LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 1 masa. 6-7
  • Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendele na Anthu Ena

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendele na Anthu Ena
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Khalani Okhululuka
  • Khalani Odzicepetsa Komanso Aulemu
  • Khalani Opanda Tsankho
  • Khalani Ofatsa
  • Khalani Opatsa Komanso Oyamikila
  • Opatsa Mowoloŵa Manja Amakhala Acimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Umoyo wa Banja Komanso Mabwenzi
    Galamuka!—2019
  • Musapunthwitse “Tianati”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Tingatengele Bwanji Kukhululuka kwa Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 1 masa. 6-7
Banja laitanila anthu ena ku nyumba kwawo kuti adzadye nawo cakudya ca madzulo.

Malangizo Otithandiza Kukhala Mwamtendele na Anthu Ena

Mlengi wathu amatiuza zimene tingacite kuti tizikhala mwamtendele na anthu ena, kaya panyumba, kunchito, kapena na anzathu. Onani ena mwa malangizo ake anzelu amene athandiza anthu ambili.

Khalani Okhululuka

“Pitilizani. . . kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake.”—AKOLOSE 3:13.

Tonse timalakwitsa nthawi zina. Tingakhumudwitse ena, kapena iwo angatikhumudwitse. Mulimonsemo, tonse timafunika kukhululukila anzathu, ndipo timafunanso kuti iwo azitikhululukila. Tikakhululukila munthu amene watilakwila, sitimusungila mkwiyo. Sitibwezela “coipa pa coipa”, ndipo sitikhalila kum’kumbutsa za colakwa cake. (Aroma 12:17) Koma bwanji ngati zimene munthuyo anacita zinatiŵaŵa kwambili, ndipo tikulephela kuziiŵalako? Zikakhala conco, tiyenela kukamba naye munthuyo mwaulemu za nkhaniyo tili aŵili. Pokambilana, tiyenela kukhala na colinga cokhazikitsa mtendele, osati kuwina mkangano.—Aroma 12:18.

Khalani Odzicepetsa Komanso Aulemu

‘Modzicepetsa, onani ena kukhala okuposani.’—AFILIPI 2:3.

Tikakhala odzicepetsa komanso aulemu, anthu amakondwela kukhala nafe. Amadziŵa kuti tidzacita nawo zinthu mokoma mtima komanso mowaganizila. Amadziŵanso kuti sitingacite mwadala zinthu zowakhumudwitsa. Koma ngati timadziona apamwamba kuposa ena, kapena ngati nthawi zonse timafuna kuti zinthu ziziyenda mmene tikufunila, timayambitsa mikangano na kukwesana. Zotulukapo zake, anthu amayamba kutipewa. Ndipo timakhala na mabwenzi ocepa, mwinanso kukhala opanda bwenzi lililonse.

Khalani Opanda Tsankho

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.

Mlengi wathu sakondela anthu ena cifukwa ca dziko lawo, cinenelo cawo, cuma cimene ali naco, kapena cifukwa ca khungu lawo. “Kucokela mwa munthu mmodzi, [iye] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26) Conco tingakambe kuti anthu onse ni pacibale. Tikamacita zinthu mwaulemu komanso mokoma mtima na anthu onse, timawapangitsa kukhala acimwemwe. Nafenso timakhala acimwemwe, ndipo timakondweletsa Mlengi wathu.

Khalani Ofatsa

“Valani. . . kufatsa.”—AKOLOSE 3:12.

Ngati ndife ofatsa, anthu amamasuka nafe. Amakhala omasuka kukamba nafe, ngakhale kutiwongolela tikalakwitsa cifukwa amadziŵa kuti sitidzakhumudwa. Munthu wina akatikwiyila, tiyenela kumuyankha modekha. Tikatelo tingam’thandize kubweza mkwiyo wake. Miyambo 15:1 imati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”

Khalani Opatsa Komanso Oyamikila

“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—MACHITIDWE 20:35.

Anthu ambili masiku ano ni adyela ndipo amangoganizila za iwo okha basi. Koma anthu opatsa ndiwo amakhala na cimwemwe ceniceni. (Luka 6:38) Anthu opatsa amakhala acimwemwe cifukwa amakonda anthu kuposa zinthu zakuthupi. Cikondi cimeneco n’cimene cimawalimbikitsa kukhala oyamikila, na kuonetsa kuyamikila kwawo munthu akawapatsa zinthu. (Akolose 3:15) Dzifunseni kuti, ‘Ni munthu wotani amene nimakonda kukhala naye? Womana komanso wosayamikila, kapena wopatsa komanso woyamikila?’ Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tiphunzilapo kuti tiyenela kucitila anthu zinthu zimene timafuna kuti nawonso aziticitila.—Mateyu 7:12.

N’naleka Kuona Anthu Ena Ngati Otsika

“Malemba amati: ‘Tiziona ena mmene ifeyo timadzionela . . . Tisadziyese anzelu.’“ (Aroma 12:16) “Malangizo amenewa ananithandiza kuthetsa khalidwe la kunyada na cizoloŵezi coona ena ngati otsika. Lomba sinionanso kuti anthu a mtundu wathu ndiwo abwino kuposa anthu a mitundu ina. Ndipo siniona anthu a zipembedzo zina ngati otsika. Kuwonjezela apo, ndine waubwenzi tsopano ndipo nimamasuka kupeleka moni kwa ena.”—Asha.

Asha.

Phunzilani zambili:

Kuti mudziŵe malangizo owonjezeleka a mmene mungakhalile mwamtendele na anthu ena, pitani pa jw.org ku Chichewa na kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MTENDELE KOMANSO MOYO WOSANGALALA > KUKHALA BWINO NDI ANTHU.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani