Nyimbo 72
Tizisonyeza Chikondi
1. Tikupemphera kwa Mulungu,
Kuti tizikonda anzathu.
Tikakhala ndi mzimu wake
Ndiye kuti tingakondane.
Tingakhale ndi luso, nzeru,
Komabe osakonda anthu.
Izi sizingatithandize.
Choncho chikondi tikulitse.
2. Tisadalire nzeru zokha
Pamene tiphunzitsa nkhosa.
Ndi kofunika kuzikonda
Kuti cho’nadi chizilowa.
Ngakhale tikalakwiridwa
Tidzakhalabe opirira.
Chikondi chipirira zonse
Ndiponso sichidzatha konse.
(Onaninso Yoh. 21:17; 1 Akor. 13:13; Agal. 6:2.)