LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ll gao 4 masa. 10-11
  • Anamvetsela kwa Satana—Nanga Cinacitika n’Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anamvetsela kwa Satana—Nanga Cinacitika n’Ciani?
  • Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Gao 4
    Mvetselani kwa Mulungu
  • Kodi Akufa Ali Kuti?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • N’cifukwa Ciani Timakalamba Na Kufa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
Onaninso Zina
Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
ll gao 4 masa. 10-11

GAO 4

Anamvetsela kwa Satana—Nanga Cinacitika n’Ciani?

Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu, conco anafa. Genesis 3:6, 23

Hava akudya cipatso coletsedwa ndipo akupatsako Adamu

Hava anamvetsela ku njoka ndipo anadya cipatso. Pambuyo pake, anapatsako Adamu, ndipo naye anadya.

Adamu na Hava acoka m’dziko lawo la Paladaiso

Cimene iwo anacita cinali coipa—ni chimo. Mulungu anawathamangitsa m’mudzi wawo wa Paladaiso.

Adamu na Hava akalamba ndi kufa m’kupita kwa nthawi

Umoyo wawo ndi wa ana awo unakhala wovuta. Iwo anakalamba ndi kufa. Sanapite kumalo a mizimu; analeka kukhala ndi moyo.

Dothi lilibe moyo; ndi mmene akufa alili. Genesis 3:19

Anthu a zikhalidwe zosiyana-siyana m’mibadwo yosiya-siyana

Timafa cifukwa tinacokela kwa Adamu ndi Hava. Akufa sangaone kapena kumva kapena kucita cina ciliconse.—Mlaliki 9:5, 10.

Mtsikana wamwalila ndipo makolo na abululu ake akulila

Yehova sanafune kuti anthu tizifa. Posacedwa adzaukitsa akufa. Ngati iwo adzamvetsela kwa iye, adzakhala ndi moyo wamuyaya.

  • N’cifukwa ciani timafa?—Aroma 5:12.

  • Imfa sidzakhalako.—1 Akorinto 15:26.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani