PHUNZILO 10
Nthawi Zonse Yesu Anali Womvela
Kodi nthawi zina umavutika kumvela makolo ako?— Kumvela nthawi zina ndi kovuta. Kodi udziŵa kuti Yesu anali kumvela Yehova ndi makolo ake?— Citsanzo ca Yesu cingakuthandize kumvela makolo ako, ngakhale kuti zimenezo zingakhale zovuta. Tiye tiphunzile zambili pankhani imeneyi.
Yesu asanabwele padziko lapansi, anali kukhala kumwamba ndi Atate wake Yehova. Koma iye analinso ndi makolo padziko lapansi. Maina ao anali Yosefe ndi Mariya. Kodi udziŵa mmene io anakhalila makolo ake?—
Yehova anatenga moyo wa Yesu kumwamba ndi kuuika m’mimba mwa Mariya, kuti abadwe monga munthu padziko lapansi. Cimeneci cinali cozizwitsa! Yesu anakulila m’mimba mwa Mariya monga mmene ana ena amacitila. Pambuyo pa miyezi 9, Yesu anabadwa. Umu ndi mmene Mariya ndi Yosefe anakhalila makolo a Yesu padziko lapansi.
N’cifukwa ciani Yesu anali m’kacisi?
Pamene Yesu anakwanitsa zaka 12, iye anacita kanthu kena kosonyeza mmene anali kuwakondela Atate wake, Yehova. Izi zinacitika pamene Yesu ndi banja lake, anayenda ulendo wautali kukacita Pasika ku Yerusalemu. Pobwelela kwao, Yosefe ndi Mariya anafuna-funa Yesu koma sanamupeze. Kodi udziŵa kumene iye anali?—
Mofulumila Yosefe ndi Mariya anabwelela ku Yerusalemu kukafuna-funa Yesu. Iwo anavutika mtima kwambili cifukwa sanamupeze. Koma pambuyo pa masiku atatu io anam’peza m’kacisi. Kodi udziŵa cifukwa cake Yesu anali m’kacisi?— Cifukwa kumeneko iye anali kuphunzila za Atate wake, Yehova. Anali kukonda Yehova ndipo anafuna kuphunzila zimene angacite kuti azimusangalatsa. Ngakhale nthawi imene anakula, nthawi zonse Yesu anali kumvela Yehova. Yesu anali kumvela ngakhale pamene kucita zimenezo kunali kovuta ndipo kukanam’loŵetsa m’mavuto. Kodi Yesu anali kumvelanso Yosefe ndi Mariya?— Baibulo limanena kuti anali kuwamvela.
Kodi uphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yesu?— Ufunika kumvela makolo ako, ngakhale kuti zimenezo zingakhale zovuta. Kodi udzacita zimenezo?—
ŴELENGA M’BAIBULO LAKO
Aefeso 6:1
Aheberi 5:8