LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 3 tsa. 14-tsa. 15 pala. 3
  • Adamu na Hava Sanamvele Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Adamu na Hava Sanamvele Mulungu
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Anataila Malo Ao Okhalako
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Umoyo Unali Bwanji m’Paladaiso?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Kuyamba Kwa Umoyo Wovuta
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Munthu Akafa Amayenda Kuti?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 3 tsa. 14-tsa. 15 pala. 3
Adamu na Hava acotsedwa m’munda wa Edeni

PHUNZILO 3

Adamu na Hava Sanamvele Mulungu

Adamu watenga cipatso coletsedwa cimene Hava wam’patsa

Tsiku lina, pamene Hava anali yekha, njoka inakamba naye. Inati: ‘Kodi n’zoona kuti Mulungu anakuletsani kudyako zipatso za m’mitengo yonse?’ Hava anayankha kuti: ‘Tingadye zipatso za m’mitengo yonse kusiyapo mtengo umodzi cabe. Tikadya cipatso ca mu mtengo umenewo, tidzafa.’ Njoka inakamba kuti: ‘Simudzafa iyai. Ndipo mukadya, mudzalingana na Mulungu.’ Kodi zinali zoona? Iyai, inali bodza. Koma Hava anakhulupilila. Anaciyang’anitsitsa cipatso cija, ndipo anayamba kucikhumbila kwambili. Basi anathyola na kudya cipatsoco, na kupatsako Adamu. Adamu anali kudziŵa kuti onse adzafa ngati sadzamvela Mulungu. Koma nayenso anadyako cipatso cija.

Pamene Adamu na Hava atuluka m’munda wa Edeni, angelo na lupanga lamoto akulonda pageti

M’madzulo tsiku limenelo, Yehova anakamba na Adamu na Hava. Anawafunsa cifukwa cake iwo sanamumvele. Hava anapatsa mlandu njoka, naye Adamu anapatsa mlandu Hava. Cifukwa Adamu na Hava sanamvele, Yehova anawacotsa m’munda wa Edeni. Pofuna kuti iwo asabwelelemo, Mulungu anaika angelo na lupanga lamoto lozungulila poloŵela m’mundawo.

Yehova anati uja amene ananamiza Hava, nayeve adzalangiwa. Si njoka yeni-yeni imene inakamba na Hava. Yehova sanapange njoka zimene zinali kukamba. Anali mngelo woipa amene anapangitsa kuti njoka ikambe. Anacita zimenezi kuti anamize Hava. Mngelo ameneyo dzina lake ni Satana Mdyelekezi. Kutsogolo, Yehova adzawononga Satana kuti asakapitilize kunamiza anthu kuti azicita vinthu voipa.

“Mdyelekezi . . . ndi wopha anthu ciyambile kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’coonadi, cifukwa mwa iye mulibe coonadi.”—Yohane 8:44

Mafunso: N’cifukwa ciani Hava anadya cipatso? Nanga n’ciani cinacitikila Adamu na Hava pamene sanamvele Yehova? Kodi Satana Mdyelekezi n’ndani?

Genesis 3:1-24; Yohane 8:44; 1 John 3:8; Chivumbulutso 12:9

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani