Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?
Kodi muganiza kuti ndi . . .
Mulungu?
anthu?
wina wake?
ZIMENE BAIBO IMANENA
“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.
“Mwana wa Mulungu anabwela . . . kuti aononge nchito za Mdyelekezi.”—1 John 3:8, New Century Version.
UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI
Mudzamvetsetsa cifukwa cake padziko pali mavuto.—Chivumbulutso 12:12.
Mudzakhala ndi ciyembekezo cakuti zinthu padziko zidzakhala bwino mtsogolo.—1 Yohane 2:17.
KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?
Inde, pa zifukwa zitatu izi:
Ulamulilo wa Satana udzaonongedwa. Yehova ndi wokonzeka kwambili kucotsa ulamulilo wa Satana padziko lapansi. Iye walonjeza kuti ‘adzaononga Mdyelekezi’ ndi kukonzanso zinthu zonse zimene Satana waononga.—Aheberi 2:14, Baibulo la Dziko Latsopano.
Mulungu wasankha Yesu Kristu kukhala wolamulila wa dziko. Yesu ndi wosiyana kwambili ndi wolamulila wa dzikoli amene ndi wankhanza ndi wodzikonda. Ponena za ulamulilo wa Yesu, Mulungu walonjeza kuti: “Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka . . . Adzaombola miyoyo yao ku cipsinjo ndi ciwawa.”—Salimo 72:13, 14.
Mulungu sanama. Baibo imakamba mosapita m’mbali kuti: “N’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Aheberi 6:18) Yehova akalonjeza zinthu, zimakhala monga kuti zacitika kale. (Yesaya 55:10, 11) ‘Wolamulila wa dzikoli adzaponyedwa kunja.’—Yohane 12:31.
GANIZILANI FUNSO ILI
Kodi dzikoli lidzakhala bwanji wolamulila wake akacotsedwapo?
Baibo imayankha funso limeneli pa SALIMO 37:10, 11 ndi pa CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.