LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 August tsa. 3
  • Kumbukilani Mkazi wa Loti

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kumbukilani Mkazi wa Loti
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Kumbukilani Mkazi wa Loti
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mkazi Wa Loti Anayang’ana Kumbuyo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Poyamba N’nali Wosauka, Koma Lomba N’nalemela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Thandizani Ena Kulimbana na Nkhawa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 August tsa. 3
Mkazi wa Loti ayang’ana kumbuyo ku mzinda wa Sodomu, ndipo asanduka culu ca m’cele

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kumbukilani Mkazi wa Loti

N’cifukwa ciani mkazi wa Loti anayang’ana kumbuyo pamene anali kuthaŵa kucoka mu mzinda wa Sodomu? Baibo siikamba. (Gen. 19:17, 26) Cenjezo limene Yesu anapeleka lionetsa kuti mwina iye anakonda kwambili zinthu zimene anasiya kumbuyo. (Luka 17:31, 32) Tingacite ciani kuti Mulungu asaleke kutiyanja monga mmene zinacitikila kwa mkazi wa Loti? Sitifunika kulola kuti kufuna-funa zinthu zakuthupi kukhale pamalo oyamba mu umoyo wathu. (Mat. 6:33) Yesu anaphunzitsa kuti ‘sitingathe kutumikila Mulungu ndi cuma nthawi imodzi.’ (Mat. 6:24.) Nanga bwanji ngati taona kuti zinthu zakuthupi zayamba kutidyela nthawi yocita zinthu zauzimu? Tingapemphele kwa Yehova kuti atipatse nzelu zotithandiza kuona pamene tifunika kuwongolela. Tingam’pemphenso kuti atipatse mphamvu na kutithandiza kukhala wolimba mtima kuti tikwanitse kuwongolela.

MOGWILIZANA NA VIDIYO YA MBALI ZITATU YAKUTI KUMBUKILANI MKAZI WA LOTI, YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Anna ali ku nchito; Gloria ali na amalume ake; Brian na Gloria apemphelela pamodzi

    Mwa zocita zanga, ningaonetse bwanji kuti ‘nimakumbukila mkazi wa Loti’?

    Kodi kufunitsitsa kukhala na ndalama zambili kunakhudza bwanji maganizo a Gloria, zokamba zake, na zocita zake?

  • N’cifukwa ciani mkazi wa Loti ni citsanzo coticenjeza ise masiku ano?

  • Kodi kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kunathandiza bwanji Joe na banja lake?

  • Kodi anzake a Anna a ku nchito anamusokoneza bwanji mwauzimu?

  • N’cifukwa ciani tifunika kukhala olimba mtima ngati ena atikakamiza kuika cuma pamalo oyamba mu umoyo wathu?

  • N’ciani cinathandiza Brian na Gloria kuyambilanso kuika zinthu zauzimu patsogolo?

  • Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene munaphunzila m’vidiyo imeneyi?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani