LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 3 masa. 14-15
  • Cifukwa Cake Kudziŵa Ngati Mlengi Aliko N’kofunika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cifukwa Cake Kudziŵa Ngati Mlengi Aliko N’kofunika
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mudzakhala na umoyo wacimwemwe
  • Mudzapeza malangizo othandiza pa umoyo
  • Mudzapeza mayankho pa mafunso anu
  • Mudzakhala na ciyembekezo ca tsogolo labwino
  • Kodi Ziphunzitso Zoona Ponena za Mulungu ndi Ziti?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • Kodi Mulungu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Galamuka!—2021
g21 na. 3 masa. 14-15
Anthu angapo amene ni mabwenzi akuyang’ana mwacidwi mbalame zimene zili mumtengo.

Cifukwa Cake Kudziŵa Ngati Mlengi Aliko N’kofunika

N’cifukwa ciani kudziŵa ngati Mlengi aliko n’kofunika? Cifukwa ngati mwakhutila na umboni wakuti kuli Mulungu wamphamvuzonse, mungafune kupenda umboni wakuti Baibo ni youzilidwa na iye. Ndipo mukakhulupilila zimene Baibo imakamba, mudzapindula m’njila izi:

Mudzakhala na umoyo wacimwemwe

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “[Mulungu] anakupatsani mvula kucokela kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambili. Anadzaza mitima yanu ndi cakudya komanso cimwemwe.”—Machitidwe 14:17.

TANTHAUZO LAKE: Ciliconse ca m’cilengedwe cimene mumasangalala naco ni mphatso yocokela kwa Mlengi. Mudzayamikila kwambili mphatso zimenezi mukadziŵa kuti amene anakupatsani amakukondani kwambili.

Mudzapeza malangizo othandiza pa umoyo

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “Ukacita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njila yonse ya zinthu zabwino.”—Miyambo 2:9.

TANTHAUZO LAKE: Popeza Mulungu ni Mlengi wathu, amadziŵa zimene timafunikila kuti tikhale acimwemwe. Mukamaŵelenga Baibo, mudzapeza mfundo zambili zimene zingakuthandizeni pa umoyo wanu.

Mudzapeza mayankho pa mafunso anu

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “Udzamudziwadi Mulungu.”—Miyambo 2:5.

TANTHAUZO LAKE: Mukadziŵa kuti Mlengi alipo, mudzapeza mayankho pa mafunso ofunika kwambili monga akuti: Kodi colinga ca moyo n’ciani? N’cifukwa ciani padzikoli pali mavuto ambili? Kodi cimacitika n’ciani munthu akamwalila? Mungapeze mayankho okhutilitsa pa mafunso amenewa m’Baibo.

Mudzakhala na ciyembekezo ca tsogolo labwino

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizila zokupatsani mtendele osati masoka, kuti mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watelo Yehova.’”—Yeremiya 29:11.

Onelelani vidiyo ya pa jw.org yakuti Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona?, komanso yakuti Ndani Analemba Baibulo? Mungapeze mavidiyo amenewa mwa kulemba mawu akuti “Baibulo zoona,” kapena akuti “wolemba Baibulo” m’danga lofufuzila.

TANTHAUZO LAKE: Mulungu analonjeza kuti m’tsogolo adzathetsa zoipa, mavuto, ngakhale imfa. Mukakhulupilila malonjezo a Mulungu, mudzakhala na ciyembekezo ca tsogolo labwino cimene cidzakuthandizani kukhalabe wolimba mtima pamene mwakumana na mavuto.

Mmene ena apindulila cifukwa cokhulupilila kuti kuli Mlengi

Cyndi.

“Nthawi zonse nimacita cidwi nikaganizila mmene Mulungu amatithandizila m’njila zosiyanasiyana pa umoyo wathu. Amatithandiza kudziŵa zoyenela kuika patsogolo mu umoyo wathu, mocitila tikasemphana maganizo na ena, komanso mmene tingakhalile mabwenzi ake.”—Cyndi, wa ku America.

Elise.

“Kukhulupilila kuti kuli Mlengi kumanithandiza kukhala na umoyo wacimwemwe komanso waphindu. Sinisoŵa cocita cifukwa pali zinthu zambili zokondweletsa zimene niyenela kuphunzila ponena za iye, cilengedwe cake, komanso Mawu ake.”—Elise, wa ku France.

Peter.

“Kuseŵenzetsa malangizo a Mlengi opezeka m’Baibo kumanipangitsa kukhala wacimwemwe. Kumanithandiza kuti nisamakonde kupeza ena zifukwa, nizikhala woganizila ena komanso wokhutila. Kwanithandizanso kukhala tate wabwino.”—Peter, wa ku Netherlands.

Liz.

“Kale, n’nali na umoyo wongokhalila kudya, kugona, na kuyesetsa mwamphamvu kuti nikafike kunchito panthawi yake. N’nali kukhala wopanikizika kwambili. Koma tsopano nimaona kuti moyo ni mphatso yabwino kwambili, imene niyenela kusangalala nayo na kuikonda.”—Liz, wa ku Estonia.

Adrien.

“Ine nimakonda kukhala na nkhawa kwambili. Koma kudziŵa kuti kuipa, kupanda cilungamo, na mavuto zidzatha kumanithandiza kupilila.” —Adrien, wa ku France.

Onani mmene Baibo imayankhila mafunso ofunika kwambili pa umoyo. Onelelani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?—Yathunthu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani