Misonkhano Yokonzekela Ulaliki Imene Imakwanilitsa Colinga Cake”
1. Kodi colinga ca misonkhano yokonzekela ulaliki n’ciani?
1 Pa nthawi ina, Yesu anasonkhana ndi ophunzila ake 70 asanapite kukalalikila. (Luka 10:1-11) Iye anawalimbikitsa mwa kuwakumbutsa kuti sadzakhala okha koma adzatsogoleledwa ndi “Mwini zokolola” Yehova. Anawapatsanso malangizo amene anawathandiza kugwila bwino nchito yao ndipo pambuyo pake anawatumiza “aŵiliaŵili.” Lelolino misonkhano yokonzekela ulaliki ilinso ndi colinga cimodzimodzi, cimene ndi kutilimbikitsa, kutiphunzitsa ndi kutikonzekeletsa.
2. Kodi msonkhano wokonzekela ulaliki uyenela kutenga nthawi yaitali bwanji?
2 Msonkhano wokonzekela ulaliki umatenga mphindi 10 kapena 15 zimene zimaphatikizapo kugaŵa gulu, kuchula gawo lokalalikilako, ndi kupemphela. Koma kuyambila mu April, msonkhano wokonzekela ulaliki umenewu uzicitika m’mphindi 5 kapena 7 zokha. Ngakhale n’telo, msonkhano wokonzekela ulaliki ukacitika pambuyo pa misonkhano ya mpingo, uyenela kukhala waufupi kwambili, popeza kuti onse amene apezekapo apindula kale ndi mfundo za m’Malemba. Kufupikitsa nthawi yocita msonkhano wokonzekela ulaliki kudzathandiza onse kuthela nthawi yambili mu ulaliki. Kuonjezela apo, ngati apainiya kapena ofalitsa ena ayamba kulalikila nthawi ya msonkhano wokonzekela ulaliki isanayambe, io ayenela kulekeza ulaliki ndi kupita ku makambilano. Koma wocititsa msonkhanowo asawadyele nthawi.
3. Kodi msonkhano wokonzekela ulaliki uyenela kukonzedwa bwanji kuti ukhale wothandiza kwa ofalitsa?
3 Msonkhano wokonzekela ulaliki uyenela kukonzedwa bwino kuti uzithandiza ofalitsa. M’mipingo yambili, abale amaona kuti ndi bwino kukumana m’tumagulu kuti akonzekele ulaliki m’malo mokumana pamodzi. Kucita zimenezi kumathandiza ofalitsa kufika mofulumila pa msonkhano wokonzekela ulaliki komanso kugawo. Ndipo kumathandiza woyang’anila kagulu kugaŵa abale ndi alongo mosavuta ndiponso kusamalila anthu amene ali m’kagulu kake. Bungwe la akulu lingaone mmene zinthu zilili pampingo ndi kusankha zoyenela kucita. Musanamalize msonkhano ndi pemphelo lacidule, onse afunika kudziŵilatu kumene akalalikile ndi munthu amene ayende naye mu ulaliki.
4. Ncifukwa ciani sitiyenela kuona misonkhano yokonzekela ulaliki ngati yosafunikila poyelekezela ndi misonkhano ina?
4 Misonkhano Yokonzekela Ulaliki ndi Yofunika Mofanana ndi Misonkhano ya Mpingo: Popeza kuti misonkhano yokonzekela ulaliki imacitika n’colinga copindulitsa amene afuna kupita mu ulaliki, si onse mumpingo angapezekepo. Ngakhale zili conco, sitifunika kuona misonkhanoyi ngati yosafunika poyelekezela ndi misonkhano ina ya mpingo. Mofanana ndi misonkhano yonse ya mpingo, misonkhano yokonzekela ulaliki ndi makonzedwe a Yehova amene amatithandiza kulimbikitsana pa cikondi ndi nchito zabwino. (Aheb. 10:24, 25) Conco, wocititsa msonkhanowu ayenela kukonzekela bwino kuti makambilano amenewo alemekeze Yehova ndi kupindulitsa amene apezekapo. Ngati n’kotheka, ofalitsa onse amene afuna kupita mu ulaliki ayenela kuyesetsa kupezakapo.
5. (a) Ndi udindo wotani umene woyang’anila nchito ali nawo popanga makonzedwe a misonkhano yokonzekela ulaliki? (b) Kodi mlongo angacititse bwanji msonkhano wokonzekela ulaliki?
5 Zimene Wocititsa Angakonzekele: Kuti m’bale akacite bwino mbali yake pa msonkhano, ayenela kulandila mbaliyo kukali nthawi. Izi n’zofanana ndi misonkhano yokonzekela ulaliki. Pamene kagulu ka ulaliki kakumana pakokha, woyang’anila kagulu kapena wothandiza wake ndi amene amacititsa msonkhano umenewo. Komabe mpingo ukacitila pamodzi msonkhano wokonzekela ulaliki, woyang’anila nchito angasankhe wina kuti acititse msonkhanowo. Oyang’anila nchito ena amapeleka ndandanda kwa onse amene amatsogoza msonkhanowo ndi kuika ndandanda yofananayo pa bolodi ya zilengezo. Kuti misonkhano yokonzekela ulaliki ikhale yopindulitsa zimadalila luso la kuphunzitsa la wocititsa. Conco woyang’anila nchito ayenela kucita zinthu mwanzelu posankha ocititsa misonkhanoyi. Ngati kulibe mkulu, mtumiki wothandiza, kapena m’bale wina woyenelela amene angacititse msonkhanowu, woyang’anila nchito ayenela kusankha mlongo woyenelela amene ndi wobatizika kuti acititse msonkhanowo.—Onani nkhani yakuti “Zimene Mlongo Angacite Pocititsa Makambilano.”
6. Ncifukwa ciani m’bale wocititsa msonkhano wokonzekela ulaliki ayenela kukonzekela mokwanila?
6 Tikapatsidwa mbali m’Sukulu ya Ulaliki kapena pa Msonkhano wa Nchito, timakonzekela bwino kwambili. Ambili a ife timakonzekela zimene tidzakambe m’nkhani yathu tisanapite ku misonkhano. Mofananamo, mukapatsidwa mbali yocititsa msonkhano wokonzekela ulaliki muyenela kukonzekela mokwanila. Popeza kuti msonkhano wokonzekela ulaliki wafupikitsidwa, kukonzekela bwino ndi kofunika kwambili kuti msonkhanowo ukhale wopindulitsa ndi kuti uzitha pa nthawi yake. Kukonzekela bwino kumaphatikizapo kudziŵilatu gawo limene mukalalikile.
7. Ndi zinthu ziti zimene wotsogoza angasankhe kukambilana pa msonkhano wokonzekela ulaliki?
7 Zimene Mungakambilane: Popeza zocitika m’gawo zimasiyanasiyana, ‘kapolo wokhulupilika’ sanapeleke autilaini ya msonkhano wokonzekela ulaliki. Bokosi lakuti, “Zimene Mungakambilane pa Msonkhano Wokonzekela Ulaliki,” lifotokoza zina mwa zinthu zimene mungakambilane. Mwacionekele, msonkhanowu uyenela kucitika mokambilana. Nthawi zina, msonkhanowo ungaphatikizepo kucita citsanzo cokonzedwa bwino kapena kuonelela vidiyo ya pa jw.org. Pamene wotsogoza akukonzekela kukacititsa msonkhano wokonzekela ulaliki, ayenela kuganizila zimene zingalimbikitse ndi kuthandiza amene akupita mu ulaliki tsiku limenelo.
Pokonzekela msonkhano wokonzekela ulaliki, wocititsa ayenela kuganizila zimene zingalimbikitse ndi kuphunzitsa ofalitsa amene akupita mu ulaliki tsikulo
8. Ndi zinthu zothandiza ziti zimene mungakambilane pa msonkhano wokonzekela ulaliki pa ciŵelu ndi pa sondo?
8 Mwacitsanzo pa ciŵelu, ofalitsa ambili amagaŵila Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! Ambili amene amalalikila pa ciŵelu sapita mu ulaliki mkati mwa mlungu, mwina io sangakumbukile ulaliki wacitsanzo umene anacita pa Kulambila kwao kwa Pabanja. Conco wocititsa msonkhanowu angacite bwino kukambilananso ulaliki wacitsanzo umodzi umene upezeka patsamba lothela la Utumiki Wathu wa Ufumu. Mungakambilanenso mmene mungayambile makambilano pogaŵila magazini kapena poyala maziko a ulendo wobwelelako mwa kugwilitsila nchito nkhani za pa nyuzi, cocitika cinacake, kapena tsiku la holide. Ngati pa msonkhano wokonzekela ulaliki pali ena amene ayamba kale kugaŵila magazini amene tikugaŵila mweziwo, wocititsa msonkhano angawapemphe kuti akambe mwacidule mmene tingagaŵile magaziniwo kapena kufotokoza zocitika zolimbikitsa. Pa sondo, wocititsa angasankhe kukambilana mfundo zogwilizana ndi zofalitsa zimene tikugaŵila mweziwo. Zofalitsa zimene timagwilitsila nchito pophunzila Baibulo ndi anthu, monga kabuku ka Uthenga Wabwino, tumabuku tuŵili twa Mvetselani kwa Mulungu ndi buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa tingazigwilitsile nchito tsiku lililonse. Conco pa msonkhano wokonzekela ulaliki, wotsogoza angacite bwino kukonza zokambilana mwacidule mmene mungagaŵile cimodzi mwa zofalitsa zimenezi.
9. Ndi zinthu zotani zimene mungakambilane pogwila nchito yapadela kumapeto kwa mlungu?
9 Ngati mpingo ukugwila nchito yapadela kumapeto kwa mlungu, wotsogoza angasankhe kukambilana mmene angagaŵile magazini aposacedwapa limodzi ndi kapepala ka ciitano kapena kapepela kauthenga komanso zimene angakambe ngati munthu wina waonetsa cidwi. Njila ina ndi kufotokoza zocitika zabwino pa nchito yapadela imeneyi.
10, 11. Ncifukwa ciani ofalitsa ayenela kukonzekela kuti msonkhano wokonzekela ulaliki uyende bwino?
10 Zimene Ofalitsa Angakonzekele: Ofalitsa naonso ali ndi mbali imene angacite kuti msonkhano wokonzekela ulaliki uyende bwino. Iwo angakonzekele ulaliki kukali nthawi, mwina panthawi ya kulambila kwao kwa pabanja. Kucita zimenezi kudzawathandiza kukhala ndi zinazake zokamba kwa ofalitsa anzao. Kukonzekela bwino kumaphatikizapo kutengelatu magazini ndi zofalitsa zina zogaŵila tisanafike pamsonkhano wokonzekela ulaliki n’colinga cakuti msonkhanowo ukatha, tonse tipite m’gawo mofulumila.
11 Kuonjezela apo, tifunika kufika mofulumila pa msonkhano wokonzekela ulaliki. N’zoona kuti timayesetsa kufika mofulumila pa misonkhano yonse ya mpingo. Komabe, zingakhale zosokoneza kwambili ngati timafika mocedwa pa msonkhano wokonzekela ulaliki. N’cifukwa ciani tikutelo? M’bale amene akucititsa makambilano amaganizila mbali zingapo asanagaŵe gulu. Ngati ofalitsa amene apezeka ndi ocepa, iye angawauze kupita kugawo limene silifoledwa kaŵilikaŵili. Ngati ena ayenda wapansi kupita ku msonkhano wokonzekela ulaliki ndipo gawo lili kutali, wotsogoza angawagaŵe ndi ofalitsa ena amene ali ndi galimoto. Ngati gawo lili ndi malo oopsa, wotsogoza angakonze zoti abale alalikile pafupi ndi alongo kapena angawagaŵe ndi alongowo. Ofalitsa amene ndi odwala kapena olemala angawauze kuti aseŵenzele m’mbali mwa mseu wabwino kapena kugawo limene kulibe nyumba za masitepi ambili. Ofalitsa atsopano angawagaŵe pamodzi ndi ofalitsa ozoloŵela. Koma ngati ofalitsa afika mocedwa, zimacititsa kuti wotsogoza agaŵenso gulu kuti amene afika mocedwa apeze woyenda naye. Nthawi zina tingakhale ndi zifukwa zomveka zofikila mocedwa. Komabe ngati tili ndi cizoloŵezi cocedwa tingadzifunse kuti, ‘kodi ndimacedwa cifukwa cosayamikila msonkhano wokonzekela ulaliki kapena cifukwa colephela kukonzekela kukali nthawi?’
12. Ngati mumakonda kupanga makonzedwe anu oyenda ndi winawake mu ulaliki, kodi mungacite ciani?
12 Ofalitsa amene apezeka pa msonkhano wokonzekela ulaliki angasankhe woyenda naye mu ulaliki msonkhano usanayambe kapena angagaŵilidwe munthu woyenda naye. Ngati mumakonda kupanga makonzedwe anu, mungacite bwino ‘kufutukula mtima wanu’ mwa kuseŵenza ndi ofalitsa osiyanasiyana m’malo molalikila ndi anzanu apamtima nthawi zonse. (2 Akor. 6:11-13) Mungacitenso bwino kupanga makonzedwe akuti mudzaseŵenzele pamodzi ndi wofalitsa watsopano kuti mumuthandize kukulitsa luso la kuphunzitsa. (1 Akor. 10:24; 1 Tim. 4:13, 15) Mvetselani mosamala malangizo amene mungapatsidwe kuphatikizapo malangizo a kumene muyambile kulalikila. Msonkhano ukatha, pewani kusintha woyenda naye ndipo pitani m’gawo mofulumila.
13. Ngati onse akonzekela bwino ndi kucita mbali zao, kodi msonkhano wokonzekela ulaliki umakhala wopindulitsa bwanji?
13 Pambuyo polalikila, ophunzila 70 aja amene Yesu anatumiza “anabwelela ali osangalala.” (Luka 10:17) N’zosakaikitsa kuti msonkhano umene Yesu anacita ndi io asanayambe kulalikila, unawathandiza kulalikila bwino. Mofananamo, lelolino misonkhano yokonzekela ulaliki imatithandiza kwambili. Ngati onse opezekapo akonzekela kucita mbali yao, misonkhano yokonzekela ulaliki imakhala yolimbikitsa, yophunzitsa, ndi yotikonzekeletsa kukwanilitsa udindo wathu wocitila “umboni ku mitundu yonse.”—Mat. 24:14.
Sitifunika kuona misonkhano yokonzekela ulaliki ngati yosafunika poyelekezela ndi misonkhano ina ya mpingo