LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 5 tsa. 18-tsa. 19 pala. 5
  • Cingalawa ca Nowa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cingalawa ca Nowa
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Nowa Apanga Cingalawa
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Cigumula ca Nowa—Ndani Anamvetsela? Ndani Sanamvetsele?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Anam’sunga “Pomupulumutsa Pamodzi ndi Anthu Ena 7”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Anthu 8 Anapulumuka na Kulowa m’Dziko Latsopano
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 5 tsa. 18-tsa. 19 pala. 5
Nowa na banja lake amanga cingalawa

PHUNZILO 5

Cingalawa ca Nowa

M’kupita kwa nthawi anthu anaculuka pa dziko lapansi. Koma ambili anali oipa. Ngakhale angelo ena kumwamba anakhala oipa. Iwo anacoka kwawo kumwamba na kubwela pano pa dziko lapansi. Udziŵa cimene anabwelela pa dziko? Kuti adzavale matupi a anthu na kukwatila akazi.

Angelo amenewo anabala ana kwa akazi amene anakwatila. Koma viŵana vawo vinali vamphamvu komanso vankhanza. Vinali kumenya anthu. Koma Yehova sanalekelele vinthu voipa kupitiliza. Conco, anaganiza zowononga anthu oipa na cigumula ca madzi.

Nowa na banja lake apanga cingalawa na kukonza zakudya

Koma munthu wina anali wosiyana. Anali kukonda Yehova. Dzina lake anali Nowa. Anali na mkazi komanso ana aamuna atatu. Maina a ana ake anali Semu, Hamu, na Yafeti. Ndipo aliyense wa ana amenewo anali na mkazi wake. Lomba Yehova anauza Nowa kupanga cingalawa cacikulu, kapena kuti combo, kuti iye pamodzi na banja lake akapulumukilemo pa Cigumula ca madzi. Cingalawa cili monga cibokosi cacikulu coyandama pamadzi. Yehova anauzanso Nowa kuti angenetse vinyama vambili m’combo cimeneco kuti navo vikapulumuke.

Pamenepo Nowa anayamba kupanga combo. Zinawatengela zaka pafupi-fupi 50 kuti Nowa na banja lake atsilize kupanga cingalawa. Iwo anacipanga nde-nde-nde mmene Yehova anawauzila. Pa nthawi imodzi-modzi, Nowa anali kucenjeza anthu za Cigumula ca madzi. Koma palibe amene anamumvelela.

Nthawi tsopano inafika yongena m’cingalawa. Tidzaona zimene zinakonkhapo.

“Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalile.”—Mateyu 24:37

Mafunso: N’cifukwa ciani Yehova anaganiza zobweletsa Cigumula camadzi? Kodi Yehova anapatsa Nowa malangizo abwanji?

Genesis 6:1-22; Mateyu 24:37-41; 2 Petulo 2:5; Yuda 6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani