LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ll gao 3 masa. 8-9
  • Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?
  • Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Anataila Malo Ao Okhalako
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Anamvetsela kwa Satana—Nanga Cinacitika n’Ciani?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Gao 3
    Mvetselani kwa Mulungu
  • Adamu na Hava Sanamvele Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
ll gao 3 masa. 8-9

GAO 3

Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?

Yehova anapatsa Adamu ndi Hava zinthu zabwino zambili. Genesis 1:28

Yehova atalenga Hava, anam’peleka kwa Adamu

Yehova anapanga Hava, mkazi woyamba, ndipo anamupeleka kwa Adamu kuti akhale mkazi wake.—Genesis 2:21, 22.

Yehova anawalenga ndi maganizo ndi matupi angwilo, opanda coipa ciliconse.

Adamu na Hava akuyang’ana dziko lawo la Paladaiso

Mudzi wao unali munda wa Edeni, ndipo malo ake anali okongola. Munali mitsinje, mitengo ya zipatso, ndi nyama.

Yehova anali kukamba nao ndi kuwaphunzitsa. Ngati anamvetsela kwa iye, akanakhala ndi moyo wamuyaya m’Paladaiso padziko lapansi.

Mulungu anawaletsa kudya mtengo umodzi cabe. Genesis 2:16, 17

Mtengo umodzi m’munda umene Yehova analetsa Adamu na Hava kuti asadye zipatso zake

Yehova anaonetsa Adamu ndi Hava mtengo umodzi wa zipatso umene unali m’munda ndipo anawauza kuti ngati adzadya umenewo, adzafa.

Mngelo woipa, Satana Mdyelekezi, akuseŵenzetsa njoka pokamba na Hava

Mngelo wina anapandukila Mulungu. Mngelo woipa ameneyo ni Satana Mdyelekezi.

Satana sanafune kuti Adamu ndi Hava amvele Yehova. Conco anaseŵenzetsa cinjoka kuuza Hava kuti akadya cipatso ca mtengo umenewo, sadzafa, koma adzakhala ngati Mulungu. Ili linali bodza.—Genesis 3:1-5.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani