LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 1 tsa. 15
  • N’zotheka Kupeza Nzelu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’zotheka Kupeza Nzelu
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mulungu Akukupemphani Kuti Mupindule na Nzelu Zake
  • N’zotheka Imwe Kupeza Nzelu Zocokela kwa Mulungu
  • Kodi Tingamumvetsele Bwanji Mulungu?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Kodi Inu Mudzatsatila Malangizo a Ndani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • Baibulo Ni Buku Yocokela Kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Uthenga Wabwino Ni Wocokeladi kwa Mulungu?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 1 tsa. 15

N’zotheka Kupeza Nzelu

“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Pa vesiyi, mawu akuti “anauzilidwa” amatanthauza kuti Mulungu Wamphamvuzonse anaika maganizo ake m’mitima ya anthu amene analemba Baibo.

MFUNDO ZINA ZOKHUDZA BAIBO

  • Zigawo za buku.

    66

    Ciŵelengelo ca mabuku kapena zigawo zimene zimapanga Baibo.

  • Dzanja likulemba pamene kuwala kocokela kumwamba kukuunika.

    40

    Ciŵelengelo ca amuna amene Mulungu anawaseŵenzetsa polemba Baibo.

  • Galasi yopimila nthawi.

    1513 B.C.E.

    Caka cimene Baibo inayamba kulembedwa—zaka zoposa 3,500 zapitazo!

  • Zilembo za m’zinenelo zosiyana-siyana.

    Kuposa pa 3,000

    Ciŵelengelo ca zinenelo zimene Baibo kapena mbali yake imapezeka.

Mulungu Akukupemphani Kuti Mupindule na Nzelu Zake

“Ine Yehova . . . ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, . . . ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo. Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo cilungamo canu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”—YESAYA 48:17, 18.

Mawu a pa vesiyi atengeni monga ciitanilo canu cocokela kwa Mulungu. Iye amafuna kuti mukhale na mtendele wa maganizo komanso cimwemwe cokhalitsa, ndipo angakuthandizeni kuzipeza.

N’zotheka Imwe Kupeza Nzelu Zocokela kwa Mulungu

“M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenela ulalikidwe.”—MALIKO 13:10.

“Uthenga wabwino” uphatikizapo malonjezo a Yehova akuti adzathetsa kuvutika, adzapanga dziko kukhala paradaiso, komanso adzaukitsa akufa. Mboni za Yehova zimalalikila uthenga wa m’Baibo umenewu padziko lonse.

N’natseguka Mutu N’taŵelenga Baibo

“Kucokela nili mwana, n’nali kusokonezeka kuti kodi Mlengi n’ndani. N’nali kudzifunsa kuti, ‘Zingatheke bwanji mtundu uliwonse kukhala na mulungu wake kapena mlengi wake?’ Conco, nimakonda zimene Baibo imakamba pa Aroma 3:29. Lembali limaonetsa kuti Mulungu woona ni Mulungu wa anthu a mitundu yonse. Alinso na dzina lake-lake lakuti Yehova, ndipo amafuna kuti tikhale mabwenzi ake.”—Rakesh.

Rakesh.
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani