NKHANI 2
Mmene Mungasungile Cikumbumtima Cabwino
“Khalani ndi cikumbumtima cabwino.” —1 PETULO 3:16.
1, 2. N’cifukwa ciani toci yowala bwino ndi yofunika pamene tiyenda usiku? Nanga toci tingaiyelekezele bwanji ndi cikumbumtima?
TIYELEKEZELE kuti mukuyenda ulendo wapansi ndipo kwakudelani. Kodi muyenela kutenga ciani kuti musapunthwe mumdima, ndi kuti coipa cisakucitikileni? Muyenela kutenga toci yowala bwino kuti izikuunikilani m’njila.
2 Ngati mulibe toci yowala bwino simungaone kumene mukupita. Mukhoza kupunthwa ndi kugwa, kapena coipa cina cake cingakucitikileni. Koma toci yowala bwino ingakuunikileni njila ndi kukuthandizani kuti mukhale otetezeka. Motelo, tingayelekezele toci ndi cikumbumtima cimene ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa. (Yakobo1:17) Popanda cikumbumtima tikhoza kusocela ndi kutaikilatu. Koma ngati cikumbumtima cathu cimagwila bwino nchito, cingatithandize kudziwa zoyenela kucita kuti tikhalebe ndi umoyo wabwino. Conco, tiyeni tikambilane kuti tidziwe kuti cikumbumtima n’ciani ndiponso tione mmene cimagwilila nchito. Kenako tikambilananso mfundo izi: (1) Mmene tingaphunzitsile cikumbumtima cathu, (2) cifukwa cake tiyenela kuganizila zikumbumtima za anthu ena, ndi (3) madalitso amene timapeza cifukwa cokhala ndi cikumbumtima cabwino.
KODI CIKUMBUMTIMA N’CIANI, NDIPO CIMAGWILA NCHITO MOTANI?
3. Kodi liu la Cigiliki lotembenuzidwa kuti “cikumbumtima” limatanthauzanji kwenikweni? Nanga limanena za mphamvu yapadela iti imene anthufe tili nayo?
3 M’Baibulo liu la Cigiriki lotembenuzidwa kuti “cikumbumtima,” kwenikweni limatanthauza “kudzidziŵa ife eni.” Mosiyana ndi zolengedwa zina za padziko, anthufe tili ndi mphamvu imene Mulungu anatipatsa yokhoza kudzidziŵa bwino. M’mau ena, zili ngati timatha kuima patali ndi kudziyang’ana, kuona kuti khalidwe lathu lili bwanji. Cikumbumtima cathu cili monga mboni yamkati mwathu, kapena woweluza amene amasanthula zocita zathu, maganizo athu, ndi zosankha zathu. Cingatithandize kupanga cosankha cabwino kapena kuticenjeza kuti tisapange cosankha colakwika. Ndiyeno tikapanga cosankha cabwino cimatipatsa mtendele wa mumtima, koma tikapanga cosankha cosayenela cimatilanga mwa kutivutitsa mumtima.
4, 5. (a) Timadziŵa bwanji kuti onse aŵili Adamu ndi Hava anali ndi cikumbumtima? Ndipo cinacitika n’ciani pamene io anaphwanya lamulo la Mulungu? (b) Ndi zitsanzo ziti za cikumbumtima cogwila nchito zimene taona mwa anthu ena okhulupilika a m’nthawi zakale?
4 Anthufe tinalengedwa ndi mphamvu ya cikumbumtima imeneyi kucokela pa ciyambi penipeni. Onse aŵili, Adamu ndi Hava, anali ndi cikumbumtima. Umboni wa zimenezi ndi wakuti, io atacimwa anacita manyazi. (Genesis 3:7, 8) Koma panthawiyo cikumbumtima cao covutitsidwaco sicikanawathandiza cifukwa munali kale m’mbuyo mwa alendo. Iwo ananyalanyaza dala lamulo la Mulungu. Mwa kutelo, anasankha kupandukila Yehova Mulungu ndi kukhala otsutsana naye. Pokhala anthu angwilo, io anadziŵa zimene anali kucita, ndipo sakanabwelelanso kwa Mulungu.
5 Mosiyana ndi Adamu ndi Hava, pali anthu ambili opanda ungwilo amene anatsatila zimene cikumbumtima cao cinali kuwauza. Mwacitsanzo, munthu wokhulupilika Yobu anati: “Ndagwila cilungamo canga ndipo sindicitaya. Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.”a (Yobu 27:6) Yobu analidi munthu womvela cikumbumtima cake. Anacilola kum’tsogolela pa zocita ndi zosankha zake. Ndiye cifukwa cake anakamba motsimikiza mtima kuti cikumbumtima cake sicinam’tsutse kapena kum’vutitsa. Mosiyana ndi Yobu, onani mmene Davide anamvelela atanyalanyaza cikumbumtima cake. Pamene Davide anacita cinthu cosalemekeza Sauli, mfumu yodzozedwa ya Yehova, “Davide anavutika mumtima mwake.” (1 Samueli 24:5) Koma kuvutika ndi cikumbumtima kumeneko kunam’pindulitsa. Kunam’phunzitsa kuti ayenela kupewa kupanda ulemu koteloko mtsogolo.
6. N’ciani cimaonetsa kuti munthu aliyense ali ndi mphatso ya cikumbumtima?
6 Kodi ndi atumiki a Yehova okha amene ali ndi mphatso ya cikumbumtima? Ganizilani mau ouzilidwa a mtumwi Paulo akuti: “Nthawi zonse anthu a mitundu amene alibe cilamulo akamacita mwacibadwa zinthu za m’cilamulo, amakhala cilamulo kwa io eni ngakhale kuti alibe cilamulo. Amenewa ndio amasonyeza kuti mfundo za m’cilamulo zinalembedwa m’mitima mwao, pamene cikumbumtima cao cimacitila umboni pamodzi ndi iwowo, ndipo maganizo ao amawatsutsa ngakhalenso kuwavomeleza.” (Aroma 2:14, 15) Ngakhale anthu amene sadziŵa malamulo a Yehova, nthawi zina amacita zinthu zogwilizana ndi mfundo za Mulungu cifukwa ca cikumbumtima cao.
7. N’cifukwa ciani cikumbumtima nthawi zina cimasoceletsa?
7 Koma nthawi zina cikumbumtima cingatisoceletse. Cifukwa ciani? Kumbukilani citsanzo cija ca toci. Ngati mabatili a toci acepa mphamvu siingatiunikile bwino njila. N’zimene zimacitikanso ndi cikumbumtima cathu. Ngati sitiphunzila Mau a Mulungu, sitingathenso kusiyanitsa cabwino ndi coipa. Conco, ngati cikumbumtima cathu cisonkhezeledwa ndi zikhumbo zadyela za mtima wathu, cingayambe kutitsogolela ku njila zolakwika. Motelo, kuti cikumbumtima cathu cizigwila bwino nchito, timafunikila citsogozo ca mzimu woyela wa Yehova. Paulo analemba kuti: “Ine pamodzi ndi cikumbumtima canga tikucitila umboni mwa mzimu woyela.” (Aroma 9:1) Koma kodi tiyenela kucita ciani kuti cikumbumtima cathu cizitsogoleledwa ndi mzimu woyela wa Yehova? Tiyenela kuciphunzitsa.
MMENE TINGAPHUNZITSILE CIKUMBUMTIMA CATHU
8. (a) Kodi mtima ungakhudze bwanji cikumbumtima? Ndipo tiyenela kuganizila ciani tisanapange zosankha? (b) N’cifukwa ciani kungokhala ndi cikumbumtima coyela si kokwanila kwa Mkristu? (Onani mau a munsi.)
8 Kodi mumapanga bwanji zosankha potsatila cikumbumtima canu? Ena amangoyang’ana pa zimene io akuganiza, zimene mtima wao ukufuna, basi n’kupanga cosankha. Anganene kuti, “Koma cikumbumtima canga sicikunditsutsa.” Zokhumba za mtima zingakhale zamphamvu kwambili cakuti zingapondeleze cikumbumtima. Baibulo limakamba kuti: “Mtima ndi wonyenga kwambili kuposa cina ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa. Ndani angaudziŵe?” (Yeremiya 17:9) Conco, tisamangotsatila zimene mtima wathu ukufuna. M’malo mwake, tiyenela kuona cimene cingakondweletse Yehova Mulungu.b
9. Kodi kuopa Mulungu n’ciani? Nanga kukhala ndi mantha amenewa kumakhudza bwanji cikumbumtima cathu?
9 Ngati cosankha cathu cizikidwa pa cikumbumtima cathu cophunzitsidwa bwino, cosankhaco cidzaonetsa kuti timaopa Mulungu m’malo motsatila zofuna zathu. Taganizilani citsanzo cabwino ici cokhudza nkhani imeneyi. Bwanamkubwa wokhulupilika Nehemiya anali ndi ufulu wolamula anthu a ku Yerusalemu kuti azikhoma misonkho yosiyanasiyana kwa iye. Koma iye sanacite zimenezo. Cifukwa ciani? Iye sanafune kukwiyitsa Yehova ngakhale pang’ono mwa kuika mtolo pa anthu a Mulungu. Iye anati: “Koma ine sindinacite zimenezo cifukwa coopa Mulungu.” (Nehemiya 5:15) Inde, kuopadi Mulungu, kapena kuti kuopa kukhumudwitsa Atate wathu wakumwamba, n’kofunika kwambili. Kuopa Mulungu kwa conco, kudzatithandiza kufuna citsogozo ca Mau ake popanga zosankha.
10. Kodi m’Baibulo muli mfundo ziti zimene zingatithandize pankhani ya moŵa?
10 Mwacitsanzo, ganizilani nkhani ya kumwa moŵa. Tikakhala pamaceza, ambili timadzifunsa kuti, Kodi ndimwe kapena ai? Tisanapange cosankha tiyenela kudzifunsa kuti: Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingandithandize pankhaniyi? N’zoona kuti Baibulo sililetsa kumwa moŵa mwacikatikati. Ndipo limayamikila Yehova cifukwa ca mphatso ya vinyo. (Salimo 104:14, 15) Komabe, Baibulo limaletsa kumwa moŵa kwambili ndi maphwando aphokoso. (Luka 21:34; Aroma 13:13) Ndipo limaika kuledzela m’gulu la macimo aakulu, monga dama ndi cigololo.c—1 Akorinto 6:9, 10.
11. Ciani cimene tiyenela kucita kuti tipeze citsogozo ca Mulungu pankhani ya kumwa moŵa?
11 Cikumbumtima ca Mkristu cimaphunzitsidwa ndi kucenjezedwa ndi mfundo zimenezi. Conco, pofuna kupanga cosankha cakuti mukamweko moŵa kumaceza kapena ai, muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi maceza amenewo adzakhala a mtundu wanji? Kodi mwina adzakhala osalamulilika ndi aphokoso? Kodi ine ndimacita bwanji pankhani ya moŵa? Kodi ndimaulakalaka kwambili? Kodi ndimavutika ngati sindinamwe, kapena kodi ndimamwa kuti ndiiŵale mavuto? Kodi ndimadziletsa kuti ndisamwe kwambili?’ Pamene tisinkhasinkha pa mfundo za m’Baibulo ndi mafunso okhudza nkhaniyi, tiyenelanso kupempha citsogozo ca Yehova. (Ŵelengani Salimo 139:23, 24.) Mwa kutelo, timalola Yehova kuti atitsogolele ndi mzimu wake woyela. Timaphunzitsanso cikumbumtima cathu kuti cizigwilizana ndi mfundo za Mulungu. Komabe, palinso mbali ina imene tiyenela kuiganizila popanga zosankha.
N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUGANIZILA ZIKUMBUMTIMA ZA ENA?
Cikumbumtima cophunzitsidwa Baibulo cingakuthandizeni kusankha kumwa moŵa kapena kusamwa
12, 13. N’cifukwa ciani zikumbumtima za Akristu zimasiyanasiyana? Ndipo kusiyana kumeneku tiyenela kukuona bwanji?
12 Nthawi zina mungadabwe kuti zikumbumtima za Akristu zingasiyane kwambili. Wina angaone khalidwe lina kapena mwambo wina wake kukhala woipa, pamene wina angaone kuti palibe vuto lililonse. Mwacitsanzo, pankhani ya kumwa moŵa pamaceza, wina angafune kumwako moŵa ndi anzake poceza, pamene wina cikumbumtima cake cingamuletse kucita zimenezo. N’cifukwa ciani zikumbumtima zimasiyanasiyana conco, ndipo zimenezi ziyenela kukhudza bwanji zosankha zathu?
13 Ife anthu timasiyanasiyana pa zifukwa zambili. Mwacitsanzo, tinaleledwa m’njila zosiyanasiyana. Ena angakumbukile mmene kumbuyoku anavutikila polimbana ndi cifooko cina cake, ndipo mwina nthawi zina anali kulephela. (1 Mafumu 8:38, 39) Pankhani ya moŵa, anthu amenewa amakhala osamala kwambili. Ngati munthu wa conco wabwela kunyumba kwanu kudzaceza, cikumbumtima cake cingamuletse kumwa moŵa umene mungamupatse. Kodi muyenela kukhumudwa? Kodi muyenela kumukakamiza kumwa? Simuyenela kutelo. Kaya mukudziŵa zifukwa zake kapena ai, ndipo mwina zifukwazo sangafune kuzichula, simungam’kakamize kumwa ngati muli ndi cikondi ca paubale.
14, 15. Kodi zikumbumtima za Akristu a m’nthawi ya atumwi zinasiyana pankhani iti? Ndipo Paulo anapeleka malangizo otani?
14 Mtumwi Paulo anaona kuti zikumbumtima za Akristu a m’nthawi ya atumwi zinali zosiyanasiyana. Nthawi imeneyo, Akristu ena anali kuipidwa ndi zakudya zina zimene zinali zitapelekedwa nsembe ku mafano. (1 Akorinto 10:25) Paulo analibe vuto ndi cikumbumtima cake pa zakudya zimenezo pambuyo pakuti zapelekedwa kumsika kuti zikagulitsidwe. Iye anali kuona mafano kukhala opanda pake cifukwa cakuti anali kudziŵa kuti cakudyaco sicinali kucokela ku mafano koma kwa Yehova. Ngakhale n’conco, Paulo anazindikila kuti ena anali ndi maganizo osiyana ndi ake pankhaniyo. N’zotheka kuti ena anali kupembedza mafano kwambili asanakhale Akristu. Kwa io ciliconse cimene kale cinali cokhudzana ndi mafano cinali conyansa. Kodi Paulo anacita nayo bwanji nkhaniyo?
15 Paulo anati: “Ife olimba tiyenela kunyamula zofooka za osalimba, osati kumadzikondweletsa tokha ai. Pakuti ngakhale Kristu sanadzikondweletse yekha.” (Aroma 15:1, 3) Paulo anaonetsa kuti tiyenela kuganizila zofuna za abale athu coyamba m’malo mwa zofuna zathu monga mmene Kristu anacitila. Pankhani ina koma yofananako ndi imeneyi, Paulo anakamba kuti sadzadyanso nyama kuti asakhumudwitse nkhosa zamtengo wapatali zimene Kristu anafela.—Ŵelengani 1 Akorinto 8:13; 10:23, 24, 31-33.
16. N’cifukwa ciani anthu amene cikumbumtima cao siciwalola kucita zinthu zina sayenela kuweluza anzao?
16 Komanso, anthu amene cikumbumtima cao cimawatsutsa pa zinthu zina, sayenela kuweluza anzao, ndi kuumilila kuti aliyense atsatile cikumbumtima cao. (Ŵelengani Aroma 14:10.) Inde, tiyenela kugwilitsila nchito cikumbumtima cathu kudziweluza ife eni, osati kuweluzila ena. Kumbukilani mau a Yesu akuti: “Lekani kuweluza ena kuti inunso musaweluzidwe.” (Mateyu 7:1) Aliyense mumpingo ayenela kupewa mikangano pankhani za cikumbumtima. M’malo mwake, tiyenela kucita zinthu zolimbikitsa cikondi ndi mgwilizano, ndi kulimbikitsana osati kulefulana.—Aroma 14:19.
MMENE TIMAPINDULILA NDI CIKUMBUMTIMA CABWINO
Cikumbumtima cabwino cingatitsogolele paumoyo wathu, ndi kutipatsa cimwemwe ndi mtendele wa mumtima
17. N’ciani cacitikila zikumbumtima za anthu ambili masiku ano?
17 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khalani ndi cikumbumtima cabwino.” (1 Petulo 3:16) Kukhala ndi cikumbumtima coyela pamaso pa Yehova Mulungu ndi mphatso yamtengo wapatali. Cikumbumtima cotelo cimasiyana ndi zikumbumtima za anthu ambili masiku ano. Paulo anakamba za anthu “amene cikumbumtima cao cili ngati cipsela cobwela cifukwa copsa ndi citsulo camoto.” (1 Timoteyo 4:2) Citsulo camoto cimaocha mnofu ndi kusiyapo cipsela, ndipo mnofuwo umafa. Anthu ambili ali ndi cikumbumtima cakufa. Cikumbumtima cao cili ndi cipsela ndipo sicigwila nchito moti siciwacenjeza, kuwatsutsa, kuwamvetsa manyazi kapena kuwaimba mlandu akalakwa. Zangokhala ngati anthu ambili masiku ano alibiletu cikumbumtima.
18. Kodi kumva cisoni kapena manyazi kungakhale ndi ubwino wotani?
18 Kumva cisoni kungakhale njila ina imene cikumbumtima cimatiuzila kuti talakwa. Ngati cisoni cimeneco cipangitsa wolakwa kuti alape, ngakhale macimo ake akule bwanji angakhululukidwe. Mwacitsanzo, Mfumu Davide anamva cisoni pambuyo pocita chimo lalikulu, koma anakhululukidwa cifukwa analapa kucokela pansi pa mtima. Kudana ndi coipa cimene anacita ndi kufunitsitsa kutsatila malamulo a Yehova, kunam’cititsa kuti aone yekha kuti Yehova ndi ‘wabwino ndipo ndi wokonzeka kukhululuka.’ (Salimo 51:1-19; 86:5) Nanga bwanji ngati tipitiliza kuvutika kwambili ndi cisoni ndi kucita manyazi ngakhale pambuyo pakuti tinalapa ndi kukhululukidwa?
19. Tingacite ciani ngati cikumbumtima cathu cipitiliza kutivutitsa cifukwa ca macimo akale amene tinalapa?
19 Nthawi zina cikumbumtima cingavutitse munthu mopitilila malile, ndi kum’pangitsa kudzimva wolakwa kwa nthawi yaitali ngakhale pambuyo pakuti walapa ndi kusiya chimolo. Zikakhala conco, tiyenela kutsimikizila mtima wathu kuti Yehova ndi wamkulu koposa mtima wathu wopanda ungwilo. Tiyenela kukhulupilila Yehova ndi kulandila cikondi ndi cikhululukilo cake, monga mmene timalimbikitsila ena. (Ŵelengani 1 Yohane 3:19, 20.) Koma cikumbumtima coyela, cimabweletsa mtendele wa mumtima ndi cimwemwe cacikulu cimene sicipezekapezeka m’dzikoli. Ambili amene kale anacita macimo aakulu, apeza mpumulo ndipo palipano amatumikila Yehova Mulungu ndi cikumbumtima coyela.—1 Akorinto 6:11.
20, 21. (a) Kodi buku lino analilemba kuti likuthandizeni kucita ciani? (b) Pokhala Akristu, ndi ufulu wotani umene tili nao? Nanga tiyenela kuugwilitsila nchito bwanji?
20 Buku lino linalembedwa kuti likuthandizeni kupeza cimwemwe cimeneco, ndi kukhala ndi cikumbumtima cabwino m’masiku otsiliza ndi ovuta ano a dongosolo la zinthu la Satana. Koma sikuti lidzafotokoza mbali zonse za malamulo a m’Baibulo ndi mfundo zimene muyenela kugwilitsila nchito paumoyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Ndiponso, musayembekezele kuti mungapeze malamulo acindunji pa nkhani zokhudza cikumbumtima. Colinga ca buku lino ndi kukuthandizani kuti muphunzitse cikumbumtima canu mwa kuphunzila mmene mungagwilitsilile nchito Mau a Mulungu paumoyo wanu. Mosiyana ndi Cilamulo ca Mose, “cilamulo ca Kristu” cimalimbikitsa Akristu kutsatila cikumbumtima ndi mfundo za makhalidwe abwino, m’malo motsatila malamulo olembedwa. (Agalatiya 6:2) Mwa kutelo, Yehova wapatsa Akristu ufulu waukulu. Komabe, Mau ake amaticenjeza kuti tisagwilitsile nchito ufulu umenewo kukhala “cophimbila zoipa.” (1 Petulo 2:16) M’malo mwake, ufulu umenewu umatipatsa mwai wapadela woonetsa kuti Yehova timam’konda.
21 Ngati mupemphela kwa Mulungu kuti akuthandizeni kupanga zosankha zogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo paumoyo wanu ndi kuzigwilitsila nchito, mudzapitiliza kucita cinthu cina cofunika kwambili cimene munayamba pamene munadziŵa Yehova. Cinthuco ndico kuphunzitsa ‘mphamvu zanu za kuzindikila.’ (Aheberi 5:14) Cikumbumtima canu cophunzitsidwa Baibulo cidzakhala dalitso lanu tsiku ndi tsiku. Mofanana ndi toci yowala bwino yokuunikilani njila usiku, cikumbumtima canu cingakuthandizeni kupanga zosankha zokondweletsa Atate wanu wakumwamba. Imeneyi ndiyo njila yodalilika imene ingakuthandizeni kukhalabe m’cikondi ca Mulungu.
a M’malemba Aciheberi mulibe liu lenileni lotanthauza “cikumbumtima.” Komabe mogwilizana ndi citsanzo ici, pali umboni woonekelatu wakuti anthu anali kumvela cikumbumtima cao. Liu lakuti “mtima” nthawi zambili limatanthauza munthu wamkati. Koma pa lembali, liu limeneli limakamba za cikumbumtima, cimene ndi mbali imodzi cabe ya munthu wamkati. Liu la Cigiriki lotembenuzidwa kuti “cikumbumtima” limaonekela nthawi 30 m’Malemba Acigiriki Acikristu.
b Baibulo limaonetsa kuti, kungokhala ndi cikumbumtima coyela sikokwanila. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anati: “Sindikudziŵa kanthu kalikonse konditsutsa mumtima mwanga. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti basi ndine wolungama, koma Yehova ndiye amandifufuza.” (1 Akorinto 4:4) Ngakhale anthu amene amazunza Akristu, monga mmene Paulo anali kucitila, angacite zimenezo ndi cikumbumtima coyela, ndi kumaganiza kuti Mulungu amavomeleza zocita zao. Conco, n’kofunika kuti cikumbumtima cathu cikhale coyela kwa ife ndi kwa Mulungu.—Machitidwe 23:1; 2 Timoteyo 1:3.
c Dziŵaninso kuti madokotala ambili amati munthu akafika pa ucidakwa n’zosatheka kumwa moŵa mwacikatikati. Kwa iye “cikatikati” ndi kulekelatu kumwa.