PHUNZILO 8
Ni Cifukwa Ciani Timavala Bwino Pamisonkhano Yathu?
Ku Iceland
Ku Mexico
Ku Guinea-Bissau
Ku Philippines
Kodi mwaona mapikicha amene ali m’kabuku kano, oonetsa mmene Mboni za Yehova zimavalila bwino pamisonkhano yao? Kodi n’cifukwa ciani timasamala kavalidwe kathu ndi maonekedwe athu?
Timafuna kulemekeza Mulungu wathu. N’zoona kuti Mulungu amaona zambili osati maonekedwe athu cabe. (1 Samueli 16:7) Komabe pamene tisonkhana kuti timulambile, timafuna kulemekeza iye ndi olambila anzathu. Ngati tingakhale ndi mwai wokaonekela kwa pulezidenti, tingasamale maonekedwe athu poganizila udindo wake. Conco, maonekedwe athu pamisonkhano amaonetsa kuti timalemekeza “Woweluza wa dziko lonse lapansi,” Yehova Mulungu, ndi malo athu olambilila.—Genesis 18:25.
Timafuna kuonetsa kuti tili ndi mfundo zimene timatsatila pa umoyo wathu. Baibo imalimbikitsa Akristu kuvala “mwaulemu ndi mwanzelu” monga anthu amene “amalemekeza Mulungu.” (1 Timoteyo 2:9, 10) Kuvala “mwaulemu” kumatanthauza kupewa kavalidwe kodzionetsela, kodzutsa cilako-lako, kapena kuvala zoonetsa thupi. Ndiponso ‘nzelu’ imatithandiza kusankha zovala zabwino osati zotailila kapena za masitaelo onyanya. Mfundo zimenezi zimapatsa munthu ufulu wosankha zovala zosiyana-siyana. Popanda mau, maonekedwe athu abwino ‘angakometsele ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu’ ndi ‘kutamanda Mulungu.’ (Tito 2:10; 1 Petulo 2:12) Kuvala kwathu bwino pamisonkhano kungathandize ena kukhala ndi maganizo oyenela pa kulambila Yehova.
Musalole kuti kavalidwe kanu kakulepheletseni kubwela ku Nyumba ya Ufumu. Kavalidwe koyenela sikatanthauza kuvala zodula kapena za mafasho apamwamba, koma kuvala zaudongo ndi zooneka bwino.
Kodi n’cifukwa ciani kavalidwe kathu polambila Mulungu ni nkhani yaikulu?
Kodi ni mfundo ziti zimene zimatithandiza pa nkhani ya kavalidwe ndi maonekedwe?