Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Munthu Amene Amakamba Cinenelo Cina
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Yehova amacita cidwi ndi umoyo wakuuzimu wa anthu a “mtundu uliwonse.” (Mac. 10:34, 35) N’cifukwa cake Yesu anakamba kuti uthenga wabwino udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu” ndi ku “mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Mneneli Zekariya analosela kuti anthu a “m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina” adzalandila coonadi. (Zek. 8: 23) Masomphenya a mtumwi Yohane aonetsa kuti anthu amene adzapulumuka cisautso cacikulu adzakhala ocokela “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse.” (Chiv. 7: 9, 13, 14) Malinga ndi zimene tafotokoza m’nkhaniyi, tikakumana ndi munthu amene amalankhula cinenelo cina, tiyenela kuyesetsa kumulalikila.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pa kulambila kwanu kwa pabanja, citani citsanzo coonetsa wofalitsa akulalikila munthu amene amakamba cinenelo cina.