LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 7 masa. 59-70
  • Misonkhano Yolimbikitsa ‘Cikondi na Nchito Zabwino’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Misonkhano Yolimbikitsa ‘Cikondi na Nchito Zabwino’
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MISONKHANO YA MPINGO
  • MSONKHANO WA KUMAPETO KWA MLUNGU
  • MSONKHANO WA MKATI MWA MLUNGU
  • KUKUMANA KOKONZEKELA ULALIKI
  • MASONKHANIDWE A MIPINGBO YATSOPANO KAPENA YAING’ONO
  • MISONKHANO YADELA
  • MISONKHANO YACIGAWO
  • MGONELO WA AMBUYE
  • Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Misonkhano Yokonzekela Ulaliki Imene Imakwanilitsa Colinga Cake”
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Njila Zolalikilila Uthenga Wabwino
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Onaninso Zina
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 7 masa. 59-70

MUTU 7

Misonkhano Yolimbikitsa ‘Cikondi na Nchito Zabwino’

KUCOKELA ku zaka za makedzana, anthu a Yehova akhala akucita misonkhano mwadongosolo. M’nthawi ya Aisiraeli, caka ciliconse amuna onse anali kupita ku Yerusalemu kukacita zikondwelelo zitatu zikulu-zikulu. (Deut. 16:16) M’zaka za zana loyamba, Akhristu anali kusonkhana nthawi zonse, kambili m’nyumba za abale. (Filim. 1, 2) Nafenso masiku ano, timasangalala na misonkhano ya mpingo, yadela, komanso yacigawo. Koma n’cifukwa ciani atumiki a Mulungu amasonkhana pamodzi? Cifukwa ni gawo lofunika kwambili pa kulambila kwathu.—Sal. 95:6; Akol. 3:16.

2 Cina, misonkhano imawapindulitsa kwambili aja opezekapo. Ponena za Cikondwelelo ca Misasa m’caka ca seveni ciliconse, Aisiraeli anauzidwa kuti: “Sonkhanitsani anthu, amuna, akazi, ana ndi alendo okhala m’mizinda yanu, kuti amvetsele ndi kuphunzila, pakuti ayenela kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatila mosamala mawu onse a m’cilamulo ici.” (Deut. 31:12) Mwacionekele, cifukwa cacikulu cosonkhanila pamodzi n’cakuti ‘tiphunzitsidwe na Yehova.’ (Yes. 54:13) Misonkhano imatipatsanso mpata wakuti tidziŵane bwino, tilimbikitsidwe, komanso kukhala na mayanjano olimbikitsana wina na mnzake.

MISONKHANO YA MPINGO

3 Ophunzila amene anasonkhana pambuyo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., anapitiliza kumvela zimene atumwi anaphunzitsa, ndipo “tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukacisi mogwilizana.” (Mac. 2:42, 46) M’kupita kwa nthawi, Akhristu posonkhana pamodzi kuti alambile Mulungu, anayamba kuŵelenga Malemba ouzilidwa, ndiponso makalata olembedwa na atumwi komanso ophunzila ena acikhristu. (1 Akor. 1:1, 2; Akol. 4:16; 1 Ates. 1:1; Yak. 1:1) Anali kupelekanso mapemphelo opemphelela mpingo wonse. (Mac. 4:24-29; 20:36) Nthawi zina, amishonale anali kusimba zocitika za mu utumiki wawo. (Mac. 11:5-18; 14:27, 28) Panali kukhalanso kukambilana ziphunzitso za m’Baibo, na kuunikilana maulosi ouzilidwa. Anali kupelekanso malangizo pa makhalidwe ofunika kwa Akhristu. Onse anali kulimbikitsidwa kukhala alengezi okangalika a uthenga wabwino.—Aroma 10:9, 10; 1 Akor. 11:23-26; 15:58; Aef. 5:1-33.

M’masiku otsiliza ovuta ano, kusonkhana nthawi zonse n’kofunika kwambili kuti tizipeza cilimbikitso

4 M’masiku athu ano, misonkhano yacikhristu imacitika motengela citsanzo ca m’nthawi ya atumwi. Timalabadila malangizo ouzilidwa a pa Aheberi 10:24, 25 akuti: “Tiyeni tiganizilane . . . . Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizolowezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” M’masiku otsiliza ovuta ano, tifunikila kwambili cilimbikitso copezeka ku misonkhano. Ngati tisonkhana mokhazikika, tidzakhala Akhristu okhulupilika komanso olimba kuuzimu. (Aroma 1:11, 12) Monga tikudziŵila, tikukhala pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndiponso wokhota-khota. Umoyo wosawopa Mulungu ife tinaufulatila pamodzi na zilakolako za dziko. (Afil. 2:15, 16; Tito 2:12-14) Kunena zoona, n’kutinso kwina kumene tingakonde kukhala, kuposa kuyanjana na anthu a Yehova? (Sal. 84:10) Ndipo n’cianinso cina cingatipindulitse kuposa kuphunzila Mawu a Mulungu na kuwakambilana? Tiyeni lomba tione misonkhano yosiyana-siyana imene inakonzedwa kuti izitipindulitsa.

MSONKHANO WA KUMAPETO KWA MLUNGU

5 Gawo loyamba la msonkhano wa kumapeto kwa mlungu, limakhala nkhani ya m’Baibo. Nkhaniyi amaikonzela anthu onse, ndipo ena a iwo kangakhale koyamba kupezeka pamsonkhano. Nkhani ya anthu onse imathandiza kwambili pa zosoŵa zauzimu za mabwenzi atsopano, komanso za ofalitsa mumpingo.—Mac. 18:4; 19:9, 10.

6 Yesu Khristu, atumwi ake, komanso anthu ena, anali kucita misonkhano ya anthu onse monga imene imacitika m’mipingo ya anthu a Yehova masiku ano. Mosakayika konse, Yesu anali mkambi wa nkhani za onse waluso kuposa wina aliyense padziko lapansi. N’cifukwa cake ena anakamba kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” (Yoh. 7:46) Yesu anali kukamba na ulamulilo, cakuti omumvetsela anali kucita kudabwa. (Mat. 7:28, 29) Anthu amene analabadila zimene Yesu anaphunzitsa anapindula kwabasi. (Mat. 13:16, 17) Atumwi nawonso anatengelako citsanzo kwa Yesu. Pa Machitidwe 2:14-36, timaŵelenga nkhani yamphamvu imene Petulo anakamba pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Anthu ofika masauzande anacitapo kanthu pokhudzika na zimene anamva. M’kupita kwa nthawi, anthu anakhala okhulupilila pambuyo pomvetsela nkhani ya Paulo ku Atene.—Mac. 17:22-34.

7 Masiku anonso, mlungu uliwonse anthu ofika m’mamiliyoni amapindula na nkhani za anthu onse zimene zimakambidwa m’mipingo, pamisonkhano yadela, komanso yacigawo. Nkhani zimenezi zimatikumbutsa ziphunzitso zacikhristu, na kutithandiza kukhalabe olimbikabe m’nchito ya Ufumu. Poitanila anthu acidwi komanso wina aliyense kumisonkhano imeneyi, tingathandize ambili kudziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo.

8 Nkhani za anthu onse zimafotokoza mfundo zosiyana-siyana. Zimafotokoza ziphunzitso za m’Baibo, maulosi, mfundo za m’Baibo, uphungu pa nkhani za umoyo wa banja na cikwati, mavuto omwe acinyamata amakumana nawo, komanso makhalidwe acikhristu. Nkhani zina zimakamba pa cilengedwe ca Yehova codabwitsa. Zina zimafotokoza anthu a m’Baibo amene anapeleka citsanzo cabwino pa nkhani ya kukhulupilika na kulimba mtima, amene tingatengeleko masiku ano.

9 Kuti tipindule ngako na nkhani za anthu onse zimenezi, tiyenela kumvetsela mochela khutu, kupeza malemba amene mlankhuli akuchula, na kum’tsatila pamene aŵelenga na kuwafotokozela. (Luka 8:18) Pamene titsimikizila zimene akutifotokozela, tidzalimbikitsidwa kuzigwilitsila nchito pa umoyo wathu.—1 Ates. 5:21.

10 Ngati akambi alipo okwanila, mpingo udzakhala na nkhani ya anthu onse mlungu uliwonse. Kuwonjezela pa akambi a pampingo, timakhalanso na akambi ocokela ku mipingo ina. Ngati akambi ni ocepekela, nkhanizi zingamakambidwe mmene kungathekele.

11 Gawo laciŵili la msonkhano wa kumapeto kwa mlungu limakhala Phunzilo la Nsanja ya Mlonda. Amakhala makambilano a mafunso na mayankho pa nkhani ya m’magazini yophunzila ya Nsanja ya Mlonda. Kupitila mu Nsanja ya Mlonda, Yehova amatigaŵila cakudya cauzimu ca panthawi yake.

12 Nkhani zophunzila zimenezi, nthawi zambili zimaunika mmene tingaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo pa umoyo wathu wa tsiku na tsiku. Zimathandiza Akhristu kupewa “mzimu wa dziko” na makhalidwe ake onyansa. (1 Akor. 2:12) Nsanja ya Mlonda imatiunikilanso kuwala kwa kamvedwe katsopano ka ziphunzitso za m’Baibo na maulosi ake, kuti tonse tiziyendela pamodzi na coonadi, panjila ya anthu olungama. (Sal. 97:11; Miy. 4:18) Kupezeka pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda na kutengako mbali, kungatipatse ciyembekezo codzakhala m’dziko latsopano lolungama la Yehova. (Aroma 12:12; 2 Pet. 3:13) Mayanjano athu acikhristu amatithandiza kukulitsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala, na kutilimbikitsa kukhalabe okangalika mu utumiki wathu kwa Yehova. (Agal. 5:22, 23) Cikhulupililo cathu cimalimba kuti tizitha kupilila mayeso, na kumanga “maziko abwino a kutsogolo,” kuti tigwile “mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 Tim. 6:19; 1 Pet. 1:6, 7.

13 Kodi tingatengele bwanji mwayi cakudya cauzimu cimeneci? Tizikonzekela phunzilo pasadakhale, patokha kapena monga banja. Tiziŵelenganso malemba osagwila mawu. Popeleka ndemanga tiziyankha m’mawu athu-athu. Pocita izi, coonadi cidzakhomelezeka m’mitima yathu, ndipo ena adzapindula potimvela tikukambapo ndemanga zoonetsa cikhulupililo cathu. Ifenso pomvetsela mwacidwi ku ndemanga za ena, tidzapindula kwambili paphunzilo la mlungu uliwonse.

MSONKHANO WA MKATI MWA MLUNGU

14 Mlungu uliwonse, mpingo umasonkhana pa Nyumba ya Ufumu kuti upindule na pulogilamu yochedwa Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu. Msonkhanowu uli na mbali zitatu zokonzedwa na colinga cotithandiza kukhala “oyenela kugwila nchito” monga atumiki a Mulungu. (2 Akor. 3:5, 6) Ndandanda na nkhani zake zimapezeka mu Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu ka mwezi na mwezi. Kabukuka kamakhalanso na maulaliki acitsanzo ogwilitsila nchito mu ulaliki.

15 Mbali yoyamba ya msonkhano umenewu yochedwa, Cuma Copezeka m’Mawu a Mulungu, imatithandiza kudziŵa nkhani za m’Baibo komanso pamene zinacitika. Timaonanso maphunzilo amene tingatengepo. Mbaliyi imakhala na nkhani yokambidwa, kuŵelenga, komanso makambilano ozikidwa pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu na mlungu. Mu Kabuku ka Umoyo na Utumiki mumakhalanso zithunzi komanso mbali zofuna kulembamo zotithandiza kumvetsa bwino nkhani zake. Kuphunzila Baibo mozama kumeneku kumathandiza aliyense pa umoyo wake, komanso pa luso la kuphunzitsa, kuti ‘tikhale oyenelela bwino ndi okonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.’—2 Tim. 3:16, 17.

16 Mbali yaciŵili ya msonkhano umenewu ni yakuti Citani Khama pa Ulaliki. Imatipatsa mwayi woyeseza maulaliki, na kutithandiza kunola maluso athu pankhani ya kulalikila na kuphunzitsa. Kuwonjezela pa mbali za ana a sukulu, timakambilananso mavidiyo a makambilano acitsanzo. Colinga ca mbali imeneyi n’kutithandiza kukhala na “lilime la anthu ophunzitsidwa bwino” kuti ‘tidziŵe mmene tingamuyankhile bwino munthu wotopa.’—Yes. 50:4.

17 Mbali yacitatu yakuti Umoyo Wathu Wacikhristu, imatithandiza mmene tingaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku. (Sal. 119:105) Cina cofunikanso pacigawo cimeneci ni Phunzilo la Baibo la Mpingo. Makambilano ake amakhala a mafunso na mayankho, muja timacitila Phunzilo la Nsanja ya Mlonda.

18 Mwezi uliwonse Kabuku ka Umoyo na Utumiki kakabwela, mgwilizanitsi wa bungwe la akulu, kapena mkulu wina wom’thandizila, amaona nkhani zimene zilimo, na kuona mosamala amene angakambe nkhanizo, kenaka amapanga ndandanda. Mlungu uliwonse, mkulu wokhoza bwino kuphunzitsa komanso woyenelezedwa na bungwe la akulu kukhala cheyamani, amatsogoza msonkhanowo. Ayenela kuonetsetsa kuti msonkhano ukuyamba na kutha panthawi yake. Amapelekanso cilimbikitso na uphungu wacikondi kwa aja okamba nkhani zawo za m’sukulu.

19 Tikamaukonzekela nthawi zonse Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, kupezekapo na kutengako mbali, timawonjezela cidziŵitso cathu pa Malemba, timamvetsa bwino mfundo za m’Baibo, timakulitsa cidalilo cathu, ndiponso timawonjezela maluso athu panchito yopanga ophunzila. Ngakhale amene akalibe kukhala Mboni zobatizika amapindula na mayanjano abwino, komanso na mfundo zauzimu zolimbikitsa. Potithandiza kukonzekela msonkhano umenewu komanso ina, tingaseŵenzetse Watchtower Library, JW Library®, Watchtower ONLINE LIBRARY™ (ngati zilimo m’cinenelo canu), komanso laibulali ya pa Nyumba ya Ufumu. Laibulali ya pa Nyumba ya Ufumu imakhala na zofalitsa za Mboni za Yehova, Watch Tower Publications Index, kapena Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, ma Baibo ena, dikishonali, na zofalitsa zina zothandiza. Aliyense ali na ufulu woseŵenzetsa laibulali imeneyi misonkhano isanayambe kapena pambuyo pake.

KUKUMANA KOKONZEKELA ULALIKI

20 Panthawi zosiyana-siyana mkati mwa mlungu, na kumapeto kwa mlungu, ofalitsa a m’tumagulu amakumana mwacidule kuti atenge malangizo a ulaliki. Nthawi zambili, kukumana kumeneku kumacitikila m’nyumba za abale, kapena pamalo ena oyenelela, ngakhalenso mu Nyumba ya Ufumu. Kukumana m’tumagulu tung’ono-tung’ono m’malo osiyana-siyana, kumathandiza ofalitsa kusayenda msenga wautali popita ku malo okumanila, komanso ku magawo awo. Amatha kuwagaŵa mwamsanga, basi n’kuloŵa m’gawo mosataya nthawi. Komanso, cimakhala cosavuta kwa woyang’anila kagulu kusamalila a m’kagulu kake. Koma ngakhale kuti kukumana na kagulu kalikonse pakokha kuli na maubwino ake, nthawi zina mikhalidwe ingafune kuti tumagulu tungapo tuzikumana pamodzi. Mwacitsanzo, ngati ni ofalitsa ocepa kwambili amene amapita mu ulaliki mkati mwa mlungu, zingakhale bwino kuphatikiza tumagulu kuti tuzikumana pa Nyumba ya Ufumu, kapena pamalo ena oyenelela. Zikatelo, nthawi zonse ofalitsa adzakhala na wina wolalikila naye. Mpingo ungaonenso kuti n’zothandiza kumakumana pa Nyumba ya Ufumu pa maholide a kudziko. Kapenanso, mpingo ungasankhe kuti tumagulu tonse tuzitengela pamodzi malangizo a ulaliki pambuyo pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda.

21 Ngati kagulu kalikonse kakumana pakokha, woyang’anila kagulu ndiye amatengetsa malangizo a ulaliki. Nthawi zina, woyang’anila kagulu angauze wothandiza wake kapena m’bale wina woyenelela kuti acititse makambilano a ulaliki. Wotengetsa malangizo ayenela kukonzekela mfundo zothandizadi mu ulaliki. Akamaliza kugaŵa ofalitsa, na kuŵauza kokalalikila, m’bale wina wa m’kaguluko amapeleka pemphelo. Kenaka, ofalitsa ayenela kupita ku gawo mosataya nthawi. Makambilano amenewa ayenela kutenga mphindi 5 mpaka 7 cabe. Ndipo ngati acitika pambuyo pa msonkhano wa mpingo, ayenela kukhala ofupikilapo ndithu. Makambilanowo ayenela kukhala olimbikitsa ndiponso othandizadi pa ulaliki kwa ofalitsa. Acatsopano, kapenanso ena amene angafunikile thandizo mu ulaliki, angayende na aciyambakale kuti atengeleko maluso.

MASONKHANIDWE A MIPINGBO YATSOPANO KAPENA YAING’ONO

22 Pamene anthu akupitiliza kubatizika, mipingo nayo imaculukila-culukila. Nthawi zambili, woyang’anila dela ndiye amatumiza fomu yopempha kukhazikitsa mpingo watsopano. Koma nthawi zina, kagulu kangaone kuti zingakhale zothandiza kugwilizana na mpingo wapafupi.

23 Ndipo nthawi zina, mipingo ing’ono-ing’ono ingakhale ya alongo okha-okha. Zikakhala telo, mlongo amene amapemphela mumpingo kapena kucititsa misonkhano, ayenela kuvala cophimba kumutu, mogwilizana na malangizo a m’Malemba. (1 Akor. 11:3-16) Nthawi zambili amacita zimenezi atakhala pansi mopenyana na kagulu. Alongo sacita kuimilila n’kumakamba nkhani ku mpingo ayi. M’malomwake, amaŵelenga nkhaniyo na kupelekapo ndemanga, kapena mwa kuikambilana. Ndipo pofuna kusiyanitsako, alongo angacite coikambilana nkhaniyo, kapena kukonza citsanzo. Ofesi yanthambi idzapempha mmodzi wa alongowo kuti azilembelana naye makalata, na kuti azithandizila kuti misonkhanoyo iziyenda bwino. M’kupita kwa nthawi, abale akayenelela pa udindo, amasamalila mbali zimenezi.

MISONKHANO YADELA

24 Caka ciliconse, makonzedwe amapangidwa akuti mipingo ya m’dela limodzi icite misonkhano iŵili yadela ya tsiku limodzi. Imeneyi imakhala nthawi yosangalatsa imene imapeleka mpata kwa onse opezekapo kuti ‘afutukule mitima yawo’ mwa mayanjano acikhristu. (2 Akor. 6:11-13) Gulu la Yehova limakonza mitu ya misonkhano yocokela m’Malemba na nkhani zake zolekana-lekana, pofuna kukwanilitsa colinga cina cake. Msonkhanowo umaphatikizapo nkhani zokambidwa, zitsanzo, mbali zoonetsa munthu wokamba yekha, komanso mbali zofunsa mafunso. Malangizo apanthawi yake amenewa amakhala olimbikitsa kwa onse opezekapo. Misonkhano yadela imeneyi imapelekanso mwayi kwa acatsopano kuti abatizike, monga cisonyezelo cakuti anadzipatulila kwa Yehova.

MISONKHANO YACIGAWO

25 Kamodzi pacaka, timacitanso misonkhano ikulu-ikulu. Misonkhano yacigawo imeneyi nthawi zambili imakhala ya masiku atatu, yophatikiza mipingo yocokela m’madela angapo. Maofesi a nthambi oyang’anila mipingo yocepekelapo angakoze zakuti mipingo yonse m’gawo lawo izisonkhana pamalo amodzi. M’maiko ena, makonzedwe a misonkhano imeneyi angasinthe malinga na mmene mikhalidwe ilili, kapena cifukwa ca malangizo amene gulu lingapeleke. Nthawi zina, m’maiko ena mumacitika misonkhano ya maiko kapena misonkhano yacigawo yapadela. Ndipo Mboni zofika masauzande zocokela m’maiko osiyana-siyana zimasonkhana pamodzi. Kwa zaka zambili, anthu oculuka amva za uthenga wabwino wa Ufumu cifukwa ca nkhani zofalitsidwa ponena za misonkhano ikulu-ikulu imeneyi ya Mboni za Yehova.

26 Kwa anthu odzipatulila a Yehova, misonkhano yacigawo imakhala nthawi yosangalatsa yolambila Yehova capamodzi. Yakhalanso mipata yabwino younikila kuwala kowonjezeleka kwa coonadi. Pamisonkhano ina yacigawo, pamatulutsidwa zofalitsa zatsopano, zoŵelenga ife eni, zokaphunzila ku mpingo, kapena zogwilitsila nchito mu ulaliki. Pamisonkhano yacigawo pamacitikanso ubatizo. Misonkhanoyi imatilimbikitsa kwambili kupita patsogolo kuuzimu. Imapeleka umboni wakuti anthu a Yehova alidi paubale wa padziko lonse wa Akhristu odzipatulila, amene cikondi ndico cizindikilo cawo monga ophunzila a Yesu Khristu.—Yoh. 13:35.

27 Mwa kusonkhana pamodzi na anthu a Yehova, pamisonkhano ya mpingo, yadela, komanso yacigawo, timalimbikitsidwa kucita cifunilo ca Yehova. Timakhalanso otetezeka ku makhalidwe a dziko amene angawononge cikhulupililo cathu. Misonkhano yonseyi imabweletsa citamando na ulemelelo kwa Yehova. (Sal. 35:18; Miy. 14:28) Ndife oyamikila kuti Yehova wapeleka misonkhano imeneyi, yotsitsimula mwauzimu kwa anthu odzipatulila kwa iye m’nthawi ino ya mapeto.

MGONELO WA AMBUYE

28 Kamodzi pacaka, mipingo ya Mboni za Yehova zungulile dziko lapansi imacita Cikumbutso ca imfa ya Yesu Khristu, kapena kuti Mgonelo wa Ambuye. (1 Akor. 11:20, 23, 24) Kwa anthu a Yehova, uwu ndiwo msonkhano wofunika koposa pacaka. Tinacita kulamulidwa kuti tizicita Cikumbutso cimeneci.—Luka 22:19.

29 Cikumbutso cimacitika patsiku limenenso anali kucita Pasika wochulidwa m’Malemba. (Eks. 12:2, 6; Mat. 26:17, 20, 26) Pasika unali mwambo wa pacaka umene Aisiraeli anali kukumbukila nthawi imene anatuluka mu Iguputo mu 1513 B.C.E. Panthawiyo, Yehova anasankha tsiku la 14 m’mwezi woyamba pa kalenda yoyendela mwezi, lakuti Aisiraeli akadye mwana wa nkhosa wa Pasika, na kutuluka mu ukapolo wawo ku Iguputo. (Eks. 12:1-51) Tsiku limeneli limadziŵika mwa kuŵelenga masiku 13 kucokela pamene mwezi watsopano waonekela ku Yerusalemu, cakumapeto kwa March kapena kumayambililo kwa April. Nthawi zambili, tsiku la Cikumbutso limafika mwezi wonse wathunthu utaonekela.

30 Pa Mateyu 26:26-28, Yesu mwiniwake anafotokoza mmene Cikumbutso ciyenela kucitikila. Si mwambo wokhala na zocitika zodabwitsa kapena kuti madzoma a cikhulupililo ayi. Ni cakudya cabe cophiphilitsa cimene oyenelezedwa okhawo ndiwo amadya na kumwa. Inde, aja amene analandilako maitanidwe okalamulila pamodzi na Yesu Khristu mu Ufumu wakumwamba. (Luka 22:28-30) Koma Akhristu ena onse odzipatulila komanso anthu ena okondwelela, amalimbikitsidwa kupezekapo pa Mgonelo wa Ambuye monga openyelela. Mwa kupezekapo kwawo, amaonetsa kuyamikila cisomo ca Yehova Mulungu potumiza Mwana wake Yesu Khristu, kuti anthu onse akapulumuke. Cikumbutso cisanafike, pamakambidwa nkhani yapadela ya anthu onse, imene colinga cake n’kulimbikitsa anthu kukapezeka pa Cikumbutso, na kuti pambuyo pake akapitilize kuphunzila Baibo.

31 Mboni za Yehovafe, timayembekezela mwacidwi kukakumana pamodzi pamisonkhano kuti ‘tikaganizilane ndi kulimbikitsana pa cikondi ndi nchito zabwino.’ (Aheb. 10:24) Kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amakhala chelu nthawi zonse, kuti akonze misonkhano yosamaliladi zosoŵa zathu zauzimu. Tikulimbikitsa atumiki a Yehova onse komanso okondwelela, kutengela mwayi misonkhano imeneyi, mwa kupezekapo nthawi zonse. Ciyamikilo cawo ca mtima wonse pa zabwino zimene Yehova amawacitila kudzela m’gulu lake, cimamangiliza atumiki a Mulungu kukhala banja lokondana. Koma koposa zonse, timatamanda Yehova Mulungu wathu, na kum’lemekeza.—Sal. 111:1..

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani