LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 9 masa. 87-104
  • Njila Zolalikilila Uthenga Wabwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Njila Zolalikilila Uthenga Wabwino
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ULALIKI WA NYUMBA NA NYUMBA
  • KUFUNA-FUNA ANTHU OYENELELA
  • KUPANGA MAULENDO OBWELELAKO
  • KUTSOGOZA MAPHUNZILO A BAIBO A PANYUMBA
  • KUTSOGOLELA ANTHU ACIDWI KU GULU LA YEHOVA
  • KUSEŴENZETSA MABUKU OPHUNZITSILA BAIBO
  • ULALIKI WAMWAYI
  • MAGAWO OLALIKILAMO
  • KULALIKILA ANTHU A ZINENELO ZONSE MOGWILIZANA
  • ULALIKI WA KAGULU
  • Kugwilizana Polalikila M’gawo la Vitundu Vosiyana-siyana
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki —Kufikila Munthu Aliyense m’Gawo Lathu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Munthu Amene Amakamba Cinenelo Cina
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Atumiki a Uthenga Wabwino
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
Onaninso Zina
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 9 masa. 87-104

MUTU 9

Njila Zolalikilila Uthenga Wabwino

YESU POKHALA mlengezi wokangalika wa uthenga wabwino, anapeleka citsanzo kwa otsatila ake. Iye anali kupita kwa anthu, kukawalalikila na kuwaphunzitsa m’nyumba zawo na kumalo alionse kopezeka anthu. (Mat. 9:35; 13:36; Luka 8:1) Yesu analalikila kwa anthu osiyana-siyana, anaphunzitsa ophunzila ake paokha, komanso anaphunzitsa gulu la anthu ofika m’masauzande. (Maliko 4:10-13; 6:35-44; Yoh. 3:2-21) Iye anatengela mwayi mpata uliwonse kuuza anthu mawu olimbikitsa komanso opatsa ciyembekezo. (Luka 4:16-19) Ngakhale pamene anafuna kupumula, sanalekelele mpata uliwonse wolalikila. (Maliko 6:30-34; Yoh. 4:4-34) Poŵelenga nkhani za m’Baibo zofotokoza utumiki wa Yesu, kodi sizitikhudza mtima cakuti timafuna kutengela citsanzo cake? Timafunadi kutelo, monganso anacitila atumwi.—Mat. 4:19, 20; Luka 5:27, 28; Yoh. 1:43-45.

2 Taganizilani mipata imene Akhristu masiku ano ali nayo yotengako mbali m’nchito imene Yesu Khristu anayambitsa zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo.

ULALIKI WA NYUMBA NA NYUMBA

3 Pokhala Mboni za Yehova, timadziŵa kufunika kolalikila uthenga wabwino wa Ufumu ku nyumba na nyumba. Njila imeneyi taiseŵenzetsa kwa nthawi yaitali, moti inacita kukhala cizindikilo cotidziŵila naco. Imeneyi ni njila yabwino kwambili pofikila anthu ambili m’nthawi yocepa. Ndipo zotulukapo zake zabwino zatsimikizila kuti zimenezi n’zoonadi. (Mat. 11:19; 24:14) Ulaliki wa nyumba na nyumba umatipatsa mwayi woonetsa cikondi cathu pa Yehova na mnansi wathu.—Mat. 22:34-40.

4 Kulalikila nyumba na nyumba sikunayambe na Mboni za Yehova za masiku ano ayi. Mtumwi Paulo anakambapo za ulaliki wake wophunzitsa anthu ku nyumba zawo. Pofotokozela akulu a ku Efeso za utumiki wake, iye anati: “Kucokela tsiku loyamba limene ndinaponda m’cigawo ca Asia, . . . sindinakubisileni ciliconse copindulitsa, ndipo sindinaleke kukuphunzitsani . . . kunyumba ndi nyumba.” Mwanjila imeneyi komanso njila zina, Paulo anacitila “umboni mokwanila kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape ndi kutembenukila kwa Mulungu, komanso kuti akhale ndi cikhulupililo mwa Ambuye wathu Yesu.” (Mac. 20:18, 20, 21) Panthawiyo mafumu aciroma anali kulimbikitsa kulambila mafano, ndipo ambili anali ‘kuopa kwambili milungu.’ Koma Paulo anawalimbikitsa kuti afunefune “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu,” amene “akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape.”—Mac. 17:22-31.

5 Masiku ano, nchito yolalikila uthenga wabwino ni yofunika kuicita mmangu-mmangu kuposa na kale lonse. Mapeto a dongosolo loipali akuyandikila mofulumila kwambili. Mwa ici, tifunika tiwonjezele cangu cathu. Njila yosakilila anthu akumva njala ya coonadi, imene yapezeka kuti ndiyo yopambana pa zonse, ni yolalikila nyumba na nyumba. Mphamvu yake yokopa anthu masiku ano, ikali cimodzimodzi monga m’masiku a Yesu na atumwi.—Maliko 13:10.

6 Kodi mumatha kutengako mbali mofikapo m’nchito yolalikila nyumba na nyumba? Ngati mumatelo, dziŵani kuti Yehova amakondwela namwe ngako. (Ezek. 9:11; Mac. 20:35) N’kutheka kuti mwina ulaliki wa nyumba na nyumba ni wovutilako kwa imwe. Mwina pali zolepheletsa zakuthupi, kapena anthu ambili m’gawo lanu alibe nawo cidwi uthenga wabwino. Pangakhalenso ziletso za boma. Kapenanso ndimwe wamanyazi, ndipo mumadodoma kwambili kuti muyambe kukambilana na munthu amene simudziŵana naye. Pa zifukwa zimenezi, mwina mukakhala mu ulaliki wa ku nyumba na nyumba, mumakhala na nkhawa. Koma musataye mtima. (Eks. 4:10-12) Abale oculuka m’madela ambili amakhalanso na zopinga zosiyana-siyana.

7 Yesu analonjeza ophunzila ake kuti: “Dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Lonjezo limeneli limatilimbikitsa kwambili panchito yopanga ophunzila. Timamvela monga mtumwi Paulo amene anakamba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Tengelani mwayi makonzedwe a mpingo a kulalikila nyumba na nyumba. Polalikila pamodzi na ena, mudzalimbikitsidwa komanso kuthandizidwa kwambili. Pemphelani kwa Mulungu kuti akuthandizeni kugonjetsa zopinga zilizonse zimene zingakhalepo, ndipo citani camuna ndithu monga mlaliki wa uthenga wabwino.—1 Yoh. 5:14.

8 Pokambilana na ena za uthenga wabwino, mudzakhala na mipata yowauza za “ciyembekezo cimene muli naco.” (1 Pet. 3:15) Mudzaonadi kusiyana kwa anthu okhala na ciyembekezo ca Ufumu, na aja opanda ciyembekezo. (Yes. 65:13, 14) Mudzakhala na cimwemwe podziŵa kuti mumamvela lamulo la Yesu lakuti “onetsani kuwala.” Mungakhalenso na mwayi wothandiza ena kudziŵa Yehova, na coonadi cotsogolela ku moyo wosatha.—Mat. 5:16; Yoh. 17:3; 1 Tim. 4:16.

9 Makonzedwe amakhalapo okalalikila nyumba na nyumba kumapeto kwa mlungu na mkati mwa mlungu. M’madela amene n’kovuta kupeza anthu panyumba kum’maŵa, mipingo ina imakonza ulaliki wa kumadzulo. Anthu ena amamasukilapo kulandila alendo masana kapena kumadzulo, kusiyana na kum’maŵa.

KUFUNA-FUNA ANTHU OYENELELA

10 Yesu analangiza ophunzila ake ‘kufufuza’ anthu oyenelela. (Mat. 10:11) Iye anali kusakila anthu a maganizo abwino m’njila zambili, osati cabe ku nyumba na nyumba. Inde, anali kulalikila pa mpata uliwonse wopezeka, mwa ulaliki wocita kukonzedwa kapena wamwayi. (Luka 8:1; Yoh. 4:7-15) Atumwi nawonso anacitila umboni kwa anthu m’malo olekana-lekana.—Mac. 17:17; 28:16, 23, 30, 31.

Colinga cathu ni kufikila munthu aliyense na uthenga wa Ufumu

11 Masiku anonso, colinga cathu ni kufikila aliyense na uthenga wa Ufumu. Izi zitanthauza kutengela citsanzo ca Yesu na atumwi ake mmene anagwilila nchito yopanga ophunzila, komanso mogwilizana na kusintha kwa zinthu m’dzikoli, na kuonanso mmene mikhalidwe ilili pa umoyo wa anthu m’gawo lathu. (1 Akor. 7:31) Mwacitsanzo, ofalitsa aona kuti n’zothandiza ngako kulalikila anthu m’malo a malonda. M’maiko ambili, ulaliki wa mumsewu umayenda bwino kwabasi, monga kulalikila m’mapaki, m’malo oika mamotoka, kapena kulikonse kopezeka anthu. Mipingo ina ili na mathebulo na tumasitandi twa ulaliki. Pamwamba pa izi, ofesi ya nthambi nthawi zina imakonza ulaliki wapoyela wapadela m’mizinda ikulu-ikulu, maka-maka m’malo odutsilapo anthu ambili. Ofalitsa otengako mbali amasankhidwa m’mipingo yosiyana-siyana. Mwa ici, anthu amene sapezeka ku nyumba zawo angalandile uthenga m’malo ngati amenewa.

12 Tikakumana na munthu m’malo otelo, ndipo waonetsa cidwi pa uthenga wa m’Baibo, tingam’patse cofalitsa coyenelela. Kuti tikulitse cidwi cake, tingam’patse nambala yathu ya foni na kupangana naye kuti tikacezenso naye, monga ulendo wobwelelako. Apo ayi, tingamuuze kuti akapite pawebusaiti ya jw.org, kapenanso kum’fotokozela kumene mpingo wakufupi na kwawo umacitila misonkhano. Mudzapeza kuti ulaliki wapoyela umenewu umasangalatsa zedi, ndipo ni njila yabwino yowonjezela utumiki wanu.

13 Komabe, nchito yathu monga Akhristu si kulengeza uthenga wabwino cabe ayi. Palinso mbali ina. Kuti muthandizedi anthu kulandila coonadi cotsogolela ku moyo wosatha, muyenela kupanga maulendo obwelelako ambili mpaka akapite patsogolo n’kukhala Akhristu ofikapo.

KUPANGA MAULENDO OBWELELAKO

14 Yesu anauza otsatila ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Koma anawauzanso kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.” (Mat. 28:19, 20) Kupanga maulendo obwelelako kungamatipatse cimwemwe mu utumiki wathu kwa Yehova. Aja omwe anaonetsa cidwi mutawafikila ulendo woyamba amasangalala ngako mukapitanso kukaceza nawo. Powafotokozela mfundo zowonjezeleka za m’Baibo, mungalimbitse cikhulupililo cawo mwa Mulungu na kuwathandiza kuzindikila zosoŵa zawo zauzimu. (Mat. 5:3) Ngati mwaukonzekela bwino ulendo wobwelelako na kupitako panthawi yowakomela, mungathe kuwayambitsa phunzilo la Baibo la panyumba. Muzikhala na colinga cimeneci popanga maulendo obwelelako. Inde, sitimangobyala mbewu za coonadi basi n’kucokapo ayi, timakathilila.—1 Akor. 3:6.

15 N’zoona kuti kwa ena maulendo obwelelako ingakhale nkhani yovutilako. Mwina mumacita bwino kwambili kulalikila mwacidule pa ulendo woyamba, ndipo mumaukonda ulaliki umenewu. Koma mukaganizila zobwelelako kuti mukakambilane na mwininyumba za m’Baibo, mwina mumadodoma kwambili. Koma mankhwala ake ni kukonzekela bwino basi. Gwilitsilani nchito malangizo amene timalandila pamsonkhano wa mkati mwa mlungu. Mungapemphenso wofalitsa wokhoza bwino kuti mukapite naye.

KUTSOGOZA MAPHUNZILO A BAIBO A PANYUMBA

16 Pokamba na munthu wotembenukila ku Ciyuda amene anali kuŵelenga Mawu a Mulungu, mlengezi Filipo anamufunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwelengazo?” Munthuyo poyankha anati: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulila?” Machitidwe caputala 8, imatiuza kuti Filipo anayambila makambilano ake pa Lemba limene munthuyo anali kuŵelenga, ndipo ‘anamuuza uthenga wabwino wonena za Yesu.’ (Mac. 8:26-36) Sitidziŵa kuti Filipo anakambilana na munthuyo kwa utali wotani, koma Filipo anafotokoza uthenga wabwino momveka bwino, cakuti munthuyo anakhulupilila, moti anapempha kuti abatizike. Inde, panthawi yomweyo anakhala wophunzila wa Yesu Khristu.

17 Alipo anthu ena masiku ano amene Baibo saidziŵa bwino. Conco, kuti akafike pokhala na cikhulupililo colimba na kuyenelela ubatizo, pangafunikile maulendo obwelelako ambili-mbili, na kuphunzila nawo mowafika pamtima kwa milungu, miyezi, ngakhale caka kapena koposelapo. Koma kuleza mtima kwanu pothandiza anthu oona mtima kuti akhale ophunzila, kuli na madalitso ake, monga anakambila Yesu kuti: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Mac. 20:35.

18 Potsogoza phunzilo la Baibo la panyumba, seŵenzetsani cofalitsa cimene cinakonzedwela kuyambitsa maphunzilo. Gwilitsilani nchito malangizo omwe timalandila pamsonkhano wa mkati mwa mlungu, komanso muzilalikilako na aphunzitsi amaluso mumpingo. Mukatelo, muzitsogoza maphunzilo a Baibo opita patsogolo, powathandiza kukhala ophunzila a Yesu Khristu.

19 Ngati mufuna wokuthandizani moyambitsila phunzilo la Baibo komanso molitsogozela, masukani kukambilana na mmodzi wa akulu kapena wofalitsa mnzanu amene amakhoza bwino kutsogoza maphunzilo a Baibo a panyumba. Mungapezenso thandizo pa malangizo a mu Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, amene timaona zitsanzo zake pamsonkhano umenewu. Dalilani Yehova, ndipo muchulileni cokhumba canu m’mapemphelo anu. (1 Yoh. 3:22) Conco ngati n’kotheka, khalani na colinga comatsogozako phunzilo la Baibo la panyumba, kuwonjezela pa maphunzilo amene mungamatsogoze pabanja panu. Mwa kutsogoza maphunzilo a Baibo, mudzawilikiza cimwemwe pa utumiki wanu.

KUTSOGOLELA ANTHU ACIDWI KU GULU LA YEHOVA

20 Tikathandiza anthu kum’dziŵa Yehova Mulungu na kukhala ophunzila a Yesu Khristu, iwo amakhala ziwalo za mpingo. Maphunzilo a Baibo angapite patsogolo na kukhala okhwima kuuzimu ngati afika polidziŵa bwino gulu la Yehova na kugwilizana nalo. Ni udindo wanu kuwaphunzitsa zimenezo. Mavidiyo na bulosha yakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? zinapangidwa na colinga cimeneci. Mfundo zina za mu Mutu 4 m’bulosha imeneyi zingakhalenso zothandiza.

21 Mukangoyamba kuphunzila Baibo na munthu, m’thandizeni kuona kuti Yehova ali na gulu limene amaseŵenzetsa pofuna kuti nchito yolalikila icitike padziko lapansi masiku ano. M’thandizeni kuona phindu la zofalitsa zathu zothandiza kuphunzilila Baibo, na kumufotokozela mmene amazilembela na kuzitumiza padziko lonse. Muunikileni kuti amene amagwila nchito zonsezi ni anchito ongodzipeleka popanda malipilo, odzipatulila kwa Mulungu. M’pempheni wophunzila Baibo wanu kuti mukapite naye ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Mufotokozeleni mmene misonkhano imacitikila, ndipo mudziŵikitseni kwa anzanu kumeneko. Mukamuthandizenso kudziŵana na Mboni za Yehova zina pamisonkhano yadela komanso yacigawo. Pa zocitika zimenezi na zina, wophunzila Baibo wanu adzadzionela yekha mmene anthu a Yehova amaonetsela cikondi, cimene ndiye cizindikilo cathu monga Akhristu. (Yoh. 13:35) Pamene munthu wacidwi apitiliza kukonda gulu la Yehova, amayandikila kwa Yehova.

KUSEŴENZETSA MABUKU OPHUNZITSILA BAIBO

22 Akhristu a m’nthawi ya atumwi, anali ofalitsa Mawu a Mulungu okangalika. Iwo anakopolola Malemba kuti aziwaseŵenzetsa paokha, komanso pophunzila mumpingo. Anali kulimbikitsanso ena kuti aziŵelenga Mawu a Mulungu a coonadi. Mipukutu ya Malemba inali yocepa panthawiyo, moti inali yamtengo wapatali kwambili. (Akol. 4:16; 2 Tim. 2:15; 3:14-17; 4:13; 1 Pet. 1:1) Masiku ano, Mboni za Yehova zimaseŵenzetsa njila zamakono zopulintila mabuku. Mwa ici, amapanga ma Baibo na mabuku ophunzitsila Baibo ofika m’mamiliyoni ambili-mbili. Mabukuwo amaphatikizapo mathirakiti, mabulosha, mabuku, na magazini m’zinenelo zambili.

23 Pamene muuzako ena uthenga wabwino, yesetsani kuseŵenzetsa zofalitsa za gulu la Yehova zothandizila kuphunzila Baibo. Kuona mmene mwapindulila poŵelenga na kuphunzila zofalitsa za Mboni za Yehova, kudzakulimbikitsani kuti muzigaŵilako ena zofalitsazo.—Aheb. 13:15, 16.

24 Anthu ambili masiku ano amaseŵenzetsa Intaneti pofuna kudziŵa zinthu. Conco, kuwonjezela pa mabuku ophunzitsa Baibo, webusaiti yathu ya jw.org ni cida cothandiza kwambili cofalitsila uthenga wabwino. Anthu padziko lonse lapansi angaseŵenzetse kompyuta kuŵelenga kapena kumvetsela Baibo, mabuku, na zofalitsa zina m’zinenelo zofika mahandiledi. Aja amene amaopa kukambilana nafe, kapena okhala kumalo amene n’zovuta kukamba na Mboni za Yehova, amatha kuloŵa pa jw.org ali kunyumba kwawo, na kudziŵelengela okha zimene timakhulupilila.

25 Ndiye cifukwa cake timafuna kudziŵitsa anthu ambili za webusaiti yathu ya jw.org. Ngati mwininyumba wafunsa zokhudza cikhulupililo cathu, tingaseŵenzetse foni kapena tabuleti na kumuonetsa yankho panthawi yomweyo. Tikapeza munthu wokamba cinenelo cina, kuphatikizapo cinenelo camanja, tingamuuze kupita pawebusaiti yathu kuti apeze Baibo kapena mabuku ophunzitsa Baibo m’citundu cake. Ofalitsa ambili ayambitsa makambilano a m’Baibo poseŵenzetsa mavidiyo a pawebusaiti.

ULALIKI WAMWAYI

26 Kwa amene anali kumvetsela mosamala mawu ake, Yesu anati: “Inu ndinu kuwala kwa dziko. . . . Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mat. 5:14-16) Ophunzila amenewo anaonetsa njila za Mulungu mwa kutengela citsanzo ca Yesu, amene anakamba kuti: “Ine ndine kuwala kwa dziko.” Yesu anapeleka citsanzo kwa Akhristu, cifukwa anali kuonetsa “kuwala kwa moyo, kuti apindulitse onse omvetsela.—Yoh. 8:12.

27 Mtumwi Paulo nayenso anatisiila citsanzo cabwino cakuti titsatile. (1 Akor. 4:16; 11:1) Ali ku Atene, analalikila tsiku lililonse kwa anthu amene anawapeza kumsika. (Mac. 17:17) Akhristu a ku Filipi anatsatila citsanzo cake. Mwa ici, Paulo anawalembela kuti anali kukhala “pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota,” koma iwo anali ‘kuwala pakati pawo monga zounikila m’dzikoli.’ (Afil. 2:15) Nafenso masiku ano, tingaonetse kuwala kwa coonadi m’mawu na zocita zathu paliponse papezekela mpata wouzako ena uthenga wabwino. N’zoona kuti citsanzo cathu monga anthu oona mtima, komanso a makhalidwe abwino, cimaonetsa kuti ndife osiyana kwambili na dzikoli. Koma ngati tikamba nawo anthu za uthenga wabwino, m’pamene amadziŵa cifukwa cake tili osiyana nalo dzikoli.

28 Monga anthu a Yehova, timalengeza uthenga wabwino kwa anthu kunchito, kusukulu, m’zoyendela za anthu onse, kapena kwina kulikonse. Tikakhala paulendo, tingakhale na mwayi wokambilana na amene tili nawo paulendowo. Aliyense wa ife ayenela kukhala chelu kupezelapo mwayi pamakambilano kuti tiloŵetsepo ulaliki. Tizikhala okonzeka kulalikila kwa ena pa mpata uliwonse woyenelela.

29 Tidzacita khama kulalikila kwa anthu ngati tikumbukila kuti kumabweletsa citamando kwa Mlengi wathu na kulemekeza dzina lake. Ndiponso, tingathandize anthu oona mtima kudziŵa Yehova kuti nawonso akam’tumikile na ciyembekezo ca moyo pokhulupilila mwa Yesu Khristu. Utumiki umenewu Yehova amakondwela nawo zedi, ndipo ni wopatulika m’maso mwake.—Aheb. 12:28; Chiv. 7:9, 10.

MAGAWO OLALIKILAMO

30 Cifunilo ca Yehova n’cakuti uthenga wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse, m’matauni komanso m’madela a kumidzi. Mwa ici, mipingo komanso anthu otumikila kumadela akutali, amalandila magawo olalikilamo kucokela ku ofesi ya nthambi. (1 Akor. 14:40) Ndiwo makonzedwe amene Mulungu anakhazikitsa ngakhale m’zaka za zana loyamba. (2 Akor. 10:13; Agal. 2:9) Cifukwa ca kuwonjezeka kwa nchito yolengeza za Ufumu m’masiku ano otsiliza, zambili zimakwanilitsidwa ngati mpingo uli na makonzedwe abwino ofolela gawo lawo.

31 Woyang’anila utumiki ndiye amayang’anila makonzedwe amenewa. Koma mtumiki wa magawo ndiye amagaŵila magawo kwa ofalitsa. Pali mitundu iŵili ya magawo. Pali magawo a tumagulu na magawo aumwini. Ngati gawo la mpingo ni locepa, woyang’anila kagulu aliyense amapatsidwa gawo la kagulu mmene ofalitsa a m’kagulu kake amalalikilamo. Koma ngati mpingo uli na gawo lalikulu, wofalitsa aliyense angapatsidwe gawo laumwini.

32 Ubwino wokhala na gawo laumwini ni wakuti wofalitsa amakhalabe na kokalalikila ngakhale m’masiku amene kulibe kukumana kotenga malangizo a ulaliki, kapena pamene n’zosatheka kukakumana pamodzi na kagulu kake. Mwacitsanzo, ofalitsa ena angatenge gawo lakufupi na kunchito kwawo, ndipo amakwanitsa kulalikila m’gawolo panthawi yopumula kapena akakomboka kunchito. Mabanja ena amapempha gawo lakufupi na kumene akhala kuti azitha kukalalikila madzulo. Kukhala na gawo laumwini lakufupi, kumathandiza wofalitsa kuthela nthawi yoculuka mu ulaliki m’malo moyenda msenga wautali. Komanso dziŵani kuti m’gawo laumwini timatha kucitilamonso ulaliki wa kagulu. Ngati mufuna kukhala na gawo lanu laumwini, pemphani kwa mtumiki wa magawo.

33 Kaya likhale gawo la kagulu lopelekedwa kwa woyang’anila kagulu, kapena gawo laumwini lopelekedwa kwa wofalitsa, amene wapatsidwa gawoyo ayenela kuonetsetsa kuti nyumba iliyonse yafikilidwa m’gawolo. Koma magawo amenewo azifoledwa mogwilizana na malamulo oteteza cinsinsi ca anthu ena. Woyang’anila kagulu aliyense kapena wofalitsa amene watengako gawo, ayenela kuyesetsa kulitsiliza m’miyezi 4. Akalimaliza, ayenela kudziŵitsa mtumiki wa magawo. Malinga na mmene zinthu zinayendela, woyang’anila kagulu kapena wofalitsa angafune kupitiliza kulalikila m’gawolo, kapena angalibweze kwa mtumiki wa magawo.

34 Ngati onse mumpingo atsatila malangizo amenewa, gawo lonse la mpingo lingafoledwe mokwanila. Tingapewenso vuto lakuti ofalitsa aŵili kapena angapo n’kumalalikila makomo amodzi-modzi, zimene zingakhumudwitse anthu m’gawolo. Tikapewa kucita izi, tidzaonetsa kuwaganizila ofalitsa anzathu, komanso anthu a m’gawo lathu.

KULALIKILA ANTHU A ZINENELO ZONSE MOGWILIZANA

35 Munthu aliyense afunika kuphunzila za Yehova Mulungu, Mwana wake, na Ufumu wake. (Chiv. 14:6, 7) Tiyenela kuthandiza anthu a zinenelo zosiyana-siyana kuti aitanile pa dzina la Yehova, akhale na makhalidwe acikhristu, na kuti akapulumuke. (Aroma 10:12, 13; Akol. 3:10, 11) Kodi pamakhala zovuta zotani polalikila uthenga wabwino m’madela a zilankhulo zosiyana-siyana? Tingacite motani kuti tizilalikila kwa anthu otelo a m’delalo kuti amve uthenga wa Ufumu m’citundu cimene amamvetsetsa bwino?—Aroma 10:14.

36 Mpingo umapatsidwa gawo malinga na citundu ca mpingowo. Conco, m’madela amene anthu amakamba zinenelo zosiyana-siyana, ofalitsa a mipingo yosiyana-siyana amalalikila m’gawo limodzi. Zikakhala conco, ni bwino kuti ofalitsa a mpingo uliwonse azilalikila cabe kwa anthu a citundu ca mpingo wawo. Ni mmenenso ziyenela kucitikila pamakampeni acimemezo. Koma pocita ulaliki wapoyela kapena ulaliki wamwayi, ofalitsa angalalikile kwa aliyense na kugaŵila zofalitsa m’citundu ciliconse.

37 Nthawi zina, mipingo ya zinenelo zina ingamalephele kufola kaŵili-kaŵili magawo awo akutali. Zikakhala telo, oyang’anila utumiki a mipingoyo angakambilane kuti apange makonzedwe omakalalikila ku gawolo. Izi zingapatse mwayi aliyense m’gawolo wa kumva uthenga wa Ufumu. Zingapewetsenso kumakalalikila mmene anzathu alalikilamo kale.—Miy. 15:22.

38 Kodi tiyenela kucita ciani ngati pakhomo tapezapo munthu wokamba cinenelo cisali ca mpingo wathu? Tisangomusiya poganiza kuti ofalitsa a citundu cake adzam’lalikila. Ofalitsa ena aphunzila maulaliki osavuta acidule m’zilankhulo zimene amapeza kaŵili-kaŵili m’gawo lawo. Tingamuonetse munthuyo mmene angaŵelengele kapena kucita daunilodi mabuku pawebusaiti yathu ya jw.org. Apo ayi, tingam’lonjeze kuti tidzam’bweletsela mabuku a m’citundu cake.

39 Ngati munthuyo waonetsa cidwi ceni-ceni, tiyesetse kupeza wofalitsa amene angam’thandize m’citundu cimene amvetsetsa bwino. Tingamuuzenso za kufupiko na kumene kumacitika misonkhano m’citundu cake. Ngati afuna kuti aziphunzila naye m’citundu cake, tingamuonetse molembela dzina lake komanso nambala yake ya foni pa jw.org kuti wina akamutumile foni. Ndiyeno ofesi ya nthambi idzayesetsa kupeza wofalitsa amene ali kufupi na munthuyo, kapena kagulu, kapenanso mpingo umene ungapitilize kum’thandiza.

40 Tipitilize kum’thandiza munthuyo mpaka atapezeka wina wokamba citundu cake amene angapitilize kuthandizana naye. Nthawi zina, ofesi ya nthambi ingadziŵitse akulu kuti kumene munthu wacidwiyo akukhala sikunapezeke amene angam’thandize m’citundu cake. Zikakhala telo, ife tiyeni tipitilize kuthandiza munthuyo kuti cidwi cake cipite patsogolo ndithu. Ngati n’kotheka, tingayambe kuphunzila naye Baibo, mwina m’cofalitsa ca m’cinenelo cake. Ngati tiseŵenzetsa bwino zithunzi, pamene munthuyo akuŵelenga malemba osagwila mawu m’cofalitsaco, akhoza kumatolapo mfundo zikulu-zikulu. Mwina wina wa m’banjamo wodziŵa bwino citunduco angamathandizile kumasulila.

41 Kuti titsogolele munthu wacidwi ku gulu la Mulungu, tiyenela kumuitanila ku misonkhano yathu, ngakhale kuti sangamvetse ndondomeko yonse ya msonkhano. Poŵelenga Baibo, tingam’thandize kupeza malemba m’Baibo ya m’citundu cake ngati ilipo. Nakonso kuceza na abale kapena alongo mumpingo kungam’limbikitse, ndipo kungam’thandize kuti apite patsogolo kuuzimu.

42 Kagulu koyesela: Kagulu koyesela kamapangidwa na kagulu ka ofalitsa amene amalalikila m’citundu cina cosiyana na citundu ca mpingo wawo, ngakhale kuti alibe mkulu kapena mtumiki wothandiza amene angamacititse misonkhano ya mlungu na mlungu m’cinenelo cimeneco. Ofesi ya nthambi ingavomeleze mpingo kuyambitsa kagulu koyesela ngati pali ziyenelezo izi:

  1. (1) Pakhale anthu ambiliko ndithu m’gawo amene amakamba cinenelo cinaco, osati ca mpingowo.

  2. (2) Pakhale ofalitsa angapo odziŵa cineneloco, kapena okonzeka kuciphunzila.

  3. (3) Bungwe la akulu likhale lokonzeka kumalinganiza na kuyang’anila makonzedwe a ulaliki m’citundu cimeneco.

Ngati bungwe la akulu lifuna kuyambitsa kagulu koyesela ka citundu cina, akulu ayenela kufunsila kwa woyang’anila dela. Iye mwina akudziŵanso za mipingo ina imene imayesetsa kulalikila anthu a citundu cimeneco, ndipo angapeleke cithunzi cabwino pofuna kuona kuti ni mpingo uti uli pamalo abwino okhazikitsa kagulu kameneko. Mpingowo ukasankhidwa, akulu adzalemba kalata ku ofesi ya nthambi yopempha cilolezo coyambitsa kagulu koyesela.

43 Kagulu: Ofesi ya nthambi ingavomeleze mpingo kukhazikitsa kagulu ngati pali ziyenelezo izi:

  1. (1) Pakhale umboni wakuti anthu acidwi akupezeka m’gawo la cineneloco, ndipo pali kuthekela kwa ciwonjezeko.

  2. (2) Pakhale kagulu ka ofalitsa ocidziŵa cineneloco, kapena amene akuciphunzila.

  3. (3) Pali mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenelezedwa amene angamacititseko msonkhano umodzi pamlungu, kapena mbali imodzi ya msonkhano wa pamlungu, monga nkhani ya anthu onse kapena Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, m’citundu cimeneco.

Ngati ziyenelezo zimenezi zifikilidwa pa mlingo wokhutilitsa, bungwe la akulu lidzalemba kalata ku ofesi ya nthambi, kupempha cilolezo cokhazikitsa kagulu. Mkulu amene wasankhidwa kutsogolela kaguluko azichedwa “woyang’anila kagulu.” Ngati ni mtumiki wothandiza, azichedwa “mtumiki wa kagulu.”

44 Kagulu kakakhazikitsidwa, bungwe la akulu la mpingo woyang’anila kaguluko liyenela kuona kuti ni mbali ziti za misonkhano ya mpingo zimene zingawonjezeledwe ku kaguluko, komanso kuti zizicitika kangati pamwezi. Pakhalenso makonzedwe a kukumana kotenga malangizo a ulaliki. Onse a m’kaguluko ali pansi pa uyang’anilo wa bungwe la akulu la mpingowo. Akulu adzapeleka citsogozo coyenelela na kuona zimene angacite posamalila zofunikila za kaguluko. Woyang’anila dela akaseŵenzanso pamodzi na kaguluko pocezela mpingo, adzatumiza lipoti lacidule ku ofesi ya nthambi lofotokoza za mmene kaguluko kakucitila, na kuchulanso zosoŵa za kaguluko. M’kupita kwa nthawi, zingatheke kaguluko kudzakhala mpingo. Ngati onse oloŵetsedwamo atsatila malangizo a gulu la Mulungu, Yehova amakondwela kwambili.—1 Akor. 1:10; 3:5, 6.

ULALIKI WA KAGULU

45 Mkhristu wodzipatulila aliyense ali na udindo wouzako ena uthenga wabwino. Pali njila zambili zocitila zimenezi. Koma tonsefe timakondwela kupita na ofalitsa anzathu mu utumiki wakumunda. (Luka 10:1) Pa cifukwa cimeneci, ofalitsa m’mipingo amakumana kuti atenge malangizo a ulaliki, kumapeto kwa mlungu kapena mkati mwa mlungu. Maholide nawonso amapeleka mpata wabwino wocita ulaliki wa kagulu, cifukwa abale ambili sapita kunchito. Komiti ya Utumiki ya Mpingo ndiyo imalinganiza makonzedwe okumana kaamba ka utumiki wakumunda, panthawi na malo oyenelela masana kapena madzulo.

46 Ulaliki wa kagulu umapeleka mwayi kwa ofalitsa kuti aseŵenzele pamodzi na ‘kulimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Ofalitsa acatsopano angakhale na mwayi wolalikila pamodzi na aciyambakale kuti aphunzileko maluso. M’madela ena, cingakhale cinthu canzelu ofalitsa aŵili kapena oposelapo kuyendela pamodzi pa zifukwa za citetezo. Ngakhale ngati mungafune kuyenda mwekha m’gawo, kuyamba mwakumana monga kagulu kumatipatsa cilimbikitso capadela. Kungodziŵa cabe kuti enanso akulalikila m’gawolo, kumatipatsa cidalilo cabwino. Apainiya komanso ofalitsa ena sayenela kukhala okakamizika kupezeka pa kukumana kulikonseko kotenga malangizo a utumiki wakumunda wolinganizidwa na mpingo, maka-maka ngati kukumanako kumacitika tsiku na tsiku. Koma mlungu uliwonse ayenela kupezekapo ndithu pa kukumana kwina kotenga malangizo a ulaliki.

47 Tiyeni tonse titengele citsanzo ca Yesu na atumwi ake! Dziŵani ndithu kuti Yehova adzadalitsa khama lathu lotengako mbali mokwanila pa nchito yofunika koposa imeneyi, yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu.—Luka 9:57-62.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani