LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 10/12 masa. 5-6
  • Mmene Mungapindulile ndi Kagulu Kanu ka Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mungapindulile ndi Kagulu Kanu ka Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Zofanana
  • Misonkhano Yokonzekela Ulaliki Imene Imakwanilitsa Colinga Cake”
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
km 10/12 masa. 5-6

Mmene Mungapindulile ndi Kagulu Kanu ka Ulaliki

1. Kodi ndi mapindu anji amene tinali kupeza ku Phunzilo la Buku la Mpingo omwe akalikobe ku tumagulu twa ulaliki?

1 Kodi pali mbali zina za Phunzilo la Buku la Mpingo zimene mukali kuziyewa? Tumaguluto tunali tung’ono-tung’ono ndipo ife tinali kukhala omasukilapo kumeneko. Pa cifukwa ici, kunali kosavuta kupalana ubwenzi ndi abale otilimbikitsa m’cikhulupililo (Miy. 18:24) Woyang’anila phunzilo la buku anali kudziŵa bwino umoyo wa munthu aliyense, moti anali kutha kupeleka cilimbikitso coyenelela aliyense. (Miy. 27:23; 1 Pet. 5:2, 3) Koma ngakhale tsopano, mapindu amenewa akaliko ku tumagulu twa ulaliki.

2. Kodi tingacite bwanji kuti tipalane ubwenzi ndi ena m’kagulu kathu ka ulaliki, amene tingamalimbikitsane nao kuuzimu?

2 Yambani Ndinu Kucitapo Kanthu: Tumagulu twa ulaliki nthawi zambili tumakhala ndi anthu ocepa mofanana ndi mmene tumagulu twa phunzilo la buku tunalili. Tikhozabe kupalana ubwenzi wathithithi ndi abale athu ngati tiyenda nao muulaliki. (Afil. 1:27) Kodi mwagwilako nchito ndi anthu angati m’kagulu kanu? Kodi ‘mungafutukule mtima wanu’ pambali imeneyi? (2 Akor. 6:13) Nthawi zina tikhoza kupempha wina wa m’kagulu kathu kuti adzakhale nafe pa kulambila kwathu kwa pabanja, kapena kumuitanila ku cakudya. M’mipingo ina, tumagulu twa ulaliki tumasinthana kuceleza mlendo wodzakamba nkhani. Pa mlungu wao wocita zimenezo, kaguluko kamasonkhana kumalo amodzi kuti asangalale ndi cakudya ndi maceza olimbikitsana. Amacita zimenezi kaya mlendoyo adzakhala nao kapena ayi.

3. Kodi ku kagulu ka ulaliki kuli mipata yanji imene akulu angacitile ubusa kwa ife?

3 Ngakhale kuti masiku ano mpingo umasonkhana kaŵili kokha pamlungu, sizitanthauza kuti akulu ayenela kucepetsa maulendo aubusa kwa ofalitsa ai. Oyang’anila tumagulu amaikidwa kuti azilimbikitsa ndi kuphunzitsa munthu aliyense payekha-payekha pa nchito yolalikila. Ngati woyang’anila kagulu wanu sanakupempheni kale kuti mukagwile naye nchito muulaliki, bwanji osayamba ndinu kum’pempha? Komanso kamodzi pamwezi, woyang’anila nchito amaloŵa muulaliki ndi kagulu kosiyana kumapeto kwa mlungu. M’mipingo ing’ono-ing’ono yokhala ndi tumagulu toŵelengeka, woyang’anila nchito angakonze zoyendela kagulu kalikonse kaŵili pacaka. Kodi inu mumalinganiza zinthu kuti mukalalikile nao pamene iye adzacezela kagulu kanu?

4. (a) Kodi kukumana kwa ulaliki kuyenela kucitika motani? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kuganizilapo za kutsegula nyumba yathu kuti tizikumanilamo kaamba ka ulaliki?

4 Nthawi zambili zimakhala bwino ngati kagulu kalikonse kamakumana pakokha kaamba ka ulaliki kumapeto kwa mlungu. Kukhala ndi makonzedwe akuti tumagulu tuzikumana m’malo osiyana-siyana panthawi yofananako n’kothandiza kwambili. Ubwino wake ngwakuti ofalitsa amatha kufika mwamsanga pamalopo ndi m’gawo lao lolalikilamo. Komanso kumakhala kosavuta kugaŵa msanga ofalitsa ndi kuti asacedwe kuloŵa m’gawo. Kumakhalanso kosavuta kwa woyang’anila kagulu kusamalila a m’kagulu kake. Komabe, mikhalidwe ina ingafunikilitse kuti tumagulu tuŵili kapena toposelapo tukumane pamodzi. Ngati mpingo wanu umakumana pamodzi kaamba ka ulaliki pa Ciŵelu coyamba ca mwezi, kapena pambuyo pa Phunzilo la Nsanja ya Olonda, ndi bwino kuti musanapeleke pemphelo lomalizila makambilano, woyang’anila kagulu aliyense apatsidwe mpata wakuti akhale pamodzi ndi kagulu kake kuti agaŵane.—Onani kabokosi kakuti “Kodi Mungatsegule Nyumba Yanu?”

5. Ngakhale kuti makonzedwe a Phunzilo la Buku la Mpingo anatha, kodi tiyenela kukhala otsimikiza za ciani?

5 Ngakhale kuti makonzedwe a Phunzilo la Buku la Mpingo anatha, Yehova akupitilizabe kutigaŵila zonse zofunikila kuti ticite cifunilo cake. (Aheb. 13:20, 21) Kwa Yehova sitisoŵa kanthu. (Sal. 23:1) Pali madalitso amene tingapeze ku kagulu kathu ka ulaliki. Ngati ticitapo kanthu ndi ‘kubzala moolowa manja, tidzakololanso zoculuka.’—2 Akor. 9:6.

[Bokosi papeji 6]

Kodi Mungatsegule Nyumba Yanu?

Mipingo ina imaphatikiza pamodzi tumagulu pokonzekela ulaliki cifukwa ca kucepekela kwa nyumba zokumanamo. Kukumana kwa ulaliki ndi mbali ina ya makonzedwe a mpingo. Conco, kukumanaku kukamacitika m’nyumba mwathu ndi mwai wapadela kwambili. Kodi mungatsegule nyumba yanu? Musazengeleze ndi mmene nyumba yanu ilili. Akulu adzaona kumene nyumba yanu ili ndipo adzalingalilanso zinthu zina zimene anali kulingalilapo posankha nyumba zocitilamo phunzilo la buku. Ngati mungafune kupeleka nyumba yanu, dziŵitsani woyang’anila kagulu kanu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani