GAO 5
Cigumula ca Nowa—Ndani Anamvetsela? Ndani Sanamvetsele?
Anthu ambili m’nthawi ya Nowa anali kucita zoipa. Genesis 6:5
Adamu ndi Hava anabala ana, ndipo anthu anaculuka padziko lapansi. M’kupita kwa nthawi, angelo ena anapanduka ndi kugwilizana ndi Satana.
Iwo anabwela padziko lapansi ndi kuvala matupi a anthu kuti akwatile akazi. Akazi amenewa anabala viŵana vikulu-vikulu vimene vinali vamphamvu ndi voopsa.
Dziko linadzala ndi anthu amene anali kucita zoipa. Baibo imakamba kuti: ‘Kuipa kwa anthu kunaculuka padziko lapansi, ndipo malingalilo onse a m’mitima ya anthu anali oipa okha-okha nthawi zonse.’
Nowa anamvetsela kwa Mulungu ndi kumanga cingalawa. Genesis 6:13, 14, 18, 19, 22
Nowa anali munthu wabwino. Yehova anauza Nowa kuti adzaononga anthu oipa ndi cigumula cacikulu.
Mulungu anauza Nowa kumanga ciboti cacikulu cochedwa cingalawa, ndi kuloŵetsamo banja lake ndi nyama zosiyana-siyana.
Nowa anacenjeza anthu za Cigumula cimene cinali kubwela, koma iwo sanamvele. Ena anam’seka; ena anam’zonda.
Pamene Nowa anatsiliza kumanga cingalawa, analoŵetsamo nyama.