Nyimbo 67
Muzipemphera kwa Yehova Tsiku Lililonse
(1 Atesalonika 5:17)
1. Pemphera kwa Yehova amamva.
Ndi mwayi umene watipatsa.
Mu’ze zakukhosi monga mnzako,
Ndi wodalirika, bwenzi lako.
Pempherabe kwa M’lungu.
2. Pemphera kwa M’lungu uthokoze.
Um’pemphe akukhululukire.
Timuuze zakukhosi kwathu,
Amadziwa zofooka zathu.
Pempherabe kwa M’lungu.
3. Pemphera kwa M’lungu zikavuta,
Ndi Tate wathu akuthandiza.
Um’pemphe kuti akuteteze,
Um’khulupirire usaope.
Pempherabe kwa M’lungu.
(Onaninso Mat. 6:9-13; 26:41; Luka 18:1.)