LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Gawo 1: Zimene ife Akhristu Timakhulupilila
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
    • MAFUNSO KWA OFUNSILA UBATIZO

      Gawo 1: Zimene ife Akhristu Timakhulupilila

      Cifukwa cophunzila Baibo na Mboni za Yehova, mwadziŵa coonadi ca m’Baibo. Mosakayika, zimene mwaphunzila zakuthandizani kukhala pa ubale wabwino na Mulungu, ndipo mwakhala na ciyembekezo ca umoyo wa madalitso m’paradaiso pano padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu. Cikhulupililo canu m’Mawu a Mulungu calimba, ndipo poyanjana na mpingo wacikhristu, munayamba kale kulandila madalitso ambili. Mwafika pomvetsetsa mmene Yehova amacitila zinthu na anthu ake lelo lino.—Zek. 8:23.

      Pamene mukonzekela za ubatizo lomba, mudzapindula pokambilana na akulu a mpingo ziphunzitso zoyambilila zacikhristu. (Aheb. 6:1-3) Yehova apitilize kudalitsa zoyesa-yesa zanu zofuna kumudziŵa bwino, kuti pothela pake mukalandile mphoto imene analonjeza.—Yoh. 17:3.

      1. Kodi n’cifukwa ciani mufuna kubatizika?

      2. Kodi Yehova ndani?

      • “Yehova ndiye Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi. Palibenso wina.”—Deut. 4:39.

      • “Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”—Sal. 83:18, BL.

      3. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti muzilichula dzina la Mulungu?

      • “Koma inu muzipemphela motele: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.’”—Mat. 6:9.

      • “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Aroma 10:13.

      4. Kodi Baibo imachula Yehova na mawu ena ati omufotokoza?

      • “Yehova, Mlengi wa malekezelo a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.—Yes. 40:28.

      • “Atate wathu wakumwamba.”—Mat. 6:9.

      • “Mulungu ndiye cikondi.”—1 Yoh. 4:8.

      5. Kodi Yehova Mulungu mungam’patse ciani?

      • “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.”—Maliko 12:30.

      • “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.”—Luka 4:8.

      6. N’cifukwa ciani mufuna kukhala wokhulupilika kwa Yehova?

      • “Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miy. 27:11.

      7. Kodi mumapemphela kwa ndani? Nanga mumapemphela m’dzina la ndani?

      • “Ndithudi [ine Yesu] ndikukuuzani, ngati mupempha ciliconse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yoh. 16:23.

      8. Ni zinthu zina ziti zimene mungapemphelele?

      • “Koma inu muzipemphela motele: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano. Mutipatse ife lelo cakudya cathu ca lelo. Mutikhululukile zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukila amene atilakwila. Musatilowetse m’mayeselo, koma mutilanditse kwa woipayo.’”—Mat. 6:9-13.

      • “Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.”—1 Yoh. 5:14.

      9. N’cifukwa ciani nthawi zina Yehova sangamvele mapemphelo a munthu?

      • “Adzafuulila Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha. Adzawabisila nkhope yake pa nthawi imeneyo cifukwa ca zoipa zimene anali kucita.”—Mika 3:4.

      • “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzelo lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyila anthu ocita zoipa.”—1 Pet. 3:12.

      10. Kodi Yesu Khristu ndani?

      • “Poyankha, Simoni Petulo ananena kuti: ‘Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.’”—Mat. 16:16.

      11. Kodi Yesu anabwela kudzacita ciani padziko lapansi?

      • “Mwana wa munthu sanabwele kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila ndi kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.”—Mat. 20:28.

      • “Ndiyenela [ine Yesu] kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.”—Luka 4:43.

      12. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumayamikila nsembe imene Yesu anapeleka?

      • “Iye anafelanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafela n’kuukitsidwa.”—2 Akor. 5:15.

      13. Kodi Yesu ali na ulamulilo waukulu bwanji?

      • “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”—Mat. 28:18.

      • “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomela mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.”—Afil. 2:9.

      14. Kodi mukhulupilila kuti Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova ndilo “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” amene Yesu anamusankha?

      • “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa cakudya pa nthawi yoyenela?”—Mat. 24:45.

      15. Kodi mzimu woyela n’ciani?

      • “Poyankha mngeloyo anauza Mariya kuti: ‘Mzimu woyela udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa cifukwa cimenecinso, wodzabadwayo adzachedwa woyela, Mwana wa Mulungu.’”—Luka 1:35.

      • “Conco ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.

      16. Kodi Yehova wakhala akuugwilitsila nchito motani mzimu woyela?

      • “Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova, ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.”—Sal. 33:6.

      • “Koma mzimu woyela ukadzafika pa inu, mudzalandila mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—Mac. 1:8.

      • “Coyamba, mukudziwa kuti ulosi wa m’Malemba sucokela m’maganizo a munthu. Cifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.”—2 Pet. 1:20, 21.

      17. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani?

      • “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Dan. 2:44.

      18. Kodi Ufumu wa Mulungu udzakucitilani zabwino zotani?

      • “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chiv. 21:4.

      19. Nanga mudziŵa bwanji kuti madalitso a Ufumuwo ali pafupi?

      • “Ophunzila anafika kwa iye mwamseli ndi kunena kuti: ‘Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti, ndipo cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciani?’ Poyankha Yesu ananena kuti: ‘. . . Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.’”—Mat. 24:3, 4, 7, 14.

      • “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale awo, osafuna kugwilizana ndi anzawo, onenela anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, aciwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipeleka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe.”—2 Tim. 3:1-5.

      20. Kodi mumaonetsa bwanji kuti Ufumuwo ni wofunika kwambili kwa imwe?

      • “Cotelo pitilizani kufunafuna Ufumu coyamba ndi cilungamo cake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mat. 6:33.

      • “Yesu anauza ophunzila ake kuti: ‘Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikilapo ndipo anditsatile mosalekeza.’”—Mat. 16:24.

      21. Kodi Satana ndani? Nanga ziŵanda n’ciani?

      • “Inu ndinu ocokela kwa atate wanu Mdyelekezi, . . . Iyeyo ndi wopha anthu ciyambile kupanduka kwake.”—Yoh. 8:44.

      • “Cinjokaco cinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”—Chiv. 12:9.

      22. Kodi Satana ananeneza ciani Yehova? Nanga olambila Mulungu amawaneneza zotani?

      • “Mkaziyo anayankha njokayo kuti: ‘Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.”’ Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: ‘Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.’”—Gen. 3:2-5.

      • “Satana anamuyankha Yehova kuti: ‘Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolele kupeleka ciliconse cimene ali naco kuti apulumutse moyo wake.’”—Yobu 2:4.

      23. Kodi mungaonetse bwanji kuti zinenezo za Satana n’zabodza?

      • “Um’tumikile [Mulungu] ndi mtima wathunthu.”—1 Mbiri 28:9.

      • “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.

      24. Kodi n’cifukwa ciani anthu amafa?

      • “Ndiye cifukwa cake monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.”—Aroma 5:12.

      25. Kodi anthu akufa ali mu mkhalidwe wabwanji?

      • “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa ciliconse.”—Mlal. 9:5.

      26. Kodi pali ciyembekezo canji kwa amene anamwalila?

      • “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Mac. 24:15.

      27. Kodi ni anthu angati amene adzapita kumwamba kukalamulila pamodzi na Yesu?

      • “Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa ataimilila paphili la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.”—Chiv. 14:1.

  • Gawo 2: Umoyo Wacikhristu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
    • MAFUNSO KWA OFUNSILA UBATIZO

      Gawo 2: Umoyo Wacikhristu

      Pa kuphunzila kwanu Baibo, mwadziŵa zimene Yehova amafuna kuti muzicita, na mmene mungamatsatilile miyezo yake yolungama. Cifukwa ca zimene mwaphunzila, muyenela kuti munasintha kale zinthu zambili mu umoyo wanu, komanso mmene mumaonela moyo. Popeza kuti munatsimikiza mtima kuti muziyendela miyezo ya Yehova yolungama, ndimwe woyenelela kukhala mtumiki wa uthenga wabwino.

      Kukambilana mafunso otsatilawa kudzakuthandizani kukumbukila bwino miyezo ya Yehova yolungama, ndipo kudzakukumbutsani zimene mungacite kuti mukhale mtumiki wake wovomelezeka. Mudzaonanso kufunika kocita zinthu zonse na cikumbumtima cabwino polemekeza Yehova.—2 Akor. 1:12; 1 Tim. 1:19; 1 Pet. 3:16, 21.

      Pamene mwafika apa lomba m’kuphunzila kwanu, mosakayikila ndimwe wofunitsitsa kugonjela ulamulilo wa Yehova, na kukhala m’gulu lake. Mafunso otsatilawa pamodzi na Malemba ake, adzakuthandizani kuona mmene mumagonjelela makonzedwe a Yehova, kaya ni mumpingo, m’banja, kapena kwa olamulila andale adziko. Ndithudi, mudzayamikila kwambili makonzedwe a Yehova ophunzitsa anthu ake na kuwalimbikitsa mwauzimu. Makonzedwe amenewa akuphatikizapo misonkhano ya mpingo imene mumapezekapo na kutengapo mbali.

      Kuwonjezela apo, gawo limeneli lidzaonetsanso kufunika kotengako mbali nthawi zonse m’nchito yolalikila za Ufumu, kuthandiza anthu kuti adziŵe Yehova na zimene akucitila mtundu wa anthu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Comalizila, mudzamvetsa bwino kufunika kwa kudzipatulila kwanu kwa Yehova Mulungu na ubatizo wanu. Dziŵani ndithu kuti Yehova ni wokondwa kwambili na mmene mwalabadilila cisomo cimene wakuonetsani.

      1. Kodi Yehova amavomeleza cikwati cotani? Kodi pali maziko okha ati olola anthu kusudzulana mwa Malemba?

      • “Kodi simunawelenge kuti amene analenga anthu pa ciyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa cifukwa cimeneci mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiliwo adzakhala thupi limodzi’? Cotelo salinso awili, koma thupi limodzi. Conco cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse. . . . Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatila wina wacita cigololo, kupatulapo ngati wamusiya cifukwa ca dama.”—Mat. 19:4-6, 9.

      2. N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi amene akukhala pamodzi afunika kukhala okwatilana mwalamulo? Ngati muli pa cikwati, kodi cikwati canu cilidi covomelezeka mwalamulo?

      • “Pitiliza kuwakumbutsa kuti azigonjela ndi kumvela maboma ndiponso olamulila.”—Tito 3:1.

      • “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatilana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweluza adama ndi acigololo.”—Aheb. 13:4.

      3. Kodi mbali yanu m’banja ni iti?

      • “Mwana wanga, tamvela malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.”—Miy. 1:8.

      • “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo, . . . Amuna inu, pitilizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondela mpingo.”—Aef. 5:23, 25.

      •“Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalele m’malangizo a Yehova kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”—Aef. 6:4.

      • “Ananu, muzimvela makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kucita zimenezi kumakondweletsa Ambuye.”—Akol. 3:20.

      • “Inu akazi, muzigonjela amuna anu.”—1 Pet. 3:1.

      4. N’cifukwa ciani tiyenela kulemekeza moyo?

      • “Ndi iyeyo [Mulungu] amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. . . . Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”—Mac. 17:25, 28.

      5. N’cifukwa ciani kupha munthu aliyense ni chimo, ngakhale mwana ali m’mimba?

      • “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambili mkazi wapakati moti . . . wina wamwalila, pamenepo uzipeleka moyo kulipila moyo.”—Eks. 21:22, 23.

      • “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale ciwalo cimodzi cimene cinali citapangidwa.”—Sal. 139:16.

      • “Yehova amadana [ndi] . . . manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.”—Miy. 6:16, 17.

      6. Kodi lamulo la Mulungu limati ciani pa nkhani ya magazi?

      • ‘Pitilizani kupewa . . . magazi [ndi] zopotola.’—Mac. 15:29.

      7. N’cifukwa ciani tiyenela kuwakonda abale na alongo athu acikhristu?

      • “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana. Mwakutelo, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:34, 35.

      8. Pofuna kupewa kupatsila ena matenda, amene angakhale akupha: (a) N’cifukwa ciani munthu wodwala sayenela kuonetsa cikondi mwa kukumbatila anthu ena? (b) Ndipo n’cifukwa ciani sayenela kukhumudwa ngati ena samuitanila kunyumba kwawo? (c) Ngati munthu analiko paciwopsezo cotenga matenda oyambukila, n’cifukwa ciani pa iye yekha afunika kukapimitsa magazi asanayambe cibwenzi? (d) Ngati munthu ali na matenda oyambukila pamene akukonzekela ubatizo, n’cifukwa ciani ayenela kudziŵitsa mgwilizanitsi wa bungwe la akulu za matendawo asanabatizike?

      • “Musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, . . . ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’ Cikondi sicilimbikitsa munthu kucitila zoipa mnzake.”—Aroma 13:8-10.

      • “Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.”—Afil. 2:4.

      9. N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizikhululukila ena?

      • “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.”—Akol. 3:13.

      10. Kodi muyenela kucita ciani ngati m’bale kapena mlongo wakukambilani misece, kapena kukubelani mokugwilani m’maso, kapena kuti mwaukathyali?

      • “Ngati m’bale wako wacimwa, upite kukam’fotokozela colakwaco panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvela, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo. Koma akapanda kukumvela, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awili, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwili kapena zitatu. Akapanda kuwamvela amenewanso, uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvela mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wocokela mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.”—Mat. 18:15-17.

      11. Kodi Yehova amawaona bwanji macimo awa?

      ▪ Ciwelewele

      ▪ Kuseŵenzetsa zifanizo polambila

      ▪ Mathanyula

      ▪ Kuba

      ▪ Njuga

      ▪ Kuledzela

      • “Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musasoceletsedwe. Adama, opembedza mafano, acigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akor. 6:9, 10.

      12. Pa nkhani ya ciwelewele, comwe cimaphatikizapo cigololo na macitidwe alionse akugonana kunja kwa cikwati, kodi ndimwe wokonzeka kucita ciani?

      • “Thaŵani dama.”—1 Akor. 6:18.

      13. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa fodya kapena amkolabongo a mtundu uliwonse?

      • “Mupeleke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyela ndi yovomelezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwilitsa nchito luntha la kuganiza. Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.”—Aroma 12:1, 2.

      14. Kodi ni macita-cita ati auciwanda amene Mulungu amaletsa?

      • “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosela, wocita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsila kwa wolankhula ndi mizimu, wolosela zam’tsogolo kapena aliyense wofunsila kwa akufa.”—Deut. 18:10, 11.

      15. Ngati munthu wacita chimo lalikulu koma afuna kubwelela kwa Yehova, kodi ayenela kucita ciani mwamsanga?

      • “Ndinaulula chimo langa kwa inu, ndipo sindinabise colakwa canga. Ndinati: ‘Ndidzaulula kwa Yehova macimo anga.’”—Sal. 32:5.

      •“Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupemphelele ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphelo la cikhulupililo lidzacilitsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anacita macimo, adzakhululukidwa.”—Yak. 5:14, 15.

      16. Mukadziŵa kuti Mkhristu mnzanu anacita chimo lalikulu, kodi muyenela kucita ciani?

      • “Munthu akaona wina akucita chimo, kapena wamva kuti wina wacita chimo, munthu ameneyo ndi mboni. Akamva cilengezo kuti akacitile umboni za wocimwayo koma iye osapita kukanena, ndiye kuti wacimwa. Ayenela kuyankha mlandu wa colakwa cakeco.”—Lev. 5:1.

      17. Cilengezo cikapelekedwa cakuti uje salinso Mboni ya Yehova, kodi tiyenela kucita naye motani?

      • “Muleke kuyanjana ndi aliyense wochedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, cidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu woteleyu ayi.”—1 Akor. 5:11.

      • “Wina akabwela kwa inu ndi ciphunzitso cosiyana ndi ici, musamulandile m’nyumba zanu kapena kumupatsa moni.”—2 Yoh. 10.

      18. N’cifukwa ciani mabwenzi anu abwino ayenela kukhala aja okonda Yehova?

      • “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miy. 13:20.

      •“Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akor. 15:33.

      19. N’cifukwa ciani a Mboni za Yehova satengako mbali m’zandale?

      • “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine [Yesu] sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.

      20. N’cifukwa ciani muyenela kumvela boma?

      • “Munthu aliyense azimvela olamulila akuluakulu, cifukwa palibe ulamulilo umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulila amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1.

      21. Ngati lamulo la anthu lawombana na lamulo la Mulungu, kodi mungacite ciani?

      • “Tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Mac. 5:29.

      22. Posankha nchito, ni malemba ati angakuthandizeni kukhalabe wolekana nalo dziko?

      • “Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunzilanso nkhondo.”—Mika 4:3.

      • “Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu] anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye macimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandila nawo ina ya milili yake.”—Chiv. 18:4.

      23. Kodi muyenela kusankha zosangalatsa na zosangulutsa za mtundu wanji? Ndipo muyenela kupewa za mtundu uti?

      •“Yehova . . . amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.”—Sal. 11:5.

      • “Nyansidwani ndi coipa, gwilitsitsani cabwino.”—Aroma 12:9.

      • “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambili, zilizonse zolungama, zilizonse zoyela, zilizonse zacikondi, zilizonse zoyamikilika, khalidwe labwino lililonse, ndi ciliconse cotamandika, pitilizani kuganizila zimenezi.”—Afil. 4:8.

      24. N’cifukwa ciani a Mboni za Yehova salambilako pamodzi na zipembedzo zina?

      • “Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.”—1 Akor. 10:21.

      • “‘Tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watelo Yehova. ‘Musakhudze cinthu codetsedwa,’ ‘ndipo ndidzakulandilani.’”—2 Akor. 6:17.

      25. Pa nkhani ya zikondwelelo, ni mfundo ziti zingakuthandizeni kuona ngati muyenela kutengako mbali kapena ayi?

      • “Iwo anayamba kusakanikilana ndi mitundu ina, ndi kuyamba kuphunzila zocita zawo. Anayamba kutumikila mafano awo, ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.”—Sal. 106:35, 36.

      • “Akufa sadziwa ciliconse.”—Mlal. 9:5.

      • “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.

      • “Pakuti nthawi imene yapitayi inali yokwanila kwa inu kucita cifunilo ca anthu a m’dzikoli pamene munali kucita zinthu zosonyeza khalidwe lotayilila, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitilila muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”—1 Pet. 4:3.

      26. Kodi zitsanzo za m’Baibo zimakuthandizani bwanji pa nkhani yokondwelela tsiku la kubadwa?

      • “Tsiku lacitatulo linafika, ndipo linali tsiku lokumbukila kubadwa kwa Farao. Mfumuyo inakonzela phwando anchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa m’ndende mkulu wa opelekela cikho ndi mkulu wa ophika mkate, n’kuwaimika pamaso pa anchito ake onse. Farao anabwezeladi pa nchito mkulu wa opelekela cikho uja, . . . Koma mkulu wa ophika mkate anam’pacika.”—Gen. 40:20-22.

      • “Tsiku lokumbukila kubadwa kwa Herode litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa Herode kwambili, mwakuti analonjeza molumbila kuti adzapatsa mtsikanayo ciliconse cimene angapemphe. Tsopano mtsikanayu, mayi wake atacita kum’pangila, anapempha kuti: ‘Ndipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.’ Conco anatuma munthu kukadula mutu wa Yohane m’ndende.”—Mat. 14:6-8, 10.

      27. N’cifukwa ciani muyenela kumvela malangizo a akulu?

      • “Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela. Iwo amayang’anila miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvela ndi kuwagonjela kuti agwile nchito yawo mwacimwemwe, osati modandaula, pakuti akatelo zingakhale zokuvulazani.”—Aheb. 13:17.

      28. N’cifukwa ciani n’kofunika kwambili kuti imwe, komanso banja lanu, muzipatula nthawi yoŵelenga Baibo na kuiphunzila nthawi zonse?

      • “Amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amawelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku. Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.”—Sal. 1:2, 3.

      29. N’cifukwa ciani mumakonda kupezeka ku misonkhano na kutengako mbali?

      • “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.”—Sal. 22:22.

      • “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizolowezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.”—Aheb. 10:24, 25.

      30. Kodi nchito yofunika kopambana imene Yesu anatipatsa kuti tiigwile ni nchito yanji?

      • “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”—Mat. 28:19, 20.

      31. Pocita zopeleka ku nchito ya Ufumu, kapena pothandiza abale na alongo athu, kodi Yehova amakondwela ngati ticita zimenezi na mtima wotani?

      •“Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.”—Miy. 3:9.

      • “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”—2 Akor. 9:7.

      32. Kodi ni mavuto otani amene Akhristu amayembekezela kukumana nawo?

      • “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa cifukwa ca cilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wawo. ‘Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizilani zoipa zilizonse cifukwa ca ine. Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.”—Mat. 5:10-12.

      33. N’cifukwa ciani ni mwayi wapadela kubatizika n’kukhala Mboni ya Yehova?

      • “Mawu anu amandikondweletsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimachedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu.”—Yer. 15:16.

  • Makambilano othela na ofunsila ubatizo
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
    • MAFUNSO KWA OFUNSILA UBATIZO

      Makambilano othela na ofunsila ubatizo

      Kaŵili-kaŵili, ubatizo umacitikila ku misonkhano yadela komanso yacigawo ya Mboni za Yehova. Nkhani ya ubatizo ikatha, mkambi amapempha opita ku ubatizo kuti aimilile na kuyankha mokweza mafunso aŵili awa:

      1. Kodi munalapa macimo anu, munadzipatulila kwa Yehova, komanso munalandila njila yake ya cipulumutso mwa Yesu Khristu?

      2. Kodi mukumvetsa kuti mukabatizika lelo, ndiye kuti mwakhala Mboni ya Yehova yeni-yeni, ndiponso mwaloŵa m’gulu lake la Yehova?

      Mmene opita ku ubatizo ayankhila motsimikiza mafunso amenewa, ndiye kuti ‘alengeza poyela’ kuti amakhulupilila dipo, komanso anadzipatulila kothelatu kwa Yehova. (Aroma 10:9, 10) Ofunsila ubatizo ayenela kuganizila mwapemphelo mafunso otsatilawa, kotelo kuti akawayankhe mocokela pansi pa mtima.

      Kodi munadzipatulila kwa Yehova mwa pemphelo, na kumulonjeza kuti mudzalambila iye yekha basi, ndipo cinthu cacikulu kopambana mu umoyo wanu cidzakhala kucita cifunilo cake? Kodi pali pano ndimwe wotsimikiza na mtima wonse kuti ndimwe wokonzeka kukabatizika pa msonkhano umene ukubwela?

      Kodi mavalidwe oyenelela ku ubatizo ni abwanji? (1 Tim. 2:9, 10; Yoh. 15:19; Afil. 1:10)

      Tiyenela kuvala ‘mwaulemu ndi mwanzelu’ ‘molemekeza Mulungu.’ Conco, opita ku ubatizo sayenela kuvala kovala konyayila koonetsa thupi, kapena covala colembedwa mawu olengeza zina zake kapena ojambulidwa zithunzi.Ayenela kuvala mwaudongo, mwaukhondo, komanso moyenelela cocitikaco.

      Kodi munthu ayenela kuonetsa khalidwe lotani pamene akubatizika? (Luka 3:21, 22)

      Ubatizo wa Yesu unapeleka citsanzo ca ubatizo wa Akhristu lelolino. Iye anazindikila kuti ubatizo ni sitepu yaikulu kwambili, ndipo anaonetsa izi mwa khalidwe lake pobatizika. Mwa ici, malo a ubatizo si ocitilako nthabwala zosayenela, maseŵela, kunyaya, kapena khalidwe lililonse limene lingacotsele ulemu cocitikaco. Komanso Mkhristu watsopanoyo sayenela kusangalala mocita kunyanya ngati kuti wapata cikho. Ngakhale kuti ubatizo ni cocitika cosangalatsa, cisangalaloco ticionetse mwaulemu wake.

      Kodi kupezeka ku misonkhano nthawi zonse, komanso kuyanjana na mpingo, kudzakuthandizani bwanji kutumikilabe monga wodzipatulila kwa Yehova?

      Mukabatizika, n’cifukwa ciani mudzafunika kukhala na pulogilamu yabwino ya phunzilo laumwini, na kumapita mu ulaliki nthawi zonse?

      MALANGIZO KWA AKULU A MPINGO

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani