LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od tsa. 179-tsa. 184
  • Zakumapeto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zakumapeto
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Ubatizo Ndi Wofunika Bwanji Paubwenzi Wanu ndi Mulungu?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Makambilano othela na ofunsila ubatizo
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
Onaninso Zina
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od tsa. 179-tsa. 184

Zakumapeto

Mawu kwa Makolo Acikhristu:

Monga kholo, colinga canu n’cakuti muthandize ana anu okondekawo kukonda Yehova kuti akadzipatulile kwa iye. Koma kodi mungawathandize bwanji kuti nawonso akabatizike? Ndipo ni liti pamene angakhale okonzeka kutenga sitepu yofunika imeneyi?

Yesu analangiza otsatila ake kuti: “Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza.” (Mat. 28:19) Malinga na mawu amenewa, ciyenelezo coyambilila kuti munthu abatizike, ni kukhala wophunzila wa Yesu. Inde, kumvetsetsa na kukhulupilila ziphunzitso za Khristu, maka-makanso kuzitsatila. Ngakhale acicepele angakwanitse kucita zimenezi.

Khalani citsanzo cabwino kwa ana anu, ndipo khomelezani ziphunzitso za Yehova m’mitima yawo. (Deut. 6:6-9) Gwilitsilaninso nchito mfundo za m’buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, komanso lakuti Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu. Mwakutelo, mudzawaphunzitsa coonadi ca m’Baibo, na kuwakonzekeletsa kuti aziyendela mfundo za m’Baibo. Athandizeni kuti azitha kufotokoza m’mawu awo-awo zimene amakhulupilila. (1 Pet. 3:15) Cidziŵitso na cilimbikitso cimene amapeza kwa imwe, komanso kucokela pa phunzilo laumwini, kulambila kwa pabanja, misonkhano ya mpingo na mayanjano abwino, zidzawathandiza kuti akabatizike na kupitabe patsogolo. Athandizeni kuti adziikile zolinga zauzimu.

Miyambo 20:11 imaonetsa kuti ngakhale mwana “amadziŵika ndi nchito zake, ngati zocita zake zili zoyela ndiponso zowongoka.” Kodi ni macitidwe ati amene amaonetsa kuti mwana, mnyamata kapena mtsikana, wakhala wophunzila wa Yesu Khristu, ndipo ni wokonzeka kubatizika?

Mwana amene akupita patsogolo mokonzekela ubatizo ayenela kukhala womvela makolo ake. (Mac. 5:29; Akol. 3:20) Ponena za Yesu ali na zaka 12, Baibo imati: “Anapitiliza kumvela [makolo ake].” (Luka 2:51) N’zoona kuti simungayembekezele kuti mwana wanu azicita zinthu mwangwilo. Koma mwana amene afuna kukabatizika amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu pokhala womvela kwa makolo ake.

Iye amaonetsanso cidwi cake cofuna kuphunzila Baibo. (Luka 2:46) Kodi mwana wanu amafuna kupezeka ku misonkhano na kutengako mbali? (Sal. 122:1) Kodi amakhala na mtima wofunitsitsa kuŵelenga Baibo, na kucita phunzilo laumwini?—Mat. 4:4.

Mwana amene akupita patsogolo kuti akabatizike, amalimbikila kuika zinthu za Ufumu patsogolo mu umoyo wake. (Mat. 6:33) Amazindikilanso udindo wake wouzako ena za cikhulupililo cake. Amatengako gawo m’mbali zosiyana-siyana za utumiki, ndipo sacita manyazi kuuza aphunzitsi ake kapena anzake a kusukulu kuti ni Mboni ya Yehova. Akapatsidwa mbali pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, saitenga mopepuka.

Amakhalanso wa makhalidwe abwino mwa kupewa mayanjano oipa. (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33) Amasankhanso mosamala nyimbo zimene amakonda, mafilimu, mapulogilamu a pa TV, maseŵela a pa kompyuta, komanso moseŵenzetsela Intaneti.

Acicepele ena akhala akulabadila pamene makolo awo akuyesetsa kuwathandiza mwakhama. Iwo atenga coonadi kukhala cawo-cawo, ndipo ayenelela ubatizo. Tikufunilani dalitso la Yehova pamene mukuthandiza ana anu kufikila sitepu yofunika kwambili imeneyi pa ubwenzi wawo na Yehova.

Mawu kwa Wofalitsa Wosabatizika:

Ni mwayi waukulu kutumikila mumpingo monga wofalitsa wosabatizika. Tikuyamikilani cifukwa ca kupita patsogolo mwauzimu. Mwafika pom’dziŵa bwino Mulungu cifukwa cophunzila Mawu ake, ndipo mumakhulupilila malonjezo ake.—Yoh. 17:3; Aheb. 11:6.

Koma musanayambe kuphunzila na Mboni za Yehova, mwina munali ku cipembedzo cina. Kapena simunali m’cipembedzo ciliconse. N’kuthekanso kuti mwina munali kucita zinthu zina zosemphana na Mfundo za m’Baibo. Koma lomba, munaonetsa cikhulupililo canu mwa kulapa, kutanthauza kumva cisoni kucokela pansi pa mtima cifukwa ca zoipa zimene munacita kumbuyoku, komanso mwa kutembenuka, kutanthauza kulekelatu njila yoipayo, na kutsimikiza mtima kuti muzicita zoyenela pamaso pa Mulungu.—Mac. 3:19.

Kumbali ina, mwina mwadziŵa malemba opatulika “kucokela muli mwana.” Ngati n’telo, mwakhala wotetezeka ku makhalidwe osemphana na Cikhristu, komanso ku macimo aakulu. (2 Tim. 3:15) Mwaphunzila kukana ngati anzanu akunyengelelani kuti mucite zinthu zimene Yehova amadana nazo. Mwaonetsa kukhulupilika kwanu pocilikiza kulambila koona, komanso pouzako ena zimene mumakhulupilila. Mwaphunzitsidwa nchito yacikhristu yolalikila. Ndipo munapanga cosankha kuti mutumikile Yehova monga wofalitsa wosabatizika.

Mulimonsemo, kaya munaphunzila coonadi mutakula kale, kapena munadziŵa njila za Yehova mukali mwana, n’kutheka kuti tsopano mukuganizila masitepu aŵili pa kupita kwanu patsogolo mwauzimu—kudzipatulila na ubatizo. Mumadzipatulila kwa Yehova mwa kum’fikila m’pemphelo, na kumuuza cosankha canu cakuti mwadzipeleka kwa iye kwamuyaya. (Mat. 16:24) Ndiyeno monga cisonyezelo cakuti munadzipatulila, mumabatizika m’madzi. (Mat. 28:19, 20) Mukadzipatulila na kubatizika, ndiye kuti mwakhala mtumiki wovomelezeka wa Yehova Mulungu. Umenewu ni mwayi wosaneneka!

Koma monga munaunikilidwa pophunzila Baibo, mukhoza kukumana na zovuta zosiyana-siyana. Kumbukilani kuti Yesu atangobatizika, ‘mzimu unam’tsogolela kucipululu kuti akayesedwe ndi Mdyelekezi.’ (Mat. 4:1) Imwenso n’cimodzimodzi. Mukadzabatizika mudzayembekezele kukumana na mayeso owonjezeleka. (Yoh. 15:20) Ndipo adzabwela m’mitundu yosiyana-siyana. A m’banja mwanu angayambe kukutsutsani. (Mat. 10:36) Mwinanso anzanu a kusukulu, anzanu a kunchito, komanso amene anali mabwenzi anu, angamakunyodoleni. Koma nthawi zonse kumbukilani mawu a Yesu opezeka pa Maliko 10:29, 30 akuti: “Ndithu ndikukuuzani amuna inu, palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda cifukwa ca ine, ndi cifukwa ca uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, limodzi ndi mazunzo, ndipo m’nthawi imene ikubwelayo, adzapeza moyo wosatha.” Conco, limbikilanibe kukhala pafupi na Yehova, na kutsatila miyezo yake yolungama.

Pamene mudzafuna kubatizika, mukadziŵitse mgwilizanitsi wa bungwe la akulu. Pambuyo pa cigawo cino, pali mafunso amene akulu adzakambilana namwe pofuna kuona ngati ndimwe woyenelela kuti mukabatizike. Mungacite bwino kuyamba kuyaŵelenga mafunso amenewo monga mbali ya phunzilo lanu laumwini.

Podzikonzekeletsa makambilano amenewo, muziŵelenganso Malemba ogwila mawu na kuwasinkha-sinkha. Mungamalembenso manotsi m’buku lino kapena pena pake. Pokambilana na akulu mafunso a ubatizo, mungagwilitsile nchito manotsi amenewo, ndipo buku lino lingakhale lotsegula. Ngati mafunso ena akukuvutani kumvetsetsa, pemphani thandizo kwa amene amakuphunzitsani Baibo, kapena kwa akulu.

Pofunsidwa mafunso amenewo na akulu, simufunika kupeleka mayankho atali-atali kapena ocolowana ayi. Mayankho aafupi, acindunji, komanso osacita kuŵelenga, ndiwo abwino koposa. Poyankha mafunso, ni bwinonso nthawi zambili kuchulako Lemba limodzi kapena aŵili, monga maziko a mayankho anu.

Ngati kwapezeka kuti cidziŵitso canu pa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo sicinafikepo kweni-kweni, musade nkhawa kwambili. Akulu adzakonza zakuti muthandizidwe kuti muzitha kufotokoza mwekha tanthauzo la Malemba, n’colinga cakuti mukayenelezedwe kukabatizika panthawi ina.

[Cidziŵitso kwa akulu a mpingo: Malangizo opendela ofalitsa amene anafunsila ubatizo ali pa masamba 208-212.]

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani