NKHANI 15
Sangalalani Cifukwa Cogwila Nchito Yanu Mwakhama
‘Munthu aliyense . . . asangalale ndi zinthu zabwino cifukwa cogwila nchito mwakhama.’ —MLALIKI 3:13.
1-3. (a) Kodi anthu ambili amaiona bwanji nchito yao? (b) Kodi Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziiona bwanji nchito? Nanga ndi mafunso ati amene tidzakambilana m’nkhani ino?
MASIKU ano anthu ambili sakondwela ndi nchito yao. Kukaca m’maŵa, io safuna kupita ku nchito cifukwa cakuti amagwila nchito yolemetsa ya maola ambili imene sasangalala nayo. Kodi n’ciani cingathandize anthu amene ali ndi vuto limeneli kuti azisangalala ndi nchito yao komanso kukhutila nayo?
2 Baibulo limatilimbikitsa kuona nchito moyenelela. Limanena kuti nchito limodzinso ndi mapindu ake ndi mphatso. Solomo analemba kuti: “Munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, cifukwa coti wagwila nchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Yehova amatikonda, ndipo nthawi zonse amatifunila zabwino. Conco, iye amafuna kuti tizikhala okhutila ndi nchito yathu ndi kusangalala ndi zipatso za nchito yathu. Kuti tikhalebe m’cikondi cake, tiyenela kuona nchito mmene iye amaionela ndi kutsatila mfundo zake pankhani imeneyi.—Ŵelengani Mlaliki 2:24; 5:18.
3 M’nkhani iyi tidzakambilana mafunso anai awa: Kodi tingacite ciani kuti tisangalale cifukwa cogwila nchito mwakhama? Ndi nchito ziti zimene Akristu oona sayenela kugwila? Kodi tingagaŵe bwanji nthawi yogwila nchito ya kuthupi ndi ya kuuzimu? Nanga ndi nchito yofunika kwambili iti imene tiyenela kugwila? Koma coyamba, tiyeni tikambilane citsanzo ca anthu aŵili amene amagwila nchito kuposa onse m’cilengedwe conse. Anthu amenewa ndi Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu.
YEHOVA MULUNGU NDIPONSO MMISILI WAKE NDI AKHAMA PA NCHITO
4, 5. Kodi Baibulo limaonetsa bwanji kuti Yehova amagwila nchito mwakhama?
4 Yehova amagwila nchito kuposa wina aliyense. Lemba la Genesis 1:1 limati: “Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Pamene Mulungu anamaliza kulenga zinthu padziko lapansi, ananena kuti zinthuzo “zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) M’mau ena, tingakambe kuti iye anakhutila kwambili ndi zimene analenga padziko lapansi. N’zosakaikitsa kuti Yehova, “Mulungu wacimwemwe,” anasangalala kwambili cifukwa cogwila nchito mwakhama.—1 Timoteyo 1:11.
5 Mulungu wathu ndi wakhama pa nchito ndipo saleka kugwila nchito. Patapita zaka zambili pambuyo polenga dziko lapansi ndi zonse za m’dziko, Yesu anati: “Atate wanga akugwilabe nchito mpaka pano.” (Yohane 5:17) Kodi Atatewo akhala akugwila nchito yotani? Kucokela kumwamba kumene amakhala, io apitilizabe kutsogolela ndi kusamalila anthu. Anapanga “colengedwa catsopano” cimene ndi Akristu odzodzedwa amene adzalamulila ndi Yesu kumwamba. (2 Akorinto 5:17) Atate akhala akugwilabe nchito kuti akwanilitse colinga cao kwa anthu. Colinga cimeneci n’cakuti anthu amene amamukonda akalandile moyo wamuyaya m’dziko latsopano. (Aroma 6:23) Yehova ayenela kuti ndi wosangalala kwambili ndi zipatso za nchito yake. Anthu mamiliyoni ambili alandila uthenga wa Ufumu ndipo akokedwa ndi Mulungu moti asintha umoyo wao kuti akhalebe m’cikondi cake.—Yohane 6:44.
6, 7. Kodi Yesu ali ndi mbili yotani pa nkhani yogwila nchito mwakhama?
6 Yesu ali ndi mbili yabwino yogwila nchito mwakhama kwa nthawi yaitali. Asanabwele padziko lapansi, iye anatumikila monga “mmisili waluso” wa Mulungu polenga zinthu zonse “zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” (Miyambo 8: 22-31; Akolose 1:15-17) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anapitilizabe kugwila nchito mwakhama. Akali mwana, iye anaphunzila nchito yomanga ndipo anali kudziŵika kuti ndi “mmisili wamatabwa.”a (Maliko 6:3) Nchito imeneyi imafuna mphamvu ndi luso, makamaka panthawi imene kunalibe makina amakono ocekela matabwa, masitolo ogulako zofunikila ndi zipangizo zamagetsi. Yelekezani kuti mukuona Yesu akupita kukafunafuna mitengo, kuidula, kuigubuduza mpaka kumalo ake ogwilila nchito. Kenako mukumuona akumanga nyumba, kukhoma denga, kupanga zitseko ndi zinthu zina zamatabwa. N’zosacita kufunsa kuti Yesu anali kusangalala cifukwa cogwila nchito mwakhama ndi mwaluso.
7 Yesu anali wakhama kwambili pogwila nchito yake yolalikila. Kwa zaka zitatu ndi theka, anali otangwanika ndi nchito yofunika kwambili imeneyi. Pofuna kufikila anthu ambili, iye masiku onse anali kugwila nchito mwakhama, kuyambila m’mamawa mpaka usiku kwambili. (Luka 21:37, 38; Yohane 3:2) Iye anali kuyenda “mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikila ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Yesu anali kuyenda ulendo wapansi mitunda ya makilomita ambili m’miseu ya fumbi kuti akalalikile uthenga wabwino.
8, 9. Kodi Yesu anasangalala motani cifukwa cogwila nchito mwakhama?
8 Kodi Yesu anasangalala cifukwa cogwila nchito yake yolalikila mwakhama? Inde anatelo. Iye anafesa mbeu za coonadi ca Ufumu, moti anasiya minda yofunika kukolola. Yesu anali kupeza mphamvu ndiponso kukhala okhutila cifukwa cogwila nchito ya Mulungu, cakuti analolela kukhala osadya pofuna kugwila nchitoyi. (Yohane 4:31-38) Taganizilani cisangalalo cimene anali naco pamene anamaliza utumiki wake padziko lapansi ndi kuuza Atate wake ndi mtima wonse kuti: “Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiliza kugwila nchito imene munandipatsa.”—Yohane 17:4.
9 Kunena zoona, Yehova ndi Yesu ndi zitsanzo zabwino koposa za anthu amene amasangalala cifukwa cogwila nchito yao mwakhama. Cikondi cathu pa Yehova cimatilimbikitsa ‘kutsanzila Mulungu.’ (Aefeso 5:1) Cikondi cathu pa Yesu cimatilimbikitsa ‘kutsatila mapazi ake mosamala kwambili.’ (1 Petulo 2:21) Tiyeni tsopano tikambilane zimene tingacite kuti tisangalale cifukwa cogwila nchito mwakhama.
ZIMENE TINGACITE KUTI TISANGALALE CIFUKWA COGWILA NCHITO MWAKHAMA
Kutsatila mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kusangalala cifukwa cogwila nchito yanu mwakhama
10, 11. N’ciani cimene cingatithandize kuona nchito yathu moyenelela?
10 Akristu oona naonso amafunikila kugwila nchito. Timafuna kusangalala ndi kukhutila ndi nchito yathu. Koma zimenezi zingakhale zovuta makamaka ngati nchito imene timagwila sitiikonda. Ngati zili conco, kodi zingatheke bwanji kusangalala ndi nchito yathu?
11 Tiziona zinthu moyenelela. Si nthawi zonse pamene tingasinthe zinthu pa nchito, koma tingasinthe mmene timaonela nchitoyo. Kuganizila mmene Mulungu amaonela nchito kungatithandize kuona nchito yathu moyenela. Mwacitsanzo, ngati ndinu mutu wa banja, ganizilani mfundo yakuti nchito yanu ngakhale ioneke yonyozeka bwanji, imakuthandizani kusamalila banja lanu. Ndipo kusamalila banja lanu si nkhani yaing’ono kwa Mulungu. Mau ake amati, munthu amene sasamalila banja lake “ndi woipa kuposa munthu wosakhulupilila.” (1 Timoteyo 5:8) Kuzindikila kuti nchito yanu imakuthandizani kukwanilitsa udindo umene Mulungu anakupatsani, kungakuthandizeni kuti mukhale okhutila ndi nchito yanu poyelekezela ndi anchito anzanu.
12. Kodi kugwila nchito mwakhama ndi moona mtima kuli ndi mapindu otani?
12 Tizikhala akhama ndi oona mtima. Kugwila nchito mwakhama ndi kuonjezela luso lanu pa nchitoyo, kungakupindulitseni. Mabwana amakonda kwambili anchito akhama ndi aluso. (Miyambo 12:24; 22:29) Monga Akristu oona, tiyenela kukhala oona mtima pa nchito yathu. Sitiyenela kubela abwana athu ndalama, katundu, kapena nthawi. (Aefeso 4:28) Monga mmene tinaonela m’nkhani yapita, kukhala oona mtima kumapindulitsa. Munthu amene amadziŵika kuti ndi woona mtima pa nchito, ena amam’dalila. Ndipo kaya abwana athu adziŵa kuti timalimbikila nchito kapena ai, tingakhalebe osangalala. Izi zili conco cifukwa cakuti timakhala ndi “cikumbumtima coona” ndipo timadziŵa kuti tikukondweletsa Mulungu amene timakonda.—Aheberi 13:18; Akolose 3:22-24.
13. Kodi khalidwe lathu labwino kunchito lingakhale ndi ubwino wotani?
13 Tizidziŵa kuti khalidwe lathu lingalemekeze Mulungu. Ngati tipitiliza kukhala ndi khalidwe labwino lacikristu kunchito, ena angaone khalidwe lathu. Kodi zimenezi zili ndi ubwino wotani? Zingapangitse kuti ‘tikometsele ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu Mulungu.’ (Tito 2:9, 10) Inde, khalidwe lathu labwino lingathandize ena kuona ubwino wa kulambila kwathu, ndipo angakopeke nako. Taganizilani mmene mungamvelele ngati amene mugwila naye nchito waphunzila coonadi cifukwa ca khalidwe lanu labwino kunchito. Kodi pali cina cimene cingakusangalatseni kuposa kudziŵa kuti khalidwe lanu labwino limalemekeza Yehova ndi kusangalatsa mtima wake?—Ŵelengani Miyambo 27:11; 1 Petulo 2:12.
KUSANKHA NCHITO MWANZELU
14-16. Posankha nchito, kodi ndi mafunso ofunika kwambili ati amene tiyenela kuganizila?
14 Baibulo silichula mwacindunji nchito imene tiyenela kugwila ndi imene sitiyenela kugwila. Zimenezi sizitanthauza kuti tingagwile nchito iliyonse malinga ndi nchito. Malemba angatithandize kusankha nchito yabwino imene imakondweletsa Mulungu, ndi kupewa imene sakondwela nayo. (Miyambo 2:6) Posankha nchito, tifunika kuganizila mafunso aŵili ofunika kwambili.
15 Kodi nchito imeneyi ingandipangitse kucita zinthu zimene Baibulo limaletsa? Mau a Mulungu, mosapita m’mbali, amatiletsa kuba, kunama, ndi kupanga mafano. (Ekisodo 20:4; Machitidwe 15:29; Aefeso 4:28; Chivumbulutso 21:8) Sitiyenela kugwila nchito iliyonse imene ingafune kuti tizicita zinthu zimenezi. Cifukwa cokonda Yehova, sitidzagwila nchito imene imaphatikizapo kucita zinthu zotsutsana ndi malamulo a Mulungu.—Ŵelengani 1 Yohane 5:3.
16 Kodi nchito imeneyi ingaonetse kuti ndikucilikiza kapena kulimbikitsa khalidwe loipa? Ganizilani citsanzo ici: Kugwila nchito pa malo ofikila alendo sikulakwa. Koma bwanji ngati Mkristu apeza nchito ku cipatala kumene amacotsela mimba? N’zoona kuti nchito yake singafune kuti iye athandizile kucotsa mimba mwacindunji. Komabe, kodi nchito yake singakhale kuti ikucilikiza nchito ya cipatala yocotsa mimba, zimene Mau a Mulungu amaletsa? (Ekisodo 21:22-24) Popeza timakonda Yehova, tiyenela kupewelatu zinthu zimene Malemba amaletsa.
17. (a)Kodi tiyenela kuganizila mfundo ziti posankha nchito? (Onani bokosi lakuti “Kodi Nchito Imeneyi Ndi Yoyenela Kwa Ine?”) (b) Kodi cikumbumtima cathu cingatithandize bwanji kupanga zosankha zokondweletsa Mulungu?
17 Mafunso ambili okhudza nchito, angayankhidwe mwa kuganizila mayankho a mafunso aŵili ofunika kwambili amene takambitsilana mu ndime 15 ndi 16. Kuonjezela pamenepa, pali mfundo zina zimene tiyenela kuziganizila mosamala tisanasankhe nchito.b Sitingayembekezele kapolo wokhulupilika ndi wanzelu kutipatsa m’ndandanda wa malamulo okhudza mmene tingasankhile nchito. Apa m’pamene pangafune kuti tikhale ozindikila bwino. Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 2, tiyenela kuphunzitsa cikumbumtima cathu, mwa kuphunzila mmene tingagwilitsile nchito Mau a Mulungu pa moyo wathu. Tikaphunzitsa ‘mphamvu zathu za kuzindikila’ mwa ‘kuzigwilitsila nchito,’ cikumbumtima cathu cidzatithandiza kupanga zosankha zokondweletsa Mulungu ndi kukhalabe m’cikondi cake.—Aheberi 5:14.
KHALANI NDI MAGANIZO OYENELA PANKHANI YA NCHITO
18. N’cifukwa ciani n’kovuta kupanga zosankha zimene zingatithandize kukhalabe m’cikondi ca Yehova?
18 Kupanga zosankha zimene zingatithandize kukhalabe m’cikondi ca Yehova n’kovuta ‘m’masiku otsiliza’ ano amene ndi ‘nthawi yovuta.’ (2 Timoteyo 3:1) Kupeza nchito ndi kuisunga kungakhale kovuta kwambili. Monga Akristu oona, timadziŵa kuti kugwila nchito mwakhama n’kofunika kuti tisamalile banja lathu. Koma ngati sitisamala, kutangwanika ndi nchito kapena mzimu wa dziko wokonda cuma zingatilepheletse kucita zinthu za kuuzimu. (1 Timoteyo 6:9, 10) Tiyeni tikambilane mmene tingalinganizile zinthu kuti tizitsimikizila kuti “zinthu zofunika kwambili ndi ziti.”—Afilipi 1:10.
19. N’cifukwa ciani Yehova ndi woyeneladi kum’khulupilila? Ndipo tikamudalila tidzapewa ciani?
19 Khulupililani Yehova ndi mtima wanu wonse. (Ŵelengani Miyambo 3:5, 6.) Iye ndi woyeneladi kum’khulupilila cifukwa amatidela nkhawa. (1 Petulo 5:7) Amadziŵa zimene timafunikila kuposa mmene ife timadziŵila, ndipo sangalephele kutithandiza. (Salimo 37:25) Conco, tiyenela kumvela pamene Mau ake amatikumbutsa kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’” (Aheberi 13:5) Atumiki a nthawi zonse ambili angacitile umboni kuti Mulungu amawapatsa zofunika pa umoyo wao. Ngati timakhulupililadi kuti Yehova adzatisamalila, tidzapewa kuda nkhawa kwambili ndi mmene tingasamalile banja lathu. (Mateyu 6:25-32) Sitidzalola nchito kutipangitsa kunyalanyaza zinthu za kuuzimu monga kulalikila uthenga wabwino ndi kusonkhana.—Mateyu 24:14; Aheberi 10:24, 25.
20. Kodi kukhala ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi kumatanthauzanji? Nanga mungacite ciani kuti mukhale ndi diso lotelo?
20 Khalani ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi. (Ŵelengani Mateyu 6:22, 23.) Kukhala ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi kumatanthauza kukhala ndi umoyo wosalila zambili. Diso lolunjika pa cinthu cimodzi la Mkristu limam’thandiza kusumika maganizo ake pa kucita cifunilo ca Mulungu. Ngati diso lathu ndi lolunjika bwino, sitidzatangwanika ndi kufunafuna nchito ya malipilo apamwamba ndi umoyo wofuna zambili. Ndipo sitidzatengeka ndi mzimu wofuna zinthu zatsopano ndi zapamwamba zimene otsatsa malonda amanena kuti tidzasangalala tikakhala nazo. Kodi mungacite bwanji kuti mukhale ndi diso lolunjika pa cinthu cimodzi? Pewani kudziloŵetsa m’nkhongole zosafunikila. Musacolowanitse umoyo wanu ndi zinthu zimene zingakudyeleni nthawi. Tsatilani uphungu wa m’Baibulo wakuti tizikhala okhutila ndi “zovala ndi pogona.” (1 Timoteyo 6:8) Yesetsani kukhala ndi umoyo wosalila zambili.
21. N’cifukwa ciani tiyenela kuika zinthu zofunika patsogolo? Nanga n’ciani cimene ciyenela kukhala patsogolo pa umoyo wathu?
21 Yesetsani kuika zinthu za kuuzimu patsogolo. Popeza kuti sitingakwanitse kucita zonse zimene timafuna pa umoyo, tifunika kuika zinthu zofunika patsogolo. Ngati tilephela kutelo, zinthu zosafunika zingatidyele nthawi, ndi kutilepheletsa kucita zinthu zofunika kwambili. Kodi n’ciani cimene tiyenela kuika patsogolo? Anthu ambili amaona kuti maphunzilo apamwamba ndi ofunika kwambili kuti munthu akapeze nchito yapamwamba. Koma Yesu analimbikitsa otsatila ake ‘kupitiliza kufunafuna Ufumu coyamba.’ (Mateyu 6:33) Inde,monga Akristu oona timaika Ufumu wa Mulungu patsogolo. Ciliconse pa umoyo wathu, monga zosankha zathu, zolinga zathu, ndi zocita zathu, ziyenela kuonetsa kuti timaona zinthu za ufumu ndi kucita cifunilo ca Mulungu kukhala zofunika kwambili kuposa zinthu zakuthupi.
KUGWILA NCHITO MWAKHAMA MU ULALIKI
Tingaonetse kuti timakonda Yehova mwa kuika nchito yolalikila patsongolo
22, 23. (a) Kodi nchito yaikulu ya Akristu oona ndi iti? Nanga tingaonetse bwanji kuti timaona nchitoyo kukhala yofunika? (Onani bokosi lakuti “Cosankha Canga Candibweletsela Cimwemwe Ndi Cikhutilo.”) (b) Kodi nchito yakuthupi muyenela kuiona motani?
22 Popeza kuti tili kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiliza, timaika maganizo athu pa nchito yofunika kwambili ya Akristu oona, imene ndi kulalikila ndi kupanga ophunzila. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Mofanana ndi Yesu citsanzo cathu, tifunika kukhala otangwanika kwambili ndi nchito yopulumutsa miyoyo imeneyi. Kodi tingaonetse bwanji kuti timaona nchito imeneyi kukhala yofunika kwambili? Atumiki ambili a Mulungu amadzipeleka ndi mtima wonse kugwila nchito yolalikila monga ofalitsa pa mpingo. Ena asintha zinthu pa umoyo wao kuti atumikile monga apainiya kapena amishonale. Makolo ambili amalimbikitsa ana ao kuyamba utumiki wa nthawi zonse cifukwa amaona kuti zolinga za kuuzimu n’zofunika kwambili. Kodi alaliki acangu a Ufumu amasangalala cifukwa cogwila nchito mwakhama muulaliki? Inde amatelo. Kutumikila Yehova ndi moyo wathu wonse kumatipatsadi cimwemwe, cikhutilo, ndi madalitso ena ambili.—Ŵelengani Miyambo 10:22.
23 Ambili a ife timagwila nchito maola ambili kuti tisamalile banja lathu. Koma musaiŵale kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala cifukwa cogwila nchito yathu mwakhama. Ngati timaona ndi kucita zinthu mogwilizana ndi maganizo ndi mfundo zake, tingakhale okhutila ndi nchito yathu. Conco, tiyeni tionetsetse kuti sitilola nchito yakuthupi kusokoneza nchito yathu yaikulu yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Mwa kuika nchito imeneyi patsogolo, timaonetsa kuti timakonda Yehova ndipo timafuna kukhalabe m’cikondi cake.
a Buku lina linati, liu la Cigiriki lomasulidwa kuti “mmisili wamatabwa,” ndi “dzina la munthu amene amagwilitsila nchito matabwa pomanga nyumba kapena zinthu zina zilizonse za matabwa.”
b Kuti mudziŵe zambili zokhudza mfundo zimene muyenela kuziganizila pa nkhani ya nchito, onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999, patsamba 28 mpaka 30, ndi ya Cingelezi ya July 15, 1982, patsamba 26.