LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 100 tsa. 232-tsa. 233 pala. 2
  • Paulo na Timoteyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Paulo na Timoteyo
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Timoteyo Anafunitsitsa Kuthandiza Anthu
    Phunzitsani Ana Anu
  • “Mwana Wanga Wokondedwa ndi Wokhulupilika mwa Ambuye”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Timoteyo—Mthandizi Watsopano Wa Paulo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Ika Mtima pa Utumiki Wako!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 100 tsa. 232-tsa. 233 pala. 2
Paulo, Sila, na Timoteyo

PHUNZILO 100

Paulo na Timoteyo

Yunike, Loisi, na wacicepele Timoteyo

Timoteyo anali m’bale wacicepele mu mpingo wa ku Lusitara. Atate ake anali Mgiriki ndipo amayi ake anali Myuda. Amayi ake a Yunike, na ambuye ake a Loisi, anam’phunzitsa za Yehova kuyambila ali wamng’ono.

Pamene Paulo anacezela mpingo wa ku Lusitara pa ulendo wake waciŵili, anaona kuti Timoteyo anali kukonda kwambili abale, ndipo anali kuwathandiza. Paulo anapempha Timoteyo kuti ayende naye pa ulendo umenewo. M’kupita kwa nthawi, Paulo anaphunzitsa Timoteyo kukhala mlaliki komanso mphunzitsi wabwino wa uthenga wabwino.

Mzimu woyela unatsogolela Paulo na Timoteyo kulikonse kumene anali kuyenda. Tsiku lina usiku, Paulo anaona masomphenya. M’masomphenyawo, munthu wina anauza Paulo kupita ku Makedoniya kuti akaŵathandize. Conco Paulo, Timoteyo, Sila, komanso Luka, anapita kukalalikila na kukhazikitsa mipingo.

Mu mzinda wa Tesalonika ku Makedoniya, amuna ndi akazi ambili anakhala Akhristu. Koma Ayuda ena anali kucitila nsanje Paulo na anzakewo. Iwo anatuntha cigulu ca anthu kuti aukile abalewo, ndipo anawagwila na kuŵapeleka kwa olamulila a mzinda. Anthuwo anali kufuula kuti: ‘Anthu awa ni adani a boma la Roma!’ Moyo wa Paulo na Timoteyo unali pa ciwopsezo. Cakuti anacita kuthaŵila ku Bereya usiku.

Anthu a ku Bereya anali ofunitsitsa kumvela uthenga wabwino. Ndipo Agiriki komanso Ayuda a kumeneko anakhala okhulupilila. Koma pamene Ayuda ena anabwela kucokela ku Tesalonika, iwo anayambitsa zaciwawa. Izi zinapangitsa Paulo kuthaŵila ku Atene. Paulo na Sila anakhalabe ku Bereya kuti alimbikitse abale. M’kupita kwa masiku, Paulo anatumizanso Timoteyo ku Tesalonika kuti akathandize abale kupilila cizunzo kumeneko. Pambuyo pake, Paulo anatumiza Timoteyo kuti akacezele mipingo ina yambili na kuilimbikitsa.

Mtumwi Paulo akukamba mawu pamene Timoteyo akum’lembela kalata, apo n’kuti ali paukaidi wosacoka panyumba, atam’manga unyolo womangidwanso kwa msilikali

Paulo anauza Timoteyo kuti: ‘Amene afuna kutumikila Yehova adzazunzidwa.’ Timoteyo anazunzidwa na kuponyedwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cake. Anauona kukhala mwayi wake woonetsa kuti ni wokhulupilika kwa Yehova.

Paulo anauza Afilipi kuti: ‘Natumiza Timoteyo kwa inu. Adzakuphunzitsani tanthauzo la kuyenda m’coonadi. Ndiponso adzakuphunzitsani zimene muyenela kucita polalikila.’ Paulo anali kum’dalila Timoteyo. Kwa zaka zambili, iwo anali kuseŵenzela pamodzi monga mabwenzi komanso atumiki a Mulungu.

“Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima. Pakuti ena onse akungofuna za iwo eni, osati za Khristu Yesu.”—Afilipi 2:20, 21

Mafunso: Kodi Timoteyo anali ndani? N’cifukwa ciani Paulo na Timoteyo anali kukondana?

Machitidwe 16:1-12; 17:1-15; Afilipi 2:19-22; 2 Timoteyo 1:1-5; 3:12, 14, 15; Aheberi 13:23

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani