LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 15
  • Mkazi Wa Loti Anayang’ana Kumbuyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mkazi Wa Loti Anayang’ana Kumbuyo
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Kumbukilani Mkazi wa Loti
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Thandizani Ena Kulimbana na Nkhawa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kumbukilani Mkazi wa Loti
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 15

Nkhani 15

Mkazi Wa Loti Anayang’ana Kumbuyo

LOTI ndi banja lake anali kukhala pamodzi ndi Abulahamu mu dziko la Kanani. Tsiku lina Abulahamu anauza Loti kuti: ‘Tilibe malo okwanila ziweto zathu zonse. Tiye tipatukane. Ukapita mbali ya uku, ine ndipita mbali ya uku.’

Loti anayang’ana malo onse, ndipo anaona mbali yabwino kwambili imene inali ndi madzi, ndi maudzu abwino a ziweto zake. Malo amenewa anali cigao ca Yorodano. Conco Loti anasamutsila banja ndi ziweto zake ku malo amenewa. Potsilizila pake, anayamba kukhala mu mzinda wa Sodomu.

Anthu a ku Sodomu anali oipa kwambili. Zimenezi zinakhumudwitsa Loti, cifukwa iye anali munthu wabwino. Zinakhumudwitsanso Mulungu. Conco, Mulungu anatumiza angelo aŵili kuti akacenjeze Loti kuti Mulungu adzaononga Sodomu ndi mzinda wa pafupi wa Gomora cifukwa ca zoipa zao.

Angelo anauza Loti kuti: ‘Fulumila! Tenga mkazi wako ndi ana ako akazi aŵiliwa, ndipo mucoke mu mzindau!’ Loti ndi banja lake anali kuwaya-waya kucoka, conco angelo anawagwila padzanja ndi kuwatulutsa mu mzindawo. Pamenepo, mmodzi wa angelo anati: ‘Thaŵani mupulumutse moyo wanu! Musayang’ane kumbuyo. Thaŵilani kudela la kumapili kuti musaonongedwe!’

Loti ndi ana ake akazi anamvela ndipo anathaŵa kucoka mu Sodomu. Iwo sanaime ngakhale pang’ono, ndipo sanayang’ane kumbuyo. Koma mkazi wa Loti sanamvele. Pamene io anayenda kamtunda kucoka mu Sodomu, mkazi wa Loti anaima ndi kuyang’ana kumbuyo. Pamenepo anasanduka mwala wa mcele. Kodi wamuona pa cithunzi-thunzi apa?

Pamenepa tingatengepo phunzilo labwino kwambili lakuti, Mulungu amapulumutsa anthu amene amamumvela. Koma anthu amene samumvela adzawaononga.

Genesis 13:5-13; 18:20-33; 19:1-29; Luka 17:28-32; 2 Petulo 2:6-8.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani