LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 87
  • Yesu Wacicepele Ali Mu Kacisi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Wacicepele Ali Mu Kacisi
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Pamene Yesu Anali Wacicepele
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Nthawi Zonse Yesu Anali Womvela
    Phunzitsani Ana Anu
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 87

Nkhani 87

Yesu Wacicepele Ali Mu Kacisi

ONA kamnyamata aka kamene kakamba ndi anthu akulu-akulu. Akulu amenewa ni aphunzitsi mu kacisi wa Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo kamnyamata aka ni Yesu. Wakulako ndipo tsopano ali ndi zaka 12.

Aphunzitsi adabwa kwambili poona kuti Yesu adziŵa zinthu zambili za Mulungu ndi zinthu zolembedwa m’Baibo. Nanga n’cifukwa ciani Yosefe ndi Mariya sali pamenepa? Kodi io ali kuti? Tiye tione.

Caka ciliconse Yosefe amabwela ndi banja lake ku Yerusalemu ku cikondwelelo capadela ca Paska. Ni ulendo utali kucoka ku Nazareti kukafika ku Yerusalemu. Palibe amene ali ndi motoka, ndipo kulibe masitima oyenda pa njanji. M’masiku amenewa kulibe zinthu zimenezi. Anthu ambili amangoyenda pansi, ndipo amatenga pafupi-fupi masiku atatu kuti afike ku Yerusalemu.

Yosefe tsopano ali ndi banja lalikulu. Conco pali ang’ono a Yesu amuna ndi akazi amene afunika kuwasamalila. Caka cimeneci Yosefe ndi Mariya anyamuka ndi ana ao paulendo utali wobwelela kwao ku Nazareti. Iwo aganiza kuti Yesu ali pamodzi ndi anthu ena paulendo umenewo. Koma nthawi ya kumadzulo pamene onse aima, io samupeza Yesu. Amufuna-funa pakati pa acibanja ndi anzao, koma iye sali pamodzi nao! Conco abwelela ku Yerusalemu kuti akaone ngati watsala kumeneko.

Potsilizila pake, amupeza Yesu ku Yerusalemu ali ndi aphunzitsi. Iye amvetsela zimene akamba ndipo aŵafunsa mafunso. Anthu onse adabwa kuona nzelu zimene Yesu ali nazo. Koma Mariya akuti: ‘Mwanawe, n’cifukwa ciani wacita zimenezi? Ine ndi atate ako tinada nkhawa kwambili ndipo tinali kukufuna-funa.’

Yesu ayankha kuti: ‘Munali kunifuna-funa cifukwa ciani? Kodi simunadziŵe kuti niyenela kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?’

Inde, Yesu amakonda kukhala kumene angaphunzile mau a Mulungu. Ngakhale ife tiyenela kumva conco. Pamene anali kwao ku Nazareti, Yesu anali kukonda kuyenda kukalambila kumisonkhano mlungu uliwonse. Cifukwa cakuti nthawi zonse anali kumvetsela mwachelu, anaphunzila zinthu zambili za m’Baibo. Tiyenela kukhala monga Yesu ndi kutengela citsanzo cake.

Luka 2:41-52; Mateyu 13:53-56.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani