Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?
Kodi dziko lathu . . .
lidzakhala mmene lililimu?
lidzaipilatu?
lidzakhala bwino?
ZIMENE BAIBO IMANENA
“Mulungu. . . adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4, Baibulo la Dziko Latsopano.
UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI
Mudzakhala ndi nchito yabwino ndi yokhutilitsa.—Yesaya 65:21-23.
Simudzadwalanso kapena kuvutika mwa njila iliyonse.—Yesaya 25:8; 33:24.
Mudzakhala ndi moyo wabwino kwamuyaya, inu ndi banja lanu ndi mabwenzi anu.—Salimo 37:11, 29.
KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?
Inde, pa zifukwa ziŵili izi:
Mulungu ali ndi mphamvu yokwanilitsa lonjezo limeneli. M’Baibo, ndi Yehova Mulungu yekha amene amachedwa kuti “Wamphamvuyonse,” cifukwa cakuti ali ndi mphamvu zopanda malile. (Chivumbulutso 15:3) Conco, iye sangalephele ngakhale pang’ono kukwanilitsa lonjezo lake lakuti adzasintha dziko lathu kuti likhale labwino, pakuti Baibo imanena kuti “zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”—Mateyu 19:26.
Mulungu amafunitsitsa kukwanilitsa lonjezo limeneli. Mwacitsanzo, Yehova ‘amalakalaka’ kuukitsa anthu amene anamwalila.—Yobu 14:14, 15.
Baibo imakambanso kuti Yesu, Mwana wa Mulungu, anacilitsa odwala. N’cifukwa ciani anacita zimenezo? Cifukwa cakuti n’zimene iye anali kufuna. (Maliko 1:40, 41) Monga Atate wake, Yesu anali wofunitsitsa kuthandiza anthu ovutika.—Yohane 14:9.
Conco, sitikukaika kuti onse aŵili, Yehova ndi Yesu, amafuna kutithandiza kuti tikakhale ndi moyo wabwino mtsogolo.—Salimo 72:12-14; 145:16; 2 Petulo 3:9.
GANIZILANI FUNSO ILI
Kodi Mulungu adzasintha bwanji dziko lathu kuti likhale labwino?
Baibo imayankha funso limenelo pa MATEYU 6:9, 10 ndi pa DANIELI 2:44.