LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 80
  • Anthu A Mulungu Acoka Ku Babulo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anthu A Mulungu Acoka Ku Babulo
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Kudalila Thandizo La Mulungu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Dzanja Lilemba pa Cipupa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 80

Nkhani 80

Anthu A Mulungu Acoka Ku Babulo

TSOPANO papita zaka pafupi-fupi ziŵili kucokela pamene Amedi ndi Aperisiya analanda Babulo. Koma ona zimene zicitika tsopano! Aisiraeli acoka ku Babulo. Kodi io amasuka bwanji? Ndani waalola kuti apite?

Koresi, mfumu ya Perisiya ndiye waalola. Kale kwambili Koresi akalibe kubadwa, Yehova anauza mneneli wake Yesaya kulemba za Koresi kuti: ‘Udzacita zimene ine nifuna kuti ucite. Zitseko zidzakhala zotseguka kuti iwe ulande mzinda.’ Ndipo Koresi anatsogolela pa kulanda Babulo. Amedi ndi Aperisiya analoŵa mu mzinda usiku kupitila pa zitseko zimene anazisiya zotsegula.

Koma Yesaya mneneli wa Yehova anakambanso kuti Koresi adzapeleka lamulo lakuti Yerusalemu ndi kacisi amangidwenso. Kodi Koresi anapeleka lamulo limeneli? Inde, analipeleka. Izi ndiye zimene Koresi auza Aisiraeli kuti: ‘Pitani tsopano ku Yerusalemu, kuti mukamangenso nyumba ya Yehova, Mulungu wanu.’ Ndipo Aisiraeli awa apita kukacita zimenezo.

Koma si Aisiraeli onse amene angakwanitse kuyenda ulendo wautali wobwelela ku Yerusalemu. Ni ulendo wautali kwambili, wa makilomita 800, ndipo ambili ni okalamba kwambili kapena ndi odwala kwambili cakuti sangayende ulendo wautali umenewu. Ndipo panali zifukwa zina zimene anthu ena sanapitile. Koma Koresi auza aja amene sanapite kuti: ‘Pelekani siliva, golide, ndi katundu wina kwa ao amene abwelela ku Yerusalemu kuti akamangile kacisi.’

Conco, mphatso zambili zipelekedwa kwa Aisiraeli amene ali paulendo wobwelela ku Yerusalemu. Ndiponso Koresi awapatsa mbale ndi makapu amene mfumu Nebukadinezara anatenga mu kacisi wa Yehova pamene anaononga Yerusalemu. Anthu ali ndi katundu wambili wobwelela nao.

Aisiraeli ayenda ulendo umenewu kwa miyezi 4, ndipo afika ku Yerusalemu panthawi yake. Panapita zaka 70 kucokela pamene mzinda unaonongedwa, ndipo dzikolo linasiidwa lopanda munthu aliyense. Koma ngakhale kuti Aisiraeli ali ku dziko lao tsopano, io ali ndi mavuto ena, monga mmene tidzaonela mu nkhani yotsatila.

Yesaya 44:28; 45:1-4; Ezara 1:1-11.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani