LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 72 tsa. 170-tsa. 171 pala. 2
  • Pamene Yesu Anali Wacicepele

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pamene Yesu Anali Wacicepele
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yesu Wacicepele Ali Mu Kacisi
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nthawi Zonse Yesu Anali Womvela
    Phunzitsani Ana Anu
  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 72 tsa. 170-tsa. 171 pala. 2
Yesu wa zaka 12 ali pakati pa aphunzitsi pakacisi

PHUNZILO 72

Pamene Yesu Anali Wacicepele

Yosefe na Mariya anali kukhala ku Nazareti pamodzi na Yesu, komanso ana ena aamuna ndi aakazi. Kuti asamalile banja lake, Yosefe anali kuseŵenza nchito yaukalipentala. Ndipo anali kuphunzitsa banja lake za Yehova na Cilamulo cake. Nthawi zonse, banja limeneli linali kupita ku sunagoge kukalambila. Komanso, caka ciliconse anali kupita ku Yerusalemu ku cikondwelelo ca Pasika.

Pamene Yesu anafika zaka 12, monga mwa nthawi zonse banja lawo linapanga ulendo wautali wopita ku Yerusalemu. Atafika, mu mzinda munali anthu ambili obwela ku cikondwelelo ca Pasika. Pambuyo pa cikondwelelo, Yosefe na Mariya anauyamba ulendo wobwelela kwawo. Iwo anaganiza kuti Yesu ali pakati pawo. Koma pamene anam’funa-funa sanam’peze.

Iwo anabwelela ku Yerusalemu, ndipo anasakila mwana wawo kwa masiku atatu. Potsilizila pake anapita ku kacisi. Anam’peza kumeneko. Anali pakati pa aphunzitsi, akuwamvetsela mwachelu na kuŵafunsa mafunso anzelu. Aphunzitsiwo anacita cidwi kwambili na Yesu cakuti nawonso anayamba kum’funsa mafunso. Ndipo anadabwa na mayankho ake. Anaona kuti Yesu anali kucidziŵa bwino Cilamulo ca Yehova.

Yosefe na Mariya anada nkhawa kwambili. Ndiyeno Mariya anati: ‘Iwe mwana iwe, tinali kukufuna-funa! Unali kuti?’ Yesu anayankha kuti: ‘Kodi simudziŵa kuti nifunika kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?’

Kenako Yesu anapita na makolo ake ku Nazareti. Yosefe anaphunzitsa Yesu nchito yaukalipentala. Kodi uganiza kuti Yesu anali munthu wotani pamene anali wacicepele? Pamene Yesu anali kukula, nzelu zake zinali kuwonjezeleka, ndipo anali kukondewa kwambili na Mulungu komanso anthu.

Yosefe na Mariya, komanso Yesu pamodzi ndi ena mwa abale ake aakazi ndi aamuna akhala pa thebulo

“Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga, ndipo cilamulo canu cili mumtima mwanga.”—Salimo 40:8

Mafunso: Kodi Yosefe na Mariya anam’peza kuti Yesu? Nanga anali kucita ciani kumeneko?

Mateyu 13:55, 56; Maliko 6:3; Luka 2:40-52; 4:16; Deuteronomo 16:15, 16

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani