NYIMBO 125
‘Acifundo ni Acimwemwe!’
Yopulinta
1. Yehova ni wacifundo,
Ndipo ni wokoma mtima.
Iye amasamalila
Zonse zimene tifuna.
Ocimwa ngati alapa,
Amaŵakhululukila.
Cifukwa iye adziŵa
Kuti ‘se ndise ofooka.
2. Tikakhala na cifundo,
M’lungu adzatidalitsa.
Adzatikhululukila
Ise pamene tilakwa.
Yesu anatiphunzitsa
Kufunika kwa cifundo.
Tidzakhala na mtendele,
Ngati timakhululuka.
3. Pamene tipatsa ena
Mphatso zathu za cifundo.
Ise tisadzitamande,
Tikhale odzicepetsa.
Anthu onse acifundo,
Amakhala acimwemwe.
Yehova amaŵakonda,
Iye amaŵadalitsa.
(Onaninso Mat. 6:2-4, 12-14.)