LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 12
  • Kodi Nchito Yathu Yolalikila Ufumu Imacitika Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Nchito Yathu Yolalikila Ufumu Imacitika Bwanji?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse Kuti Akhale Ophunzila”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Kodi Uthenga Wabwino Umalalikidwa Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 12

PHUNZILO 12

Kodi Nchito Yathu Yolalikila Ufumu Imacitika Bwanji?

Mboni za Yehova zilalikila kunyumba ndi nyumba

Ku Spain

Wa Mboni za Yehova akulalikila mu paki

Ku Belarus

Wa Mboni za Yehova akulalikila pa foni

Ku Hong Kong

Mboni za yehova zili mu ulaliki

Ku Peru

Yesu anakamba kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” Anakamba zimenezi imfa yake itayandikila. (Mateyu 24:14) Kodi nchito yolalikila padziko lonse lapansi imeneyi ikanatheka bwanji? Ikanatheka mwa kutsatila citsanzo cimene Yesu anasiya pamene anali padziko lapansi.—Luka 8:1.

Timafikila anthu kunyumba zao. Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kulalikila uthenga wabwino nyumba ndi nyumba. (Mateyu 10:11-13; Machitidwe 5:42; 20:20) Alaliki a m’zaka za zana loyamba amenewo anapatsidwa magao olalikilamo. (Mateyu 10:5, 6; 2 Akorinto 10:13) Ngakhale masiku ano, nchito yathu yolalikila imacitika mwadongosolo, ndipo mpingo ulionse umakhala ndi gao. Zimenezi zimatithandiza kumvela lamulo la Yesu lakuti “tilalikile kwa anthu ndi kupeleka umboni wokwanila.”—Machitidwe 10:42.

Timayesetsa kufikila anthu kulikonse kumene angapezeke. Yesu anapelekanso citsanzo mwa kulalikila kwa anthu kumalo osiyana-siyana, monga m’mbali mwa nyanja kapena pacitsime. (Maliko 4:1; Yohane 4:5-15) Nafenso timakambitsilana ndi anthu za m’Baibo kulikonse kumene tingawapeze—m’miseu, m’malo amalonda, m’mapaki, kapena pafoni. Tikakhala ndi mpata wabwino, timalalikilanso anansi athu, anzathu a kunchito, anzathu a kusukulu, ndi acibanja. Njila zonse izi zathandiza kuti mamiliyoni a anthu padziko lonse lapansi amve “uthenga wabwino wa cipulumutso.”—Salimo 96:2.

Kodi ndani amene mungafune kuuzako uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzawacitila mtsogolo? Musawamane uthenga wa ciyembekezo umenewu. Auzeni mwamsanga!

  • Kodi “uthenga wabwino” umene tiyenela kulalikila ni uthenga wanji?

  • Kodi Mboni za Yehova zimatsatila bwanji citsanzo ca Yesu polalikila?

DZIŴANI ZAMBILI

Pemphani mphunzitsi wanu wa Baibo kuti akuonetseni mmene mungauzileko anzanu mwanzelu zimene mukuphunzila m’Baibo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani