UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kugwilizana Polalikila M’gawo la Vitundu Vosiyana-siyana
Kambili anthu amamvetsela uthenga wa Ufumu ngati aumvela m’citundu cawo. Mwina ndiye cifukwa cake pa Pentekosite mu 33 C.E., Yehova anakonza zakuti “Ayuda ena, anthu oopa Mulungu, ocokela mu mtundu uliwonse mwa mitundu ya pansi pa thambo,” amvele uthenga wabwino mu “cinenelo cimene anabadwa naco,” olo kuti anali kukambanso citundu cofala monga Ciheberi kapena Cigiriki. (Mac. 2:5, 8) Kumadela a vitundu vosiyana-siyana masiku ano, mipingo imene imacita misonkhano m’zinenelo zosiyana ingakhale na magawo awo m’dela limodzi. Kodi ofalitsa m’mipingo yaconco angalalikile bwanji mogwilizana kuti aliyense m’gawolo alandile coonadi koma pa nthawi imodzi-modzi n’kumacita zinthu mwadongosolo kuti asamakhumudwitse eni nyumba?
Kukambilana (Miy. 15:22): Oyang’anila utumiki afunika kukambilana njila ya mmene angalalikilile uthenga wabwino, imene ingakomele mipingo yonse. Mipingo imene imalalikila m’vitundu vina ingafune kuti mpingo wanu uzilumpha manyumba a citundu cawo amene ali m’gawo lawo. Angafune kucita izi ngati gawo lawo ni laling’ono. Koma ngati sakwanitsa kulalikila gawo lawo lonse kaŵili-kaŵili cifukwa cakuti ni lalikulu, angapemphe kuti musamalumphe nyumba iliyonse, koma muziwadziŵitsa mukapeza munthu wacidwi. (od peji 93 pala. 37) Mwina angapemphe kuti mpingo wanu uwathandize kusakila anthu amene amakamba citundu ca mpingo wawo na kulemba ma adresi amene angakhale mbali ya gawo la mpingo wawo. (km 7/12 peji 6, bokosi) Komanso musaiŵale kuti nyumba zina zimakhala na anthu a vitundu viŵili kapena kuposelapo. Makonzedwe a mmene mungalalikile m’gawolo ayenela kugwilizana na malamulo oteteza nzika.
Kugwilizana (Aef. 4:16): Tsatilani mosamala malangizo aliwonse amene woyang’anila utumiki wanu angakupatseni. Kodi mumatsogoza phunzilo la Baibo m’citundu cimene munthuyo akonda koma si ca mpingo wanu? Munthuyo angapite patsogolo mwamsanga ngati mungapatse phunzilolo kwa wa mu mpingo wina kapena kagulu ka citundu cake.
Kukonzekela (Miy. 15:28; 16:1): Ngati m’gawo lanu mwapeza munthu wokamba citundu cina, citani zonse zotheka kuti mumulalikile. Mungakonzekele mwa kudziŵilatu vitundu vimene mungakumane navo komanso mwa kucitilatu daunilodi ma Baibo a vitundu vina na mavidiyo pa foni kapena pa tabuleti yanu. Mungaseŵenzetsenso JW Language app kuti mudziŵe kupeleka moni m’zinenelo zimenezo.