LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • T-30 masa. 1-4
  • Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
  • Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?
    Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?
  • Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?
    Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?
    Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?
  • Kodi Mavuto Adzathadi?
    Kodi Mavuto Adzathadi?
Onaninso Zina
Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
T-30 masa. 1-4

Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?

Kodi mumaiona ngati . . .

  • buku la anthu?

  • buku la nthano?

  • buku locokela kwa Mulungu?

ZIMENE BAIBO IMANENA

“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.”—2 Timoteyo 3:16, Baibulo la Dziko Latsopano.

UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI

Mudzapeza mayankho okhutilitsa a mafunso ofunika kwambili onena za umoyo.—Miyambo 2:1-5.

Mudzapeza malangizo othandiza pa umoyo wa tsiku ndi tsiku.—Salimo 119:105.

Mudzakhala ndi ciyembekezo codalilika ca umoyo wabwino mtsogolo.—Aroma 15:4.

Mkazi ndi mwamuna onse aŵelenga Baibo; banja lacimwemwe lili panja likusangalala pamodzi

KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?

Inde, pa zifukwa zitatu izi:

  • Nkhani zake n’zogwilizana. Baibo inalembedwa ndi anthu osiyana-siyana okwanila 40 kwa zaka zopitilila 1,600. Ndipo ambili a io sanakumanepo. Koma Baibo yonse ndi yogwilizana, ndipo ili ndi mfundo yaikulu imodzi.

  • Alembi ake anali oona mtima. Olemba mbili kaŵili-kaŵili salemba zoona ngati anthu ao agonjetsedwa. Koma alembi a Baibo anali oona mtima, cakuti analemba zolakwa zao ndi za mtundu wao.—2 Mbiri 36:15, 16; Salimo 51:1-4.

  • Ulosi wake ndi wodalilika. Kukali zaka 200, Baibo inakambilatu kuti mzinda wakale wa Babulo udzaonongedwa. (Yesaya 13:17-22) Inafotokozanso mmene mzinda wa Babulo udzaonongedwela ndi dzina la amene adzaugonjetsa.—Yesaya 45:1-3.

    Maulosi ena ambili a m’Baibo naonso anakwanilitsidwa ndendende monga mmene Baibo inanenela. Kodi zimenezi si zimene timayembekezela ndi buku locokela kwa Mulungu?—2 Petulo 1:21.

GANIZILANI FUNSO ILI

Bambo, mayi, mwana wamwamuna ndi wamkazi

Kodi Mau a Mulungu angakuthandizeni kuti mukhale ndi umoyo wabwino kwambili?

Baibo imayankha funso limeneli pa YESAYA 48:17, 18 ndi pa 2 TIMOTEYO 3:16, 17.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani