CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MLALIKI 1–6
Muzikondwela Pogwila Nchito Mwakhama
Yehova amafuna kuti tizikondwela na nchito yathu, ndipo amatiuza zimene zingatithandize. Munthu angayambe kukondwela na nchito yake ngati amaiona moyenela.
Kuti muzikondwela na nchito yanu, mufunika . . .
3:13; 4:6
kukhala na maganizo oyenela
kuganizila mmene nchito yanu imapindulitsila ena
kugwila nchito mwakhama. Koma mukakomboka, muzikhala na nthawi yoceza na banja lanu ndi kucita zinthu zauzimu