PHUNZILO 13
Timoteyo Anafunitsitsa Kuthandiza Anthu
Timoteyo anali mnyamata amene anali kukonda kuthandiza anthu. Anali kupita kumalo osiyana-siyana kuthandiza ena. Nchito imeneyi inamucititsa kuti akhale ndi umoyo wosangalatsa. Kodi ungafune kudziŵa za iye?—
Amai ake a Timoteyo ndi agogo ake anamuphunzitsa za Yehova
Timoteyo anakulila m’tauni yochedwa Lusitara. Pamene anali wamng’ono, ambuye ake a Loisi ndi amai ake a Yunike anamuphunzitsa za Yehova. Pamene Timoteyo anali kukula, iye anali wofunitsitsa kuthandiza anthu ena kuphunzila za Yehova.
Timoteyo akali wacinyamata, Paulo anamupempha kuti apite naye kukalalikila ku malo ena. Timoteyo anavomela, ndipo anali wokonzeka kupita kukathandiza ena.
Timoteyo anayenda ndi Paulo ku tauni ya Tesalonika m’dziko la Makedoniya. Coyamba io anafunika kuyenda ulendo wautali ndiyeno kukwela combo, kuti akafike kumeneko. Atafika kumeneko, io anathandiza anthu ambili kuphunzila za Yehova. Koma anthu ena kumeneko anakwiya ndipo anafuna kuwacitila zoipa. Conco, Paulo ndi Timoteyo anacokako ndi kupita kukalalikila kwina.
Timoteyo anali ndi umoyo wabwino komanso wosangalatsa
Patapita miyezi, Paulo anauza Timoteyo kubwelela ku Tesalonika kuti akaone mmene zinthu zinalili ndi abale. Iye anafunikila kulimba mtima kuti abwelele ku tauni yoopsa imeneyo. Koma Timoteyo anapita cifukwa anali kudela nkhawa kwambili abale kumeneko. Iye anabwelela kwa Paulo ndi nkhani yabwino yakuti abale ku Tesalonika akucita bwino kwambili.
Timoteyo ndi Paulo anagwila nchito pamodzi kwa zaka zambili. Nthawi ina, Paulo analemba kuti Timoteyo anali munthu woyenelela amene angam’tume kukalimbikitsa mipingo. Timoteyo anali kukonda Yehova ndi anthu.
Kodi iwe umakonda anthu?— Kodi ungafune kuwathandiza kudziŵa Yehova?— Ngati ucita zimenezo, udzakhala ndi umoyo wabwino ndi wosangalatsa monga mmene Timoteyo analili.
ŴELENGA M’BAIBULO LAKO
2 Timoteyo 1:5; 3:15
1 Atesalonika 3:2-7
Afilipi 2:19-22