PHUNZILO 9
Mmene Tingakonzekelele Misonkhano Yathu
Ku Cambodia
Ku Ukraine
Ngati mumaphunzila Baibo ndi Mboni za Yehova, ndiye kuti mumakonzekela phunzilo lililonse. Koma kuti mupindule kwambili, muzicita cimodzi-modzi ndi misonkhano ya mpingo. Cofunika kwambili kuti tikwanitse zimenezi ni kukhala ndi cizoloŵezi cabwino.
Sankhani malo amene muzikonzekelela ndi nthawi yake. Kodi ni nthawi yanji imene simuvutika kumva zimene muŵelenga? Kodi ni m’mawa kwambili musanayambe nchito kapena usiku ana anu atagona? Ngakhale ngati simukwanitsa kuŵelenga nthawi yaitali, sankhani nthawi yocepa imene mungakwanitse, ndipo musalole ciliconse kukusokonezani. Khalani pamalo a zii! opanda congo, ndipo zimani wailesi, TV, ndi foni kuti zisakusokonezeni. Kupemphela musanayambe kukonzekela kudzakuthandizani kucepetsa nkhawa za tsikulo kuti maganizo anu onse akhale pa Mau a Mulungu.—Afilipi 4:6, 7.
Congani mfundo, ndipo konzekelani kukayankhapo. Coyamba, pezani cithunzi ca nkhani yonse. Ganizilani mutu wa nkhani kapena caputala, onani mmene mitu ing’ono-ing’ono ikugwilizanilana ndi mutu wa nkhani, ndipo onani zithunzi-thunzi ndi mafunso obwelelamo amene aonetsa mfundo zazikulu za m’nkhaniyo. Ndiyeno ŵelengani palagilafu iliyonse, ndi kupeza yankho la funso yake. Ŵelengani malemba onse amene sanawagwile mau, ndipo onani kugwilizana kwake ndi nkhani imeneyo. (Machitidwe 17:11) Mukapeza yankho, congani mau angapo ofunika kapena kaciganizo m’palagalafu kamene kadzakukumbutsani yankho. Ndiyeno kumsonkhano, mungaimike dzanja ndi kuyankha mwacidule m’mau anu-anu.
Ngati mukonzekela zimene timaphunzila wiki iliyonse pamisonkhano, mudzaonjezela mfundo zatsopano ‘mosungila cuma’ canu ca cidziŵitso ca m’Baibo.—Mateyu 13:51, 52.
Kodi mufunika kukhala ndi cizoloŵezi canji kuti muzikonzekela misonkhano?
Kodi mungakonzekele bwanji kuti mukayankhepo pamisonkhano?