LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 February masa. 14-19
  • Tingatengele Bwanji Kukhululuka kwa Yehova?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tingatengele Bwanji Kukhululuka kwa Yehova?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUSAPONDELEZE MKWIYO WANU
  • ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUTHETSA MKWIYO
  • ZIMENE MUNGACITE KUTI MUZIONA ZINTHU MOYENELA
  • MUZIGANIZILA MAPINDU OBWELA CIFUKWA COKHULULUKILA ENA
  • Yehova “Amacilitsa Anthu Osweka Mtima”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kuyandikila Abale ndi Alongo Athu n’Kwabwino Kwa Ife!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Yehova Amadalitsa Amene Amakhululukila Anzawo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 February masa. 14-19

NKHANI YOPHUNZILA 8

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

Tingatengele Bwanji Kukhululuka kwa Yehova?

“Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso muzicita cimodzimodzi.”​—AKOL. 3:13.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

M’nkhani ino tikambilane masitepe amene angatithandize kukhululukila munthu amene watilakwila.

1-2. (a) Ndi pa nthawi iti makamaka pamene zimakhala zovuta kukhululukila munthu? (b) Kodi Denise anaonetsa bwanji kuti ndi wokhululuka?

KODI cimakuvutani kukhululukila ena? Ambili a ife cimativuta, makamaka ngati munthuyo wakamba mawu amene atikhumudwitsa kapena waticita zinthu zimene zatikhumudwitsa kwambili. Koma n’zotheka kuiwalako zimene munthuyo anaticita ndi kumukhululukila. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitikila mlongo Denise,a amene anakhululukila munthu winawake m’njila yapadela kwambili. Mu 2017, Denise ndi banja lake anapita kukaona malo omwe anangotsegulidwa kumene ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova. Pobwelela kunyumba, dalaivala wina analephela kuwongolela galimoto yake moti anagunda galimoto yawo. Denise anakomoka pangoziyo. Atatsitsimuka, anazindikila kuti ana ake anavulala kwambili, ndiponso kuti mwamuna wake, Brian, anafa pangoziyo. Pokumbukila zonsezi, Denise anati: “Cinandiwawa kwambili ndipo n’nasowa cocita.” Kenako anamva kuti pamene ngoziyo inali kucitika, dalaivalayo sanali woledzela ndipo sanali kugwilitsa nchito foni poyendetsa galimoto. Koma inali ngozi cabe. Conco, mlongoyu anapemphela kwa Yehova kuti amupatse mtendele wamumtima womuthandiza kulamulila mkwiyo umene anali nawo.

2 Dalaivalayo anaimbidwa mlandu wopha munthu mwangozi, umene cilango cake ndi kukapika ndende. Khoti inauza Denise kuti cigamulo ca mlanduwo cidzadalila zimene iye adzafotokoza pa nkhaniyo. Denise anakamba kuti: “Zimene anandipempha kucitazi zinali ngati munthu watenga mcele n’kuuthila pazilonda zanga. N’namva conco cifukwa n’nafunikila kukafotokoza zinthu zimene zikanandikumbutsa zimene zinacitika patsiku la ngozi.” Patapita milungu yocepa, Denise anapita kukhoti kuti akafotokoze mmene anali kuionela nkhaniyo, ndipo ngakhale dalaivala uja analipo. Kodi Denise anakamba ciyani? Iye anapempha woweluza kuti acitile cifundo munthuyo.b Denise atamaliza kufotokoza, woweluza anagwetsa misozi. Woweluzayo anakamba kuti, “Pa zaka 25 zimene ndakhala woweluza, sin’naonepo zotelezi. Sin’naonepo banja lolakwilidwa likupempha kuti munthu wolakwa acitilidwe cifundo. Sin’namvepo wolakwilidwa akukamba mawu okomela mtima womulakwila komanso kumukhululukila.”

3. N’ciyani cinathandiza Denise kukhululuka?

3 N’ciyani cinathandiza Denise kukhululuka? Iye anaganizila mmene Yehova amakhululukila. (Mika 7:18) Ngati timayamikiladi kukhululuka kwa Yehova, tidzalimbikitsidwa kukhululukila ena.

4. Kodi Yehova amafuna kuti tizicita ciyani? (Aefeso 4:32)

4 Yehova amafuna kuti tizikhululukila ena ndi mtima wonse monga mmene iye amacitila kwa ife. (Welengani Aefeso 4:32.) Amafuna kuti nthawi zonse tizikhala okonzeka kukhululukila amene atilakwila. (Sal. 86:5; Luka 17:4) M’nkhani ino, tikambilane zinthu zitatu zotithandiza kukhululukila ena pa mlingo wokulilapo.

MUSAPONDELEZE MKWIYO WANU

5. Malinga ndi Miyambo 12:​18, timamva bwanji munthu akatilakwila?

5 Zimakhala zopweteka munthu wina akatikambila mawu oipa kapena akaticita zoipa. Ndipo cimatiwawa kwambili makamaka ngati munthuyo ndi mnzathu kapena wacibale wathu. (Sal. 55:​12-14) Nthawi zina, zingatipweteke kwambili moti tingamve monga munthu watilasa ndi lupanga. (Welengani Miyambo 12:18.) Mwina tingafune kungopondeleza mkwiyo wathu. Kucita zimenezi kungakhale ngati talasidwa ndi mpeni koma n’kuusiya pacilondapo osaucotsa. Mofananamo, sitingayembekezele kuti tidzamvako bwino ngati tangopondeleza mkwiyo wathu munthu wina akatilakwila.

6. Timacita ciyani munthu akatilakwila?

6 Munthu akatilakwila, n’cibadwa kukwiya. Ndipo ngakhale Baibulo limavomeleza mfundoyi. Koma limaticenjeza kuti tisalole mkwiyo kutilamulila. (Sal. 4:4; Aef. 4:26) Cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi zambili timacita zinthu malinga ndi mmene tikumvela. Ndipo kambili, munthu akakwiya sapanga zisankho zanzelu. (Yak. 1:20) Kumbukilani, mkwiyo wanu ena amacita kuuputa. Koma kukhalabe cikwiyile n’cisankho canu.

Mkwiyo wanu ena amacita kuuputa. Koma kukhalabe cikwiyile n’cisankho canu

7. Tingamve bwanji munthu akaticita zoipa?

7 Munthu wina akaticita zoipa, zingatipweteke kwambili. Mwacitsanzo, mlongo Ann ananena kuti: “Ndili mwana, atate anasiya amayi ndi kukwatila wanchito amene anali kundisamalila. N’nadzimva kukhala ndekhandekha. Iwo atakhala ndi ana, n’naona ngati atate aleka kundiika nzelu. N’nakula ndikudziona wosafunika.” Nayenso mlongo Georgette anafotokoza mmene anamvela mwamuna wake atacita cigololo. Iye anati: “Tinali mabwenzi kucokela paubwana wathu. Ndipo tinali kucitila limodzi upainiya. Zimenezi zinandipweteka mtima kwambili.” Ndipo mlongo Naomi anati: “Sin’nayembekezele kuti mwamuna wanga angacite zinthu zondikhumudwitsa. Conco atandiuza kuti wakhala akuonelela zamalisece mseli, n’namva kuti wandicita zacinyengo.”

8. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kukhululukila ena? (b) Timapindula bwanji tikakhululukila ena? (Onani bokosi lakuti “Zimene Tingacite Munthu Wina Akatikhumudwitsa.”)

8 Sitingakwanitse kuletsa anthu kutinena kapena kuticita zoipa. Koma tingakwanitse kudziletsa pa zimene tingacitepo. Kambili, cocitapo cabwino koposa ndi kuwakhululukila. Cifukwa ciyani? Cifukwa timakonda Yehova ndipo iye amafuna kuti tizikhululukila ena. Ngati tikhala cikwiyile osakhululuka, tingacite zinthu mopanda nzelu ndipo mkwiyowo ungawononge ngakhale thanzi lathu. (Miy. 14:​17, 29, 30) Onani citsanzo ca mlongo Christine. Iye anati: “Ndikakwiya ndimangokhala wamsunamo. Ndimadya zosapatsa thanzi, ndipo tulo tumandisowa usiku. Ndimakhala ndi mtima wapacala, zomwe zimatsamwitsa ukwati wanga, komanso ubale wanga ndi anthu ena.”

Zimene Tingacite Munthu Wina Akatikhumudwitsa

M’pofunika kukumbukila kuti tikakhululukila munthu si ndiye kuti ndife okondwa ndi zimene akucita ayi, kapena kuti tikumulola kupitiliza kucita zopanda cilungamozo ayinso. Koma zimaonetsa kuti sitinamusungile cakukhosi komanso mkwiyo. Mwa kutelo, sitidzakhala muukapolo wovutika ndi zimene anaticitazo. Kusasunga cakukhosi kumatipindulilanso, cifukwa timaiwala zimene munthuyo anaticita. Ngakhale pamene takhululuka, sitiyenela kuiwala kuti munthuyo akali ndi mlandu kwa Yehova pa zimene anacitazo. Conco, kukhululukila ena ndi kusasunga cakukhosi ndi njila ina imene timatsatilila malangizo ouzilidwa a wamasalimo akuti: “Umutulile Yehova nkhawa zako.” (Sal. 55:22) Timasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, tili ndi cidalilo cakuti iye adzamuweluza wotilakwilayo. Ndipo Yehova amaweluza bwino kwambili kuposa mmene tingacitile. Iye adzaweluza mwacilungamo kuposa mmene tikanacitila patokha.

9. N’cifukwa ciyani sitiyenela kusungila ena cakukhosi?

9 Ngakhale kuti wotilakwilayo sanapepese, tingacepetsebe ululu umene tikumvela. Motani? Mlongo Georgette amene tam’chula kale, anakamba kuti: “Zinanditengela nthawi, koma n’nasiya kumusungila cakukhosi mwamuna wanga wakale. Zotsatila zake n’zakuti n’nakhala ndi mtendele wamumtima.” Kupewa kusunga cakukhosi kudzatithandiza kusacita zinthu mokwiya ndi anthu ena. Tikakhululukila munthu, nafenso timapindula cifukwa timaleka kuganizila nkhaniyo ndi kuyambanso kusangalala ndi umoyo. (Miy. 11:17) Koma kodi muyenela kucita ciyani ngati zikali kukuvutani kukhululuka?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUTHETSA MKWIYO

10. N’cifukwa ciyani tiyenela kudzipatsa nthawi kuti tithetse mkwiyo wathu? (Onaninso zithunzi.)

10 N’ciyani cingakuthandizeni kuthetsa mkwiyo? Njila imodzi n’kudzipatsa nthawi. Munthu amene wavulala kwambili amafunika nthawi kuti acile pambuyo polandila cithandizo ca mankhwala. Mofananamo, kuti tikhululukiledi munthu mocokela pansi pa mtima, pangatengeko nthawi kuti mtima wathu ukhale pansi.​—Mlal. 3:3; 1 Pet. 1:22.

Zithunzi: M’bale amene anavulala akucila patapita nthawi. 1. Azacipatala akumuika mu ambulansi. 2. Akumuthandiza kuti ayambilenso kuyenda. 3. Iye tsopano wakwanitsa kuyamba kuyenda popanda kum’thandiza.

Tikavulala timafunika cisamalilo cabwino ndipo pamatenga nthawi kuti ticile. Ndi mmenenso zimakhalila munthu wina akatikhumudwitsa (Onani ndime 10)


11. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji kuti tikhululukile ena?

11 Pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kukhululukila ena.c Mlongo Ann amene tam’chula uja, anafotokoza mmene pemphelo linamuthandizila. Iye anati: “N’napempha Yehova kuti akhululukile aliyense wam’banja mwathu pa zonse zosayenela zimene tinakamba ndi kucita. Kenako, n’nalembela atate ndi akazi awo atsopano kalata yowauza kuti ndawakhululukila.” Mlongo Ann sanabise kuti kucita zimenezi kunali kovuta. Koma anakambanso kuti: “Ndikhulupilila kuti mmene ndawakhululukila atate ndi akazi awo potengela citsanzo ca Yehova, adzaphunzila zambili za iye.”

12. N’cifukwa ciyani tiyenela kudalila Yehova m’malo motsatila mtima wathu? (Miyambo 3:​5, 6)

12 Dalilani Yehova osati mtima wanu. (Welengani Miyambo 3:​5, 6.) Nthawi zonse Yehova amadziwa zimene zili zabwino kwa ife. (Yes. 55:​8, 9) Ndipo sangatiuze kucita zinthu zimene zingativulaze. Conco, iye akatiuza kuti tizikhululuka, tisakaikile kuti kucita zimenezo kudzatipindulila. (Sal. 40:4; Yes. 48:​17, 18) Koma ngati tidalila mtima wathu, sitingakwanitse kukhululukila ena. (Miy. 14:12; Yer. 17:9) Mlongo Naomi amene tam’chula kuciyambi anati: “Poyamba n’nali kuona kuti sindiyenela kum’khululukila mwamuna wanga cifukwa coonelela zamalisece. N’nali kuopa kuti ndikamukhululukila angadzandikhumudwitsenso, kapena angaone ngati zimene anacitazo si vuto lalikulu. N’nali kuona kuti ngakhale Yehova akumvetsa kukhumudwa kwanga. Koma n’nazindikila kuti, ngakhale kuti Yehova akumvetsa mmene ndikumvela, sizitanthauza kuti akugwilizana nazo. Adziwa mmene ndikumvela komanso kuti zingatenge nthawi kuti mkwiyo wanga uthe. Ngakhale n’telo, amafunanso kuti ndikhale wokhululuka.”d

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUZIONA ZINTHU MOYENELA

13. Malinga ndi Aroma 12:​18-21, kodi tiyenela kucita ciyani?

13 Tikakhululukila munthu amene anatilakwila kwambili, tizipewa kukamba za nkhaniyo. Koma si zokhazo. Ngati anatilakwilayo ndi m’bale kapena mlongo, tiziyesetsa kubwezeletsa mtendele. (Mat. 5:​23, 24) M’malo mokhala okwiya tiyenela kuonetsa cifundo. Ndipo m’malo mosunga cakukhosi tiyenela kukhululuka. (Welengani Aroma 12:​18-21; 1 Pet. 3:9) N’ciyani cingatithandize kucita zimenezi?

14. Tiyenela kuyesetsa kucita ciyani? Ndipo n’cifukwa ciyani?

14 Tiziyesetsa kuona munthu amene anatikhumudwitsayo mmene Yehova amamuonela. Yehova amasankha kuyang’ana zabwino mwa anthu. (2 Mbiri 16:9; Sal. 130:3) Tikamawaganizila zabwino anthu ena, tidzaonamo zabwino mwa iwo. Koma tikamawaganizila zoipa, tidzaonamo zoipa. Tikamayang’ana zabwino mwa ena, sitidzavutika kuwakhululukila. Mwacitsanzo, m’bale wina dzina lake Jarrod anakamba kuti, “Cimakhala cosavuta kukhululukila m’bale ndikayelekezela kucepa kwa zimene wandilakwila ndi kuculuka kwa zabwino zimene ndimakonda mwa iye.”

15. N’cifukwa ciyani n’zothandiza kuuza munthu kuti mwamukhululukila?

15 Cina cofunika kucita ndi kumuuza munthuyo kuti mwamukhululukila. N’cifukwa ciyani kucita zimenezi n’kofunika? Onani zimene mlongo Naomi amene tam’chula uja anakamba. Anati: “Mwamuna wanga anandifunsa kuti, ‘Kodi wandikhululukila?’ N’tatsegula pakamwa kuti ndimuuze kuti, ‘Ndakukhululukilani,’ n’natsamwa. N’nazindikila kuti n’nali ndisanamukhululukile kucokela pansi pa mtima. M’kupita kwa nthawi n’nakwanitsa kumuuza mawu ogwila mtima amenewa akuti, ‘Ndakukhululukilani.’ Mawu amenewa anamukhazika mtima pansi mwamuna wanga moti anagwetsa misozi. Pambuyo pake n’nakhala ndi mtendele wamumtima. Kucokela nthawi imeneyo n’nayambanso kumukhulupilila, ndipo tsopano ndife mabwenzi apamtima monga kale.”

16. Mwaphunzila ciyani pa nkhani yokhululukila ena?

16 Yehova amafuna kuti tizikhululukila ena. (Akol. 3:13) Ngakhale n’telo, zingakhalebe zotivuta kucita zimenezo. Koma tingakwanitse kukhululuka ngati sitikupondeleza mkwiyo wathu, komanso ngati tiyesetsa kuuthetsa mkwiyowo. Kenako, tingasinthe mmene tikuonela zinthu kuti tikhale ndi kapenyedwe kabwino.​—Onani danga lakuti “Masitepe Atatu Amene Angakuthandizeni Kukhululuka.”

Masitepe Atatu Amene Angakuthandizeni Kukhululuka

Mlongo wokhumudwa akuyang’ana pawindo.

MUSAPONDELEZE MKWIYO WANU

  • Simungayembekezele kuti mungaiwale nkhaniyo ngati mukupondeleza mkwiyo wanu.

Mlongo m’modzimodziyo akuuza Yehova vuto lake m’pemphelo.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUTHETSE MKWIYO

  • Dzipatseni nthawi.

  • Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kusasunga cakukhosi.

  • Muzidalila Yehova, m’malo motsatila mtima wanu.

Tsopano mlongoyo ali pamodzi ndi mwamuna wake, ndipo ndi okondwela.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUZIONA ZINTHU MOYENELA

  • Muziona munthuyo mmene Yehova amamuonela.

  • Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukhululuka.

  • Muuzeni munthuyo kuti mwamukhululukila.

MUZIGANIZILA MAPINDU OBWELA CIFUKWA COKHULULUKILA ENA

17. Timapindula bwanji tikakhululukila ena?

17 Tili ndi zifukwa zambili zokhululukila ena. Tiyeni tioneko zocepa cabe. Coyamba, timatengela Atate wathu wacifundo Yehova, ndipo timam’kondweletsa tikatelo. (Luka 6:36) Caciwili, timaonetsa kuti timayamikiladi kuti Yehova amatikhululukila. (Mat. 6:12) Cacitatu, timakhala ndi thanzi labwino, ndipo timakhalanso paubwenzi wolimba ndi ena.

18-19. Kodi kukhululuka kwathu kungakhale ndi zotulukapo zotani?

18 Tikakhululukila ena, tingalandile madalitso amene sitinali kuwayembekezela. Mwacitsanzo, onani zinacitikila mlongo Denise amene tamuchula kuciyambi. Ngakhale kuti Denise sanali kudziwa, pa nthawi imene mlanduwo unali ku khoti, dalaivala uja anali kuganiza kuti akadziphe mlandu wake ukagamulidwa. Koma anakhudzika mtima kwambili cifukwa cakuti Denise anam’khululukila. Conco, anayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova.

19 Nthawi zina tingaone kuti kukhululukila ena n’cimodzi mwa zisankho zovuta kwambili. Koma cingakhalenso cimodzi mwa zisankho zimene zingatipindulile kwambili. (Mat. 5:7) Conco, tiyeni ticite zonse zotheka kuti tizitengela citsanzo ca Yehova ca kukhululuka.

MUNTHU WINA AKAKULAKWILANI, . . .

  • n’cifukwa ciyani simuyenela kupondeleza mkwiyo wanu?

  • n’ciyani cingakuthandizeni kuthetsa mkwiyo?

  • mungacite ciyani kuti muziona zinthu moyenela?

NYIMBO 125 ‘Acifundo ni Acimwemwe!’

a Maina ena asinthidwa.

b Pa nkhani ngati zimenezi, Mkhristu aliyense ayenela kusankha yekha mmene adzasamalila nkhaniyo.

c Onani mavidiyo a nyimbo zopekedwa koyamba awa pa jw.org, “Tizikhululukilana,” “Kukhululuka na Mtima Wonse,” komanso yakuti “Tikhalenso Paubwenzi.”

d Kuonelela zamalisece n’kulakwa. Ndipo ngati akuonelelayo ndi wokwatila, zimapweteka mnzake. Koma izi sizipatsa mnzakeyo ufulu wa m’Malemba wothetsela ukwati.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani