MUTU 8
Atumiki a Uthenga Wabwino
YEHOVA anatipatsa Mwana wake Yesu Khristu, amene ni citsanzo cabwino ngako kuti titengeleko. (1 Pet. 2:21) Munthu akakhala wotsatila wa Yesu, amayamba kulengeza uthenga wabwino monga mmodzi wa atumiki a Mulungu. Pofuna kuonetsa kuti zimenezi zidzakhala zotsitsimula mwauzimu, Yesu anati: “Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28, 29) Kwa awo amene alabadila ciitano cimeneci, lonjezo la Yesuli silinawagwilitse mwala!
2 Pokhala Mtumiki Wamkulu wa Mulungu, Yesu anaitana anthu ena kuti akhale otsatila ake. (Mat. 9:9; Yoh. 1:43) Anawaphunzitsa nchito yolalikila, na kuwatumiza kukagwila nchito yolalikila imene iyenso anali kucita. (Mat. 10:1–11:1; 20:28; Luka 4:43) Pambuyo pake, anatumizanso ophunzila ena 70 kuti akalalikile uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. (Luka 10:1, 8-11) Powatumiza, Yesu anawauza kuti: “Amene akukumvelani, akumvelanso ine. Ndipo amene akunyalanyaza inu akunyalanyazanso ine. Ndipotu amene akunyalanyaza ine akunyalanyazanso amene anandituma.” (Luka 10:16) Mwakutelo ,Yesu anaonetsa kukula kwa udindo umene anapatsa ophunzila ake. Iwo anali kukaimilako Yesu na Mulungu Wakumwambamwamba! Ni mmenenso zilili masiku ano kwa onse olabadila ciitano ca Yesu cakuti: ‘Bwela ukhale wotsatila wanga.’ (Luka 18:22; 2 Akorinto 2:17) Onse olabadila ciitano cimeneci ali na udindo waukulu wolalikila uthenga wabwino wa Ufumu, na kupanga ophunzila.—Mat. 24:14; 28:19, 20.
3 Popeza ifenso tinalabadila ciitano ca Yesu cakuti timutsatile, tinadalitsidwa ‘pophunzila’ za Yehova Mulungu na Yesu Khristu. (Yoh. 17:3) Taphunzitsidwa njila za Yehova. Na thandizo lake, takwanitsa kusintha maganizo athu, kuvala umunthu watsopano, na kukhala na umoyo woyendela miyezo ya Yehova yolungama. (Aroma 12:1, 2; Aef. 4:22-24; Akol. 3:9, 10) Kuyamikila kwathu Yehova mocokela pansi pa mtima ndiko kunatipangitsa kuti tipatulile miyoyo yathu kwa Iye, kenako n’kubatizika m’madzi monga cisonyezelo cakuti tinadzipatulila. Pa ubatizo wathu, m’pamene timaikidwa kukhala mtumiki wa Mulungu.
4 Tikumbukile nthawi zonse kuti potumikila Mulungu, tiyenela kum’tumikila na manja oyela, komanso mtima woyela. (Sal. 24:3, 4; Yes. 52:11; 2 Akor. 6:14–7:1) Pokhulupilila mwa Yesu Khristu, tinapeza cikumbumtima coyela. (Aheb. 10:19-23, 35, 36; Chiv. 7:9, 10, 14) Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti ayenela kucita zinthu zonse ku ulemelelo wa Mulungu kuti apewe kukhumudwitsa ena. Nayenso mtumwi Petulo, anakambapo za kufunika kokhala zitsanzo zabwino kuti tikope osakhulupilila abwele m’coonadi. (1 Akor. 10:31, 33; 1 Pet. 3:1) Kodi mungam’thandize bwanji munthu kuti nayenso akayenelele kukhala mtumiki wa uthenga wabwino?
OFALITSA ATSOPANO
5 Mukangoyamba kuphunzila Baibo na munthu wokondwelela, mulimbikitseni kuti aziuzako ena zimene amaphunzila. Angamauzeko ena poceza nawo, monga abululu ake moceza, mabwenzi ake, anzake a kunchito, kapena anthu ena. Iyi ni sitepu yofunika kwambili yophunzitsila atsopano kukhala otsatila a Yesu Khristu mwa kulalikila uthenga wabwino. (Mat. 9:9; Luka 6:40) Pamene watsopano wapita patsogolo, na kucita khama kumalalikila kwa ena mwamwayi ndiponso mowafika pamtima, ndithudi adzakamba kuti nayenso afuna kuti azilalikila pamodzi na mpingo.
KUKWANILITSA ZIYENELEZO
6 Mukalibe kupempha munthu kuti apite namwe koyamba mu ulaliki wa nyumba na nyumba, pali ziyenelezo zimene afunika kuzikwanilitsa coyamba. Zili telo cifukwa munthu akayenda nafe mu ulaliki, anthu amangomutenga kuti ni Mboni ya Yehova. Mwa ici, munthuyo ayenela kukhala woti anasintha kale umoyo wake ndipo amayendela miyezo ya Yehova yolungama, cakuti angayenelele kukhala wofalitsa wosabatizika.
7 Pamene muphunzila na munthu n’kumakambilana naye mfundo za m’Baibo, mumayamba kudziŵa za umoyo wake. Mumatha kuona ngati amagwilitsila nchito zimene mumaphunzila. Koma pali mbali zina zokhudza umoyo wa wophunzila wanu zimene akulu adzafuna kukambilana naye pamodzi na imwe.
8 Mgwilizanitsi wa bungwe la akulu adzakonza zakuti akulu aŵili (mmodzi wa m’komiti ya utumiki) akakambilane mbalizo na wophunzila wanu. M’mipingo yokhala na akulu ocepa kwambili, mkulu na mtumiki wothandiza wocita bwino angasamalile mbali imeneyi. Abale omwe agaŵilidwa mbali imeneyi ayenela kuisamalila mwamsanga. Cakuti ngati angawapatsile kumsonkhano wa mpingo mbali yopenda wophunzila wanu, zingatheke kuti akuluwo angafune kukumana nanu pamodzi na wophunzila wanu pambuyo pa msonkhanowo. M’thandizeni kukhala womasuka pa makambilano amenewo. Koma wophunzilayo akalibe kuyenelezedwa kukhala wofalitsa wosabatizika, akulu atsimikizile kuti iye:
(1) Amakhulupilila kuti Baibo ni Mawu ouzilidwa a Mulungu.—2 Tim. 3:16.
(2) Amadziŵa na kukhulupilila ziphunzitso zikulu-zikulu zoyambilila za m’Malemba, cakuti atafunsidwa mafunso angathe kuyankha mogwilizana na Baibo, osati monga mwa ziphunzitso za cipembedzo conyenga kapena mwa maganizo ake.—Mat. 7:21-23; 2 Tim. 2:15.
(3) Amalabadila lamulo la m’Baibo la kusonkhana pamodzi na anthu a Yehova ngati angakwanitse kutelo.—Sal. 122:1; Aheb. 10:24, 25.
(4) Amadziŵa zimene Baibo imaphunzitsa pa zaciwelewele, cigololo, cipali, komanso mathanyula, ndipo amapewa makhalidwe amenewa. Ngati iye amakhala na munthu amene si mwamuna wake kapena mkazi wake, ndipo si wacibale wake, afunika kukhala okwatilana mwalamulo.—Mat. 19:9; 1 Akor. 6:9, 10; 1 Tim. 3:2, 12; Aheb. 13:4.
(5) Amamvela lamulo la m’Baibo loletsa kumwa mwaucidakwa, komanso amapewa mtundu uliwonse wa amkolabongo.—2 Akor. 7:1; Aef. 5:18; 1 Pet. 4:3, 4.
(6) Amapewa mayanjano oipa podziŵa kuopsa kwake.—1 Akor. 15:33.
(7) Anathetselatu umembala wake na cipembedzo conyenga cimene analiko. Analeka kupezeka kumisonkhano yawo, kapena kutengako mbali m’mapulogilamu awo.—2 Akor. 6:14-18; Chiv. 18:4.
(8) Satengako mbali m’zandale zilizonse.—Yoh. 6:15; 15:19; Yak. 1:27.
(9) Amakhulupilila zimene zili pa Yesaya 2:4 za kusaloŵelela m’mikangano ya maiko.
(10) Ni wofunitsitsa kukhala Mboni ya Yehova.—Sal. 110:3.
9 Ngati akulu aona kuti si otsimikiza za mmene wophunzilayo akuonela mfundo inayake ayenela kumufunsa, ndipo mwina angakambilane naye malemba osagwila mawu monga maziko a mfundoyo. Ayenela kumvetsetsa kuti anthu amene amaloledwa kuyamba kulalikila na Mboni za Yehova, ni aja amene anasinthadi umoyo wawo, ndipo amatsatila ziyenelezo za m’Malemba zimenezi. Zokamba zake zidzathandiza akuluwo kuona ngati munthuyo akumvetsadi zoyembekezeka kwa iye, ndiponso ngati akuyenelela pa mlingo wabwino kuti ayambe kuyenda mu ulaliki na mpingo.
10 Akulu ayenela kudziŵitsa wophunzilayo mwamsanga ngati ni woyenelela kapena ayi. Kambili, zimatheka kumudziŵitsa zimenezi pamapeto pa makambilano awo. Ngati akuluwo amuyeneleza, amulandile na manja aŵili monga wofalitsa. (Aroma 15:7) Amulimbikitse kuti ayambe kupita mu ulaliki mwamsanga, komanso kuti akapeleke lipoti la utumiki wakumunda kumapeto kwa mwezi. Akulu angafotokozele wophunzila Baibo ameneyo kuti munthu akayenelezedwa kukhala wofalitsa wosabatizika, ndipo wapeleka lipoti lake loyamba la utumiki wa kumunda, amam’tsegulila Khadi ya Mpingo Yolembapo Nchito za Wofalitsa m’dzina lake, na kuiika m’faelo ya mpingo. Akulu amalemba nchito za wofalitsa kotelo kuti gulu lithe kusamalila bwino nchito ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi, komanso kuti wofalitsa azitengako mbali m’zocitika zauzimu na kuthandizidwa kuuzimu. Ndiponso, akulu amadziŵitsa ofalitsa atsopano kuti zolemba zokhudza munthu aliyense zimasamalidwa mogwilizana na lamulo lacitetezo la Mboni za Yehova lakuti Global Data Protection Policy lopezeka pa jw.org.
11 Ngati tikhala na cidwi cofuna kum’dziŵa bwino wofalitsa watsopano, na kumuyamikila pa zimene akwanitsa kucita, tingam’limbikitse kwambili. Zingam’limbikitsenso kumapeleka malipoti a utumiki mwezi uliwonse, na kuwonjezela khama lake potumikila Yehova.—Afil. 2:4; Aheb. 13:2.
12 Akulu akatsimikiza kuti wophunzilayo wayenelela kuti azilalikila, am’patse buku la Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova. Akapeleka lipoti lake loyamba, cilengezo cacidule cakuti iye ni wofalitsa wosabatizika cikapelekedwe ku mpingo.
KUTHANDIZA ACICEPELE
13 Nawonso ana aang’ono angayenelele kukhala ofalitsa uthenga wabwino. Paja Yesu analandila ana aang’ono na kuwadalitsa. (Mat. 19:13-15; 21:15, 16) Ngakhale kuti makolo ndiwo ali na udindo waukulu wothandiza ana awo, ena mu mpingo angathandize acicepele ofunitsitsa na mtima wonse kutengako mbali m’nchito yolalikila za Ufumu. Ngati ndimwe kholo, citsanzo canu cabwino pa nkhani ya ulaliki cingalimbikitse ana anu kukhala okangalika pa utumiki wawo kwa Mulungu. Ngati mwana wacitsanzo cabwino amayesetsa kuuzako ena za cikhulupililo cake, kodi inu mungacitenso ciani kuti mum’thandize?
14 Zingakhale bwino kuti kholo likaonane na mmodzi wa akulu a m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo kuti akakambilane nawo ngati mwana wawo ali woyeneleladi kukhala wofalitsa. Mgwilizanitsi wa bungwe la akulu adzakonza zakuti akulu aŵili (mmodzi wa m’komiti ya utumiki) akambilane na mwanayo pamodzi na kholo kapena makolo ake onse aŵili okhulupilila, kapenanso winawake womusunga amene ni wokhulupilila. Ngati mwanayo amadziŵa mfundo zikulu-zikulu zoyambilila za coonadi ca m’Baibo, ndipo zionekelatu kuti ni wofunitsitsa kutengako mbali mu ulaliki, zimenezi zingaonetse kuti iye akupita patsogolo. Pambuyo popenda mbali zimenezi komanso zina zokhudzanso anthu akulu-akulu, akulu aŵiliwo angaone ngati angamuyeneleze mwanayo kukhala wofalitsa wosabatizika. (Luka 6:45; Aroma 10:10) Pokambilana na mwana wamng’ono, n’kosafunikila kukambilana naye nkhani zokhudza cabe anthu akulu-akulu, zoonekelatu kuti sizingam’pindulile kanthu.
15 Pokambilana, akulu amuyamikile mwanayo cifukwa ca kupita patsogolo kwake. Am’limbikitse kumenyela nkhondo colinga cokabatizika. Popeza kuti makolo anagwila nchito yaikulu yophunzitsa mwana wawo coonadi, nawonso ayenela kuwayamikila ngako. Polimbikitsa makolo kuti apitilize kuthandiza mwana wawo, akuluwo akambilane nawo mfundo za pa mutu wakuti: ““Mawu kwa Makolo Acikhristu,” pa masamba 179-181.
KUDZIPATULILA NA UBATIZO
16 Ngati mwafika pom’dziŵa bwino Yehova na kum’konda kwambili, ndipo mumacita zimene iye afuna, komanso mumatengako mbali m’nchito yolalikila, mufunika kulimbitsa ubale wanu na iye. Motani? Mwa kupatulila moyo wanu kwa iye, na kubatizika m’madzi monga cisonyezelo cakuti munadzipatulila.—Mat. 28:19, 20.
17 Kupatulila cinthu kumatanthauza kuciika padela pa colinga copatulika. Kudzipatulila kwa Mulungu kumatanthauza kumufikila m’pemphelo na kum’lonjeza kucokela pansi pa mtima kuti mudzagwilitsila nchito moyo wanu wonse kucita cifunilo cake, na kuyenda m’njila zake. Kumatanthauzanso kudzipeleka kwa iye yekha kwamuyaya. (Deut. 5:9) Munthu amacita zimenezi payekha mseli. Ndipo palibe wina angam’citileko zimenezi.
18 Komabe, mukauza Yehova mseli kuti mwadzipeleka kwa iye, zisathele pamenepo. Muyenelanso kukaonetsa cisonyezelo kwa ena kuti munadzipatulila kwa Mulungu. Cisonyezelo cimeneco ni ubatizo wa m’madzi, monga mmene Yesu anacitila. (1 Pet. 2:21; 3:21) Kodi mukapanga cosankha cofuna kubatizika kuti mutumikile Yehova, muyenela kucita ciani? Uzani mgwilizanitsi wa bungwe la akulu za colinga canu. Iye adzapempha akulu ena kuti akakambilane namwe pofuna kuona ngati mukukwanilitsa ziyenelezo za ubatizo. Kuti mudziŵe zambili, conde ŵelenganinso mbali yakuti: Mawu kwa Wofalitsa Wosabatizika,” pa masamba 182-184 m’buku lino, komanso yakuti: “Mafunso kwa Ofuna Kubatizika,” pa masamba 185-207.
MALIPOTI OONETSA KUPITA PATSOGOLO KWA UTUMIKI
19 Kwa zaka zambili, malipoti a padziko lonse oonetsa mmene kulambila koyela kwapitila patsogolo amakhala olimbikitsa kwambili kwa anthu a Yehova. Kucokela pamene Yesu Khristu anauza ophunzila ake kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi, Akhristu oona amakhala na cidwi coona za kukwanilitsidwa kwa mawu amenewo.—Mat. 28:19, 20; Maliko 13:10; Mac. 1:8.
20 Otsatila a Yesu oyambilila anali kukondwela pakumva malipoti oonetsa kupita patsogolo kwa nchito yolalikila. (Maliko 6:30) Buku la Machitidwe limatiuza kuti anthu pafupi-fupi 120 anapezekapo pamene ophunzila analandila mzimu woyela pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Posapita nthawi, ciŵelengelo ca ophunzila cinakwela kufika m’ma 3,000, kenako mpaka m’ma 5,000. Lipoti linamveka kuti “Yehova anapitiliza kuwawonjezela anthu amene anali kuwapulumutsa” ndipo “ansembe ambilimbili anakhala okhulupilila.” (Mac. 1:15; 2:5-11, 41, 47; 4:4; 6:7) Ndithudi, malipoti amenewo anawalimbikitsa ngako ophunzilawo. N’zosacita kufunsa kuti malipotiwo anawapatsa mphamvu zopitiliza nchito imene Mulungu anawapatsa, mosasamala kanthu za mazunzo oopsa osonkhezeledwa na atsogoleli aciyuda.
21 Pofika m’ma 60 C.E na 61 C.E, Paulo anapeleka lipoti m’kalata yake kwa Akolose lakuti uthenga wabwino unali ‘kubala zipatso ndipo unawonjezeka m’dziko lonse,’ komanso “unalalikidwa m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo.” (Akol. 1:5, 6, 23) Akhristu oyambilila analabadila Mawu a Mulungu, ndipo mzimu woyela unawalimbikitsa kucita zambili panchito yolalikila, asanafike mapeto a dongosolo la zinthu la Ayuda mu 70 C.E. Kunena zoona, Akhristu okhulupilikawo analimbikitsidwa kwambili kumva malipoti osimba za mmene nchito inali kupitila patsogolo.
22 Masiku anonso, gulu la Yehova limasunga malipoti a mmene nchito ikuyendela pokwanilitsa ulosi wa pa Mateyu 24:14, umene umati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” Monga atumiki a Mulungu odzipatulila, tili na nchito yofunika kuigwila mmangu-mmangu. Aliyense wa ife ayenela kukhala na mtima wofuna kugwila nchito yolalikila kuti ikwanilitsidwe mapeto asanafike. Yehova adzaonetsetsa kuti nchitoyi yakwanilitsidwa. Ndipo ngati titengako mbali m’nchitoyi, Yehova adzakondwela nafe ndipo adzatiyanja.—Ezek. 3:18-21.
LIPOTI LANU LA UTUMIKI WAKUMUNDA
23 Kodi tiyenela kucitila lipoti ciani maka-maka? Kafomu ka gulu lathu kakuti Lipoti la Utumiki Wakumunda, kamalongoza zofunika kulembapo. Komanso malangizo otsatilawa angakuthandizeni.
24 M’danga lakuti “Zogaŵila (Zopulinta Kapena za Pacipangizo),” lembani ciwonkhetso ca zofalitsa zimene munagaŵila kwa anthu amene si mboni zobatizika, kaya zopulinta kapena za pacipangizo. M’danga lakuti “Kutambitsa Mavidiyo,” lembani maulendo amene munatambitsa anthu mavidiyo athu.
25 Pocitila lipoti “Maulendo Obwelelako,” ŵelengani maulendo amene munapanga kuti mukulitse cidwi cimene munthu amene si Mboni yobatizika anaonetsa paulendo wapita. Mungapange ulendo wobwelelako mwa kuonana na munthu mwacindunji, mwa kum’lembela kalata, kum’tumila foni, kum’lembela meseji kapena imelo, kapenanso kum’pelekela zofalitsa. Komanso mukatsogoza phunzilo la Baibo, umenewonso ni ulendo wobwelelako. Kholo lingaŵelenge ulendo wobwelelako umodzi mlungu uliwonse likacititsa kulambila kwa pabanja, ngati palinso mwana wosabatizika.
26 Ngakhale kuti nthawi zambili timatsogoza phunzilo la Baibo mlungu uliwonse, tiyenela kuliŵelenga monga phunzilo limodzi pamwezi. Ofalitsa ayenela kuwonkhetsa maphunzilo a Baibo osiyana-siyana amene atsogoza m’mweziwo. Maphunzilo amene timacitila lipoti amaphatikizapo aja amene timatsogoza kwa anthu amene si Mboni zobatizika. Mungacitilenso lipoti phunzilo la Baibo la m’bale kapena mlongo wozilala ngati munauzidwa na m’bale wa m’komiti ya utumiki kuti muziphunzila naye, komanso ngati mumaphunzila na wofalitsa wobatizika catsopano koma akalibe kumaliza buku lakuti Zimene Baibo Ingatiphunzitse, komanso lakuti Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu.
27 Tiyenela kulemba malipoti olondola a “Maola.” Imeneyi ni nthawi imene mumatayila pa ulaliki wa nyumba na nyumba, pa maulendo obwelelako, potsogoza maphunzilo a Baibo, kapena polalikila mwamwayi kwa anthu amene si Mboni zobatizika. Ngati ofalitsa aŵili aseŵenzela pamodzi mu ulaliki, onse angaŵelenge maola olingana, koma mmodzi cabe ndiye ayenela kuŵelenga ulendo wobwelelako pa munthu mmodzi kapena phunzilo la Baibo limene latsogozedwa. Makolo onse aŵili amene amathandizana pa Kulambila kwa Pabanja ayenela kuŵelenga ola limodzi mlungu uliwonse. Abale ayenelanso kucitila lipoti nthawi imene akambila nkhani ya anthu onse. Womasulila nkhani ya anthu onse nayenso ayenela kuŵelengela nthawiyo. Koma pali zocitika zina zofunika zimene sitiŵelengela nthawi yake, monga kukonzekela ulaliki, kupezeka pa makambilano otenga malangizo a ulaliki, pogwila nchito zina za mpingo, na zina zotelo.
28 Wofalitsa aliyense ayenela kutsatila cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo poŵelengela nthawi yonse imene wathela mu ulaliki. Ofalitsa ena amalalikila m’madela opezekamo anthu ambili-mbili, pamene ena amalalikila m’madela okhala na anthu ocepa cakuti amayenda mitunda itali-itali. Magawo amasiyana; ofalitsa nawonso amasiyana mmene amaŵelengela utumiki wawo. Mwa ici, pa kaŵelengedwe keni-keni ka nthawi imene munthu wathela mu ulaliki, Bungwe Lolamulila siliyesa kulamulila zikumbumtima za abale mumpingo wa Mulungu wa padziko lonse. Ndipo palibe aliyense anapatsidwa udindo woweluza anzake pa nkhani imeneyi.?—Mat. 6:1; 7:1; 1 Tim. 1:5.
29 Tiyenela kucitila lipoti maola okha, osati mphindi ayi. Okhawo ololedwa kucita lipoti mphindi cabe ni aja amene sangakwanitse cifukwa ca ukalamba, matenda, kapena okhala kunyumba zosungilako okalamba, kapena zolepheletsa zina zoti kulibe mwina mocitila. Wofalitsa woteloyo angamacitile lipoti mphindi 15, 30 kapena 45 mmene angakwanitsile. Ngakhale alalikile mphindi 15 zokha pamwezi, ayenela kucitila lipoti ndithu mphindi zimenezo. Adzaŵelengeledwa kuti ni wofalitsa wokhazikika. Makonzedwe amenewa amagwilanso nchito kwa wofalitsa amene kwa mwezi umodzi kapena kuposelapo sangakwanitse kulalikila, mwina cifukwa ca kudwala kwambili kapena kuvulala. Makonzedwe amenewa amagwila nchito cabe kwa aja amene angakwanitse kucita zocepa kwambili mu ulaliki. Komiti ya utumiki ndiyo imasankha wofalitsa amene angayenelele kuikidwa pa makonzedwe amenewa.
KHADI YA MPINGO YOLEMBAPO NCHITO ZA WOFALITSA
30 Nchito zanu mu utumiki wakumunda wa mwezi uliwonse zimalembedwa pa Khadi ya Mpingo Yolembapo Nchito za Wofalitsa. Khadi imeneyi ni katundu wa mpingo. Ngati mufuna kusamukila ku mpingo wina, musaiŵale kudziŵitsa akulu mumpingo wanu. Kalembela adzaonetsetsa kuti watumiza khadi yanu ku mpingo umene mukusamukilako. Mwanjila imeneyi, akulu ku mpingo wanu watsopano adzatha kukulandilani na kukuthandizani kuuzimu. Ngati mwacoka pa mpingo wanu kwa miyezi yosapitilila itatu, conde pitilizani kutumiza malipoti anu ku mpingo wakwanu.
CIMENE TIMAPELEKELA LIPOTI LA UTUMIKI WATHU
31 Kodi nthawi zina mumaiŵala kupeleka lipoti lanu la utumiki? Paja kuiŵala kulibe mwini, tonsefe timafunikila kukumbutsidwa nthawi zina. Koma ngati timvetsa cifukwa copelekela lipoti, na kuona phindu lake, tidzayamba kukumbukila mosavuta kupeleka lipoti lathu.
32 Koma ena afunsapo kuti: “Popeza Yehova amadziŵa zimene nimacita mu utumiki wake, n’kwanji kupeleka lipoti ku mpingo?” N’zoona kuti Yehova amaona zimene timacita, amadziŵanso ngati zimene tacita zili zeni-zeni kapena n’zaciphamaso cabe. Kumbukilani kuti Yehova analemba m’Baibo ciŵelengelo ca masiku amene Nowa anakhala m’cingalawa, na ciŵelengelo ca zaka zimene Aisiraeli anayenda m’cipululu. Mulungu anasunganso ciŵelengelo ca anthu amene anakhalabe okhulupilika, komanso ca ana amene sanamumvele. Analembanso mmene Aisiraeli anagonjetsela dziko la Kanani, na zimene oweluza okhulupilika aciisiraeli anacita. Inde, analemba zinthu zambili zokhudza atumiki ake. Anauzila anthu kulemba bwino-bwino zocitikazo. Izi zitithandiza kuona kuti Mulungu amafuna kusunga zolembedwa zolondola.
33 Zocitika za m’mbili yakale zolembedwa m’Baibo zimaonetsa kuti anthu a Yehova anali kulemba ziŵelengelo zolondola m’malipoti. Nkhani zambili za m’Baibo sizikanakhala zotsatilika bwino kukanakhala kuti ziŵelengelo zinali zongoyelekezela mwacisawawa. Onani zitsanzo izi: Genesis 46:27; Ekisodo 12:37; Oweruza 7:7; 2 Mafumu 19:35; 2 Mbiri 14:9-13; Yohane 6:10; 21:11; Machitidwe 2:41; 19:19.
34 Olo kuti malipoti athu saphatikizapo zonse zimene timacita pakulambila kwathu Yehova, ni othandiza kwambili m’gulu lake. M’zaka za zana loyamba, pamene atumwi anabwelako kokalalikila, anacitila lipoti kwa Yesu ‘pomuuza zonse zimene iwo anacita na kuphunzitsa.’ (Maliko 6:30) Nthawi zina, malipoti angaonetse mbali zina za utumiki wathu zofunikila cisamalilo capadela. Ziŵelengelo zingaonetse kuti ticita bwino pa mbali zina, koma mbali zina siticita bwino. Mwacitsanzo, zingaonetse kuti ciŵelengelo ca ofalitsa sicikukwela kweni-kweni. Mwina pangafunikile cilimbikitso pa mbali inayake, kapena kuthetsa mavuto ena amene angabuke. Oyang’anila amaona malipoti amenewa na kuyesetsa kuthetsa mavuto alionse amene angalepheletse ofalitsa ena kapena mpingo wonse kupita patsogolo.
35 Malipoti amathandizanso gulu kuona kumene kufunika anchito ambili mu utumiki wakumunda. Amaonetsanso kumene nchito yolalikila ikuyenda bwino, kumene siikupita patsogolo kweni-kweni, komanso kuona mabuku amene angathandize bwino anthu kuphunzila coonadi. Malipoti amathandizanso gulu kusankha mabuku odzaseŵenzetsa mu ulaliki m’tsogolo, m’madela osiyana-siyana padziko lapansi.
36 Ambili a ife, malipoti amatilimbikitsa ngako. Kodi sitilimbikitsidwa pakumva za mmene abale athu akucitila bwino pa nchito yolalikila uthenga wabwino padziko lonse? Malipoti a ziwonjezeko amatithandiza kuona mmene gulu lonse la Yehova likukulila. Tikamamva zocitika za abale zimatipatsa cimwemwe codzaza tsaya, na kutisonkhezela kucita zambili m’nchito yolalikila. (Mac. 15:3) Ngati tipeleka malipoti athu mwamsanga, timaonetsa kuti timasamala za abale athu kulikonse kumene ali. Mwa njila yocepa imeneyi, timaonetsa kuti ndife ogonjela ku makonzedwe a gulu la Yehova.—Luka 16:10; Aheb. 13:17.
KUDZIIKILA ZOLINGA
37 Tisakhale na maganizo ofuna kumalinganiza utumiki wathu na uja wa munthu wina. (Agal. 5:26; 6:4) Mikhalidwe imasiyana pa umoyo wathu. Koma tingapindule kwambili ngati tidziikila zolinga zimene tingazikwanilitse pamlingo wathu wopita patsogolo mu utumiki. Tikamakwanilitsa zolinga zimenezo, tidzakhala acimwemwe komanso olimbikitsidwa na nchito yathu.
38 N’zoonekelatu kuti Yehova akufulumizitsa nchito yosonkhanitsa anthu amene adzawapulumutse pa “cisautso cacikulu.” Tikukhaladi m’nthawi imene ulosi wa Yesaya ukukwanilitsidwa wakuti: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wocepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” (Chiv. 7:9, 14; Yes. 60:22) Ha! Ni mwayi waukulu cotani nanga, kukhala atumiki a uthenga wabwino m’masiku ano otsiliza!—Mat. 24:14.
Kodi ndimwe wofunitsitsadi kuona kuti nchito yolalikila ikwanilitsidwe mapeto asafike?