UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki —Kufikila Munthu Aliyense m’Gawo Lathu
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Zekariya analosela kuti anthu a zinenelo zosiyana-siyana adzalandila uthenga wabwino. (Zek. 8:23) Koma kodi n’ndani adzawaphunzitsa? (Aroma 10:13-15) Tili na mwayi komanso udindo wolalikila uthenga wabwino kwa munthu aliyense m’gawo lathu.—od peji 84 pala. 10-11.
MMENE TINGACITILE:
Muzikonzekela. Kodi mumapeza anthu amene amakamba citundu cina? Mungaseŵenzetse JW Language app kuti mudziŵe mmene mungacitile ulaliki wacidule. Mwina mungaseŵenzetse foni kapena tabuleti kuti muthandize munthu kudziŵa zambili m’citundu cake pa jw.org
Muzikhala chelu. Polalikila ku nyumba na nyumba, musalekelele mwayi wolalikila anthu oyenda m’njila, kapena amene akuyembekezela m’motoka. Ngati mukucita ulaliki wapoyela, maganizo anu azikhala pa kulalikila.
Khalani wakhama. Muziyesetsa kubwelelako ku makomo amene simunapezeko anthu. Yesetsani kukamba na anthu pa nyumba iliyonse, mwina pa nthawi ina kapena pa tsiku lina mu wikiyo. Anthu ena tingakambe nawo pa foni, m’kalata, kapena pa ulaliki wa mu mseu.
Muzibwelelako. Mukapeza munthu wacidwi muzibwelelako mwamsanga. Ngati munthuyo akamba citundu cina, yesani kupeza wofalitsa wodziŵa citunduco kuti akam’thandize. Koma poyembekezela kuti wofalitsayo apezeke, pitilizani kuphunzila naye.—od peji 94 mapa. 39-40
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KULALIKILA “MPAKA KUMALEKEZELO A DZIKO LAPANSI,” NDIYENO KAMBILANANI MAFUNSO AYA:
Kodi abale na alongo anapanga makonzedwe anji kuti akafikile anthu a ku dela lakutali? (1 Akor. 9:22, 23)
Kodi analimbana ndi mavuto anji?
Ni madalitso ati amene anapeza?
Kodi mungayese kucita zotani kuti mufikile anthu ambili m’gawo lanu?