LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 1 nkhani 8-17
  • Kodi Ziphunzitso Zoona Ponena za Mulungu ndi Ziti?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Ziphunzitso Zoona Ponena za Mulungu ndi Ziti?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI MULUNGU SATISAMALILA, NDIPO KODI NDI WOUMA MTIMA?
  • KODI MULUNGU AMAMVA BWANJI PAMENE AONA KUPANDA CILUNGAMO KUMENE KUMACITIKILA ANTHU?
  • MULUNGU AMAFUNA KUTI MUM’DZIŴE KUTI IYE NDANI
  • KODI N’ZOTHEKA KUTI INU MUMUYANDIKILE YEHOVA?
  • Kodi Mulungu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Coonadi Ponena za Mulungu na Khristu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho A zoona pa Mafunso Aya?
    Kodi Mukufuna kudziwa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya?
  • Kodi Mulungu Ndani?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
Onaninso Zina
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 1 nkhani 8-17

NKHANI 1

Kodi Ziphunzitso Zoona Ponena za Mulungu ndi Ziti?

  • Kodi m’ceni-ceni Mulungu amasamala za inu?

  • Kodi Mulungu ali ndi makhalidwe abwanji? Kodi ali ndi dzina?

  • Kodi n’zotheka kuti timuyandikile Mulungu?

Young girl looking up and asking a question

1, 2. N’cifukwa ciani nthawi zambili n’cinthu cabwino kufunsa mafunso?

KODI mumaona mmene ana amafunsila mafunso? Ana ambili amayamba kufunsa mafunso akangoyamba cabe kukamba. Amakuyan’gana ndi maso acidwi ndi kufunsa mafunso monga akuti: Dzuŵa limapita kuti usiku? Nanga nyenyezi ziliko zingati kumwamba? Kodi mbalame zija ziyenda kuti? Ungayese kufotokoza bwino, koma nthawi zambili zimakhala zovuta. Ngakhale ukapeleka yankho lomveka, m’pamene mwana amafunsanso funso lina.

2 Si ana cabe amene amafunsa mafunso. Ngakhale ife pamene tipitiliza kukula, timafunsabe mafunso. Timafunsa kuti tidziŵe njila, kuti tidziŵe ngozi zofunika kupewa, kapena kungofuna kudziŵa cabe pa zinthu zimene ticita nazo cidwi. Koma cioneka kuti anthu ambili amaleka kufunsa mafunso, maka-maka mafunso ofunika kwambili. Ndipo mwacionekele, amalekelatu kufuna-funa mayankho.

3. N’cifukwa ciani anthu ambili amaleka kufuna-funa mayankho a mafunso ofunika kwambili?

3 Ganizilani za mafunso amene ali papeji 6, kapena amene ali kuciyambi kwa nkhani ino. Amenewa ndi ena mwa mafunso ofunika amene mungafunse. Koma anthu ambili amaleka kufuna-funa mayankho ake. N’cifukwa ciani? Kodi Baibo ili ndi mayankho? Anthu ena amaona kuti mayankho a m’Baibo ndi ovuta kuwamvetsetsa. Ena amaopa kuti kufunsa mafunso kungawacititse manyazi. Ndipo ena amaganiza kuti mafunso amenewo ndi bwino kungowasiila abusa acipembedzo. Nanga inu muganiza bwanji?

4, 5. Kodi ena mwa mafunso ofunika kwambili amene tingafunse paumoyo ndi ati? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kufuna-funa mayankho ake?

4 Mwacionekele, inu mumafunitsitsa kuti mudziŵe mayankho pa mafunso ofunika kwambili onena za umoyo. Mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi colinga ca moyo n’ciani? Kodi cingakhale cakuti tizibadwa, kukalamba ndi kufa basi? Kodi Mulungu ali ndi makhalidwe abwanji?’ N’cinthu canzelu kufunsa mafunso amenewa, ndipo n’kofunika kuti mupitilize kuyesa-yesa kupeza mayankho eni-eni ndi okhutilitsa. Mphunzitsi wochuka, Yesu Kristu, anakamba kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufuna-funa, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulilani.”—Mateyu 7:7.

5 Ngati mupitiliza “kufuna-funa” mayankho a mafunso ofunika kwambili, kufufuza kwanu kudzakupindulitsani. (Miyambo 2:1-5) Mosasamala kanthu zimene anthu ena akuuzani, mayankho alipo, ndipo mungawapeze m’Baibo. Mayankho amenewo si ovuta kuwamvetsetsa. Ndipo amapatsa ciyembekezo ndi cimwemwe. Komanso angakuthandizeni kuti mukhale ndi umoyo wabwino. Koma coyamba, tiyeni tione funso limene lavutitsa anthu ambili.

KODI MULUNGU SATISAMALILA, NDIPO KODI NDI WOUMA MTIMA?

6. N’cifukwa ciani anthu ambili amaganiza kuti Mulungu sasamala za mavuto amene timakumana nao?

6 Anthu ambili amaganiza kuti n’zoona Mulungu satisamalila ndipo ndi wouma mtima. Iwo amati ‘kukanakhala kuti Mulungu anali kutisamalila, kodi dziko likanakhala loipa mmene lilili?’ Tikayang’ana m’dziko timaona nkhondo zambili, zidani, ndi mavuto osaneneka. Ndipo ife anthu, timadwala, kuvutika, ndi kufeledwa. Conco, anthu ambili amakamba kuti, ‘Kukanakhala kuti Mulungu amasamala za ife ndi mavuto athu, kodi akanalola kuti mavuto amenewa azicitika?’

7. (a) Kodi abusa amapangitsa bwanji anthu kuganiza kuti Mulungu ndi wouma mtima? (b) Kodi Baibo imati ciani pa mayeselo amene timakumana nao?

7 Cacisoni kwambili n’cakuti, abusa amacititsa anthu kuganiza kuti Mulungu ndi wouma mtima. Amacita bwanji zimenezi? Pakacitika cinthu coipa, amakamba kuti n’cifunilo ca Mulungu. M’ceni-ceni, abusa amenewo amapatsa Mulungu mlandu pa zinthu zoipa zimene zimacitika. Kodi cimeneco n’ciphunzitso coona ponena za Mulungu? Nanga Baibo imaphunzitsa ziti m’ceni-ceni? Lemba la Yakobo 1:13 limayankha kuti: “Munthu akakhala pa mayeselo asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” Conco, Mulungu sindiye amacititsa mavuto amene timaona m’dziko. (Yobu 34:10-12) Iye amangololela cabe zinthu zoipa kuti zicitike. Koma pali kusiyana kwakukulu pakati pa kulolela cinthu kucitika ndi kucipangitsa kuti cicitike.

8, 9. (a) Kodi pali kusiyana kwanji pakati pa kulolela coipa kucitika ndi kucipangitsa kucitika? (b) N’cifukwa ciani kungakhale kulakwa kuimba Mulungu mlandu wakulolela anthu kuyenda m’njila zoipa?

8 Mwacitsanzo, ganizilani za tate wacikondi ndi wanzelu amene ali ndi mwana wamkulu msinkhu pakhomo. Tinene kuti mwana uja wapanduka ndi kuganiza zocoka pakhomo, ndipo tate wake amulola kuti acoke. Kumene mwanayo wapita ayamba kucita zinthu zoipa, cakuti agwela m’mavuto aakulu. Kodi tingakambe kuti tate uja ndiye wapangitsa kuti mwana wake agwele m’mavuto? Iyai. (Luka 15:11-13) N’cimodzi-modzi ndi Mulungu. Iye saletsa anthu akasankha okha kuyenda m’njila yoipa. Koma sindiye amapangitsa mavuto amene anthuwo amakumana nao. Conco, kungakhale kulakwa kupatsa Mulungu mlandu pa mavuto onse amene amacitikila anthu.

9 Mulungu ali ndi zifukwa zake zomveka zimene walekela anthu kuyenda m’njila zoipa zimene asankha okha. Pokhala kuti ndi Mlengi wathu wanzelu ndi wamphamvuyonse, kweni-kweni iye sakanafunikila kutifotokozela zifukwa zake. Koma mwa cikondi cake cabe, watifotokozela zifukwazo. Mudzadziŵa zambili pa zifukwa zimenezo mu Nkhani 11. Koma dziŵani kuti Mulungu sindiye amacititsa mavuto amene timakumana nao. M’malo mwake, iye ndi amene angatithandize panthawi ya mavuto!—Yesaya 33:2.

10. N’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila kuti Mulungu adzacotsapo zoipa zonse?

10 Cinanso n’cakuti Mulungu ndi woyela. (Yesaya 6:3) Zimenezi zimatanthauza kuti kwa iye kulibe cidetso ciliconse, ndipo ndi waukhondo. Alibe coipa ciliconse. Ndiye cifukwa cake tiyenela kum’khulupilila ndi mtima wonse. Cikhulupililo cimeneci sitingakhale naco mwa munthu, cifukwa nthawi zina amakhala wosaona mtima. Ngakhale munthu waudindo ndi woona mtima kwambili, nthawi zambili samakwanitsa kukonza zinthu zimene anthu oipa amaononga. Koma Mulungu ndi wamphamvuyonse. Adzacotsapo mavuto onse amene anthu oipa amacititsa padziko lapansi. Pamene Mulungu adzacitapo kanthu, mavuto onse adzathelatu kwamuyaya!—Salimo 37:9-11.

KODI MULUNGU AMAMVA BWANJI PAMENE AONA KUPANDA CILUNGAMO KUMENE KUMACITIKILA ANTHU?

11. (a) Kodi Mulungu amamva bwanji pamene aona kupanda cilungamo? (b) Nanga muganiza amamva bwanji pamene inu muvutika?

11 Kodi Mulungu amamva bwanji pa zimene zimacitika m’dziko ndi paumoyo wanu? Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu “amakonda cilungamo.” (Salimo 37:28) Conco, ponena za cabwino ndi coipa sinkhani yaing’ono kwa Mulungu. Ndiye cifukwa cake iye amadana ndi kupanda cilungamo kwa mtundu uliwonse. Baibo imakamba kuti Mulungu “zinam’pweteka kwambili mumtima” pamene dziko lapansi linadzala ndi zoipa zambili m’nthawi zakale. (Genesis 6:5, 6) Mulungu sanasinthe. (Malaki 3:6) Iye akali kuipidwa ndi mavuto amene amacitika padziko. Ndipo cimamuŵaŵa kuona anthu akuvutika. Baibo imakamba kuti, ‘Iye amasamala za inu’.—1 Petulo 5:7, Buku Lopatulika.

God’s creations: mountains, lake, fish, birds, and trees

Baibo imaphunzitsa kuti Yehova ndi Mlengi wacikondi wa cilengedwe conse

12, 13. (a) N’cifukwa ciani ife anthu tili ndi makhalidwe abwino monga cikondi? Ndipo cikondi cimatipangitsa kumva bwanji tikaona kupanda cilungamo kumene kumacitika padziko? (b) Kodi mungatsimikize bwanji kuti Mulungu adzacitapo kanthu pa mavuto amene ali padziko lapansi?

12 Kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu amadana ndi mavuto? Tiyeni tione umboni wina. Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu anapanga munthu m’cifanizilo cake. (Genesis 1:26) Conco, ife tili ndi makhalidwe abwino cifukwa cakuti Mulungu ali ndi makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, kodi zimakuvutitsani maganizo mukaona anthu akuvutika? Ngati mumamva kuipa poona kupanda cilungamo kumeneko, dziŵani kuti Mulungu ndi amene amamva kuipa kwambili kuposa mmene inu mumamvelela.

13 Cimodzi mwa zinthu zabwino kwambili kwa ife anthu n’cakuti timatha kukonda anthu ena. Cimenecinso cimaonetsa mmene Mulungu alili. Baibo imaphunzitsa kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Timakonda anthu ena cifukwa cakuti Mulungu amakonda anthu ena. Kodi cikondi sicingakupangitseni kucotsapo mavuto ndi kupanda cilungamo kumene kumacitika m’dziko? N’zosacita kufunsa! Conco, musakaikile ngakhale pang’ono kuti Mulungu adzacotsapo mavuto ndi kupanda cilungamo konse. Malonjezo amene ali pa mapeji 4 ndi 5 a m’buku lino si maloto, kapena kuti zinthu zoganizila cabe iyai. Malonjezo a Mulungu adzacitikadi! Kuti mukhulupilile malonjezo amenewo, mufunikila kudziŵa zambili za Mulungu amene anawalonjeza.

MULUNGU AMAFUNA KUTI MUM’DZIŴE KUTI IYE NDANI

Two women introducing themselves to each other

Ngati mufuna kuti munthu wina akudziŵeni, kodi simumamuuza dzina lanu? Mulungu amatidziŵitsa dzina lake m’Baibo

14. Kodi dzina la Mulungu ndani? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuligwilitsila nchito?

14 Ngati mufuna kuti munthu wina akudziŵeni, kodi mumacita ciani? Kodi simumamuuza dzina lanu? Nanga Mulungu ali ndi dzina? Zipembedzo zambili zimakamba kuti dzina lake ndi “Mulungu” kapena “Ambuye.” Koma maina amenewa si maina ake eni-eni. Ndi maina audindo cabe, monga mmene alili maina akuti “mfumu” ndi “pulezidenti.” Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu ali ndi maina audindo ambili. Mau akuti “Mulungu” ndi “Ambuye” ndi ena cabe mwa maina ake audindo. Koma Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu ali ndi dzina leni-leni lakuti Yehova. Lemba la Salimo 83:18 limakamba kuti: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.” Ngati m’Baibo yanu mulibe dzina limeneli, mungaone Zakumapeto pa mapeji 195 mpaka 197 a buku lino kuti mudziŵe cifukwa cake. Coona n’cakuti, dzina la Mulungu limapezeka nthawi zokwana masauzande m’mipukutu yakale kwambili ya Baibo. Conco, Yehova amafuna kuti mudziŵe dzina lake ndi kuti muziligwilitsila nchito. M’njila ina, tingakambe kuti iye amagwilitsila nchito Baibo kuti adzidziŵikitse kwa inu.

15. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza ciani?

15 Mulungu anadzipatsa yekha dzina latanthauzo kwambili. Dzina lake, lakuti Yehova, limatanthauza kuti Mulungu akhoza kukwanilitsa lonjezo lililonse limene wapeleka, ndipo akhozanso kukwanilitsa cifunilo ciliconse cimene ali naco m’maganizo.a Dzina la Mulungu ndi lapadela, limaposa dzina lina lililonse. Ndipo ndi la iye yekha cabe. Yehova ndi wapadela m’njila zambili. M’njila ziti?

16, 17. Kodi maina audindo awa amatiuza ciani za Yehova: (a) “Wamphamvuyonse”? (b)“Mfumu yamuyaya”?(c) “Mlengi”?

16 Taona zimene Salimo 83:18 yanena za Yehova kuti: “Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba.” Ndiponso, ndi Yehova yekha amene amachedwa “Wamphamvuyonse.” Pa Chivumbulutso 15:3 pamati: “Nchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njila zanu ndi zolungama ndi zoona, inu Mfumu yamuyaya.” Dzina laudindo lakuti “Wamphamvuyonse” limationetsa kuti Yehova ndi wamphamvu kwambili kuposa wina aliyense. Mphamvu zake n’zosayelekezeleka; n’zopambana. Ndipo dzina laudindo lakuti “Mfumu yamuyaya” limatikumbutsa kuti Yehova ndi wapadela m’lingalilo linanso. Ndi iye yekha cabe amene wakhalapo kwa nthawi zonse. Salimo 90:2, imakamba kuti: “Inu ndinu Mulungu kuyambila kale-kale mpaka kale-kale.” Mfundo imeneyi ndi yocititsa mantha, si conco?

17 Yehova ndi wapadelanso m’lingalilo lakuti iye yekha ndiye Mlengi. Lemba la Chivumbulutso 4:11 limakamba kuti: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” Ciliconse cimene mungaciganizile—kuyambila ku zolengedwa zosaoneka zauzimu zakumwamba, mpaka ku nyenyezi zimene zimadzaza kumwamba usiku, mpaka ku zipatso zimene zimamela kumitengo, mpaka kukafika ku nsomba zili m’nyanja ndi mitsinje—zonsezi zilipo cifukwa Yehova ndiye anazilenga!

KODI N’ZOTHEKA KUTI INU MUMUYANDIKILE YEHOVA?

18. N’cifukwa ciani anthu ena amaona kuti sangamuyandikile Mulungu? Koma Baibo imaphunzitsa ciani?

18 Anthu ena akaŵelenga za makhalidwe ocititsa mantha a Yehova amakhala ndi maganizo omuopa. Amaona kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambili cakuti sangamuyandikile. Amadziona kuti sali kanthu kwa iye. Koma kodi zimenezi n’zoona? Baibo siiphunzitsa zimenezi. Iyo imakamba kuti Yehova, “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Baibo imatilimbikitsanso kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.

19. (a) Kodi tingayambe bwanji kumuyandikila Mulungu? Ndipo tingapeze madalitso anji? (b) Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene inu mumakonda kwambili?

19 Kodi mungamuyandikile bwanji Mulungu? Coyamba, muyenela kupitiliza kucita zimene muli kucita pano—kuphunzila za Mulungu. Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Zoona, Baibo imaphunzitsa kuti ngati munthu aphunzila za Yehova ndi Yesu adzapeza “moyo wosatha.” Monga mmene taonela kale, “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:16) Yehova alinso ndi makhalidwe ena ambili abwino. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti Yehova ndi “Mulungu wacifundo ndi wacisomo.” (Ekisodo 34:6) Iye ndi ‘wabwino ndi wokonzeka kukhululuka.’ (Salimo 86:5) Mulungu ndi woleza mtima. (2 Petulo 3:9) Ndi wokhulupilika. (Chivumbulutso 15:4) Pamene mupitiliza kuŵelenga Baibo, mudzaona mmene Yehova waonetsela kuti ali ndi makhalidwe abwino amenewa ndi ena ambili.

20-22. (a) Kodi pamene Mulungu sitimuona ndiye kuti sitingamuyandikile? Fotokozani. (b) Kodi anthu ena oona kuti amakudelani nkhawa angayese kucita ciani? Koma kodi inu simuyenela kucita ciani?

20 N’zoona kuti simungamuone Mulungu cifukwa iye ali mzimu wosaoneka. (Yohane 1:18; 4:24; 1 Timoteyo 1:17) Komabe, mwa kuphunzila za iye kupyolela m’Baibo, mungafike pomudziŵa mmene iye alili kweni-kweni. Monga mmene wamasalimo anakambila, mungaone “ubwino wa Yehova.” (Salimo 27:4; Aroma 1:20) Mukapitiliza kuphunzila za Yehova, adzakhala weni-weni kwa inu, ndipo mudzafika pom’konda ndi kumuyandikila kwambili.

A loving father with his child on his shoulders looking at creation

Mmene tate wabwino amakondela ana ake, ndi mmenenso Atate wathu wakumwamba amatikondela kwambili

21 Mudzamvetsetsa cimene Baibo imatiphunzitsila kuti tiyenela kuona Yehova kuti ndi Atate wathu. (Mateyu 6:9) Mulungu sanangotipatsa moyo cabe, koma amafunanso kuti tikhale ndi umoyo wabwino, monga mmene tate aliyense wokonda ana ake amacitila. (Salimo 36:9) Baibo imaphunzitsanso kuti anthu angakhale mabwenzi a Yehova. (Yakobo 2:23) Ganizani cabe—inu kukhala bwenzi la Mlengi wacilengedwe conse!

22 Pamene mupitiliza kuphunzila Baibo, mudzaona kuti anthu ena—oona kuti amakudelani nkhawa—angayese kukuletsani kuphunzila. Iwo angade nkhawa kuti mungasinthe cikhulupililo canu. Koma musalole munthu aliyense kukulepheletsani kukhala paubwenzi wabwino koposa—ubwenzi ndi Mulungu.

23, 24. (a) N’cifukwa ciani simuyenela kucita manyazi kufunsa mafunso pa zimene mumaphunzila? (b) Nanga m’nkhani yotsatila tidzakambitsilana ciani?

23 N’zoona kuti, poyamba padzakhala zinthu zina zimene simungazimvetsetse bwino. Mungacite manyazi kufunsa, koma osacita manyazi iyai. Yesu anakamba kuti cili bwino kukhala wodzicepetsa, ngati mmene mwana wamng’ono amacitila. (Mateyu 18:2-4) Ndipo monga mmene ana timaŵadziŵila, amafunsa mafunso ambili-mbili. Mulungu amafuna kuti mupeze mayankho. Palinso anthu ena amene Baibo imawayamikila cifukwa cokhala ndi mtima wofunitsitsa kuphunzila za Mulungu. Iwo anaŵelenga bwino-bwino m’Malemba kuti atsimikize ngati zimene anali kuphunzila zinali zoona.—Machitidwe 17:11.

24 Njila yabwino koposa yophunzilila za Yehova ndiyo mwa kuphunzila Baibo bwino-bwino. Baibo ndi yosiyana ndi buku lina lililonse. Imasiyana bwanji? Tidzakambitsilana zimenezi mu nkhani yotsatila.

a Kuti mumve zambili za tanthauzo ndi kachulidwe ka dzina la Mulungu, onani Zakumapeto pamapeji 195 mpaka 197.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Mulungu amasamala za inu panokha.—1 Petulo 5:7.

  • Dzina leni-leni la Mulungu ndi Yehova.—Salimo 83:18.

  • Yehova amafuna kuti mumuyandikile.—Yakobo 4:8.

  • Yehova ndi wacikondi, wokoma mtima, ndi wacifundo.—Ekisodo 34:6; 1 Yohane 4:8, 16.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani