LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 7
  • Kodi Misonkhano Yathu Imacitika Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Misonkhano Yathu Imacitika Bwanji?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Misonkhano Yolimbikitsa ‘Cikondi na Nchito Zabwino’
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • N’cifukwa Ciani Tiyenela Kusonkhana?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
Onaninso Zina
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 7

PHUNZILO 7

Kodi Misonkhano Yathu Imacitika Bwanji?

Msonkhano wa Mboni za Yehova ku New Zealand

Ku New Zealand

Msonkhano wa Mboni za Yehova ku Japan

Ku Japan

Mboni yacicepele iwelenga Baibo ku Uganda

Ku Uganda

Mboni ziwili ku Lithuania zicita citsanzo ca ulaliki

Ku Lithuania

Misonkhano ya Akristu oyambilila inali kuphatikizapo kuimba nyimbo, kupemphela, kuŵelenga ndi kukambitsilana Malemba, ndipo sipanali kukhala mwambo wapadela ngakhale umodzi. (1 Akorinto 14:26) Mudzaona zofanana ndi zimenezi mukabwela pamisonkhano yathu.

Malangizo ake amacokela m’Baibo ndipo ni othandiza. Kumapeto kwa wiki, mpingo ulionse umasonkhana kumvetsela nkhani ya m’Baibo ya mamineti 30. Nkhani imeneyi imafotokoza mmene tingagwilitsile nchito Malemba pa umoyo wathu ndi zimene Malemba amanena za nthawi imene tikukhala. Pamene mkambi aŵelenga Malemba, tonse timatsatila m’Mabaibo athu. Nkhani ikatha, pamakhala Phunzilo la “Nsanja ya Olonda” kwa ola limodzi, ndipo onse opezekapo amakhala ndi ufulu woyankhapo pokambitsilana nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yophunzila. Phunzilo limeneli limatithandiza kutsatila malangizo a m’Baibo pa umoyo wathu. Nkhani imeneyi imaphunzilidwa mumipingo yonse yopitilila 110,000 padziko lonse lapansi.

Imatithandiza kuonjezela luso lathu lophunzitsa. Timakhalanso ndi msonkhano wina mkati mwa wiki wa mbali zitatu wochedwa Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhiristu. Pa msonkhanowu, timaphunzila nkhani za mu Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu. Mbali yoyamba ya msonkhanowu, yakuti Cuma Copezeka m’Mau a Mulungu, imatithandiza kumvetsetsa malemba amene abale ndi alongo anaŵelenga asanabwele kudzasonkhana. Mbali yaciŵili ndi yakuti Citani Khama pa Ulaliki, imene imakhala ndi zitsanzo zotithandiza kudziŵa mmene tingafotokozele mfundo za m’Baibo kwa anthu. Pamakhala mlangizi amene amaona mbali zina zimene tifunika kuongolela kuti tiziŵelenga ndi kulankhula mwaluso. (1 Timoteyo 4:13) Pa mbali yotsiliza yakuti Umoyo Wathu Wacikhiristu, timaphunzila mmene tingaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo pa umoyo wathu. Pamakhalanso nkhani ya mafunso ndi mayankho imene imatithandiza kumvetsetsa Baibo.

Mukabwela kumisonkhano yathu, sitikaikila kuti mudzasangalala ndi maphunzilo apamwamba a m’Baibo amene mudzalandila.—Yesaya 54:13.

  • Kodi mudzaphunzila ciani mukabwela pamisonkhano ya Mboni za Yehova?

  • Kodi ndi msonkhano uti umene mungakonde kupezekapo?

DZIŴANI ZAMBILI

Ŵelengani nkhani zimene tidzaphunzila pamisonkhano ingapo yotsatila. Pezani mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni pa umoyo wanu wa tsiku ndi tsiku.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani