LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 63 tsa. 150-tsa. 151 pala. 1
  • Dzanja Lilemba pa Cipupa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Dzanja Lilemba pa Cipupa
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Dzanja Lilemba Pacipupa
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Anthu A Mulungu Acoka Ku Babulo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 63 tsa. 150-tsa. 151 pala. 1
Dzanja lilemba pa cipupa

PHUNZILO 63

Dzanja Lilemba pa Cipupa

M’kupita kwa nthawi, Belisazara anakhala mfumu ya Babulo. Tsiku lina usiku, anakonzela nduna zake 1,000 phwando lalikulu. Analamula atumiki ake kuti abweletse makapu agolide, amene Nebukadinezara anatenga m’kacisi wa Yehova. Belisazara na nduna zake anamwela m’makapuwo, kwinaku akutamanda milungu yawo. Mwadzidzidzi, m’cipinda mmene anali kucitila phwandolo, anangoona dzanja ya munthu ikulemba mawu osadziŵika pacipupa.

Belisazara anacita mantha kwambili. Anaitanitsa amatsenga ake na kuwalonjeza kuti: ‘Aliyense amene angamasulile mawu aya, nidzamuika kukhala wolamulila wacitatu m’Babulo.’ Iwo anayesa-yesa, koma palibe amene anakwanitsa kumasulila mawuwo. Kenako mkazi wa mfumuyo anati: ‘Pali munthu wina dzina lake Danieli, amene anali kumasulila maloto a Nebukadinezara. Iye angamasulile mawu amenewa.’

Danieli anaitanidwa. Ndipo Belisazara anati kwa iye: ‘Ngati ungaŵelenge na kumasulila mawu awa, nidzakupatsa cheni yam’khosi yagolide, ndipo udzakhala wolamulila wacitatu m’Babulo.’ Danieli anati: ‘Mphatso zanu sinizifuna, koma nidzakuuzani tanthauzo la mawu amenewa. Atate wanu a Nebukadinezara anali munthu wonyada, ndipo Yehova anam’tsitsa. Mudziŵa bwino zonse zimene zinam’citikila. Koma imwe mwanyoza Yehova pomwela vinyo m’makapu agolide a m’kacisi wake. Ndiye cifukwa cake Mulungu walemba mawu aya akuti: Mene, Mene, Tekeli, ndi Parasin. Mawu awa atanthauza kuti Amedi ndi Aperisiya adzagonjetsa Babulo, ndipo inu simudzakhalanso mfumu.’

Asilikali a Koresi awoloka mtsinje na kungena pageti ya Babulo

Mzinda wa Babulo unali kuoneka kuti palibe angaugonjetse. Unali wotetezeka na zipupa zolimba, na mtsinje wonoka. Koma usiku umenewo, Amedi ndi Aperisiya anaugonjetsa mzindawo. Koresi Mfumu ya Perisiya inapatutsa madzi a mtsinjewo kuti asilikali ake awoloke kukafika pageti ya mzinda. Atafika pageti, anapeza kuti inali yotseguka! Gulu lonse la asilikali linangena na kugonjetsa mzindawo, komanso anapha mfumu yawo. Kenako Koresi anakhala wolamulila Babulo.

Caka cisanathe, Koresi analengeza kuti: ‘Yehova waniuza kuti nikamangenso kacisi wake ku Yerusalemu. Ndipo aliyense wa anthu ake amene afuna kukathandiza pa nchitoyo akhoza kupita.’ Conco, monga mmene Yehova analonjezela, Ayuda ambili anabwelela kwawo patapita zaka 70, kucokela pamene Yerusalemu anawonongedwa. Koresi anabweza makapu agolide komanso asiliva, na zinthu zina zimene Nebukadinezara anatenga m’kacisi. Kodi waona mmene Yehova anaseŵenzetsela Koresi kuti athandize anthu ake?

“Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa, ndipo wakhala malo okhala ziwanda.”—Chivumbulutso 18:2

Mafunso: Kodi mawu amene analembedwa pacipupa anali kutanthauza ciani? Kodi Yehova anauza Koresi kucita ciani?

Ezara 1:1-11; Danieli 5:1-30; Yesaya 44:27–45:2; Yeremiya 25:11, 12

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani