kuti am’kondweletse, osati nthawi zonse kuumilila pa kucita zofuna zake. (Afilipi 2:4) Amakambilana na mkazi wake momasuka, ndipo amamumvetsela akamakamba. ‘Samupsela mtima kwambili’ kapena kumumenya, ngakhale kumukambila mawu oipa.—Akolose 3:19.

Akazi, Muzilemekeza Amuna Anu

“Mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.”—AEFESO 5:33.

Ngati mkazi amalemekeza mwamuna wake na kucilikiza zisankho zake, m’banja mumakhala mtendele. Mwamuna akalakwitsa, iye samupeputsa. Koma amakhalabe wofatsa ndiponso waulemu. (1 Petulo 3:4) Mkazi akafuna kufotokoza vuto linalake kwa mwamuna wake, amasankha nthawi yabwino yocita zimenezo, ndipo amakamba naye mwaulemu.—Mlaliki 3:7.

Khalani Wokhulupilika kwa Mnzanu Wam’cikwati

‘Mwamuna. . . adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’—GENESIS 2:24.

Mwamuna na mkazi akakwatilana, amapanga mgwilizano wa banja wolimba kwambili. Conco mwamuna na mkazi ayenela kucita khama kuti cikwati cawo cikhalebe colimba. Angacite zimenezi mwa kukambilana mocokela pansi pa mtima na kucitilana zinthu zabwino. Ayenelanso kukhala okhulupilika kwa wina na mnzake mwa kupewa kugonana na munthu amene si mkazi kapena mwamuna wawo. Kusakhulupilika m’banja ni nkhanza. Kumapangitsa kuti okwatilana asamakhulupililane, ndipo kungathetse banja.—Aheberi 13:4.

Makolo, Phunzitsani Ana Anu

“Phunzitsa mwana m’njila yomuyenelela. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—MIYAMBO 22:6.

Mulungu anapatsa makolo udindo wophunzitsa ana awo. Izi ziphatikizapo kuwaphunzitsa makhalidwe abwino, komanso kuwapatsa citsanzo cabwino. (Deuteronomo 6:6, 7) Mwana akacita zosayenela, kholo lanzelu silikalipa mopitilila malile. Ilo limakhala ‘lofulumila kumva, lodekha polankhula, losafulumila kukwiya.’ (Yakobo 1:19) Kholo likaona kuti m’pofunika kupeleka cilango kwa mwana, limacita zimenezo mwacikondi osati mwaukali.

Ana, Muzimvela Makolo Anu

“Ananu, muzimvela makolo anu . . . ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’” —AEFESO 6:1, 2.

Ana ayenela kumvela makolo awo na kuwalemekeza kwambili. Ngati ana amalemekeza makolo awo, m’banja mumakhala cimwemwe cacikulu, ndipo zimathandiza kuti mukhale mtendele na mgwilizano. Ana akulu-akulu amalemekeza makolo awo mwa kuonetsetsa kuti makolowo akusamalidwa bwino. Zimenezi zingaphatikizepo kuwathandiza kusamalila panyumba kapena kuwapatsa thandizo la ndalama.—1 Timoteyo 5:3, 4.

N’nakhala Mwamuna Wabwino

“Cifukwa ca mmene n’nakulila, n’nali woumitsa zinthu kwambili. Koma n’naphunzila kuti pokhala mutu wabanja, niyenela kumvetsela zokamba za mkazi wanga, ndipo niyenela kupewa kukhala wodzikonda kapena wopondeleza. Pamaso pa Mulungu, iye na ine ndise thupi limodzi, ndipo niyenela kucita naye zinthu monga thupi langa. Niyamikila kwambili malangizo anzelu amenewa. Anithandiza kukhala mwamuna wabwino, ndipo nili na banja lacimwemwe.”—Rahul.

Rahul na mkazi wake.

Phunzilani zambili:

Kuti mudziŵe malangizo owonjezeleka a mmene mungakhalile na banja lacimwemwe, pitani pa jw.org ku Chichewa na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU OKWATIRANA KOMANSO MABANJA.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani