LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • kr nkhani 20 nkhani 209-219
  • Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Nchito Yopeleka Thandizo Ndi “Utumiki Wopatulika”
  • Zolinga za Nchitoyi N’zodziŵikilatu
  • Utumiki Wopeleka Thandizo Umabweletsa Madalitso Okhalitsa
  • Kodi Mungagwile Nao Nchitoyi?
  • Mmene Tingathandizile Pakagwa Tsoka
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Thandizo pa Matsoka a mu 2021—Abale na Alongo Athu Sananyalanyazidwe
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Kucilikiza Ufumu—Kumanga Malo Olambilila ndi Kupeleka Thandizo Pakacitika Ngozi
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Kupeleka Thandizo kwa Anthu Okhudzidwa na Matsoka
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
Onaninso Zina
Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
kr nkhani 20 nkhani 209-219

NKHANI 20

Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Akristu oona amasonyezelana cikondi pakacitika ngozi

1, 2. (a) Ndi vuto lotani limene Akristu a ku Yudeya anakumana nalo? (b) Kodi Akristuwo anasonyezedwa cikondi m’njila yotani?

CA M’ma 46 C.E, ku Yudeya kunagwa njala yoopsa. Cakudya cinali cocepa ndiponso cokwela mtengo kwambili moti ophunzila a Kristu aciyuda a kumeneko anali kulephela kugula cakudyaco. Iwo anali kuvutika kwambili ndi njala. Koma Yehova anathandiza ophunzila a Kristu amenewo m’njila yapadela kwambili. Kodi anawathandiza bwanji?

2 Akristu aciyuda ndi a mitundu ina ku Antiokeya wa ku Siriya anakhudzidwa kwambili ndi mavuto amene Akristu aciyuda ku Yerusalemu ndi ku Yudeya anali kukumana nao. Iwo anasonkhanitsa ndalama zokathandizila abale ao. Kenako anasankha amuna aŵili oyenelela pakati pao, Baranaba ndi Saulo, kuti akapeleke thandizolo kwa akulu a mpingo ku Yerusalemu. (Ŵelengani Machitidwe 11:27-30; 12:25.) Taganizilani cisangalalo cimene abale osoŵa ku Yudeya anali naco ataona cikondi cimene abale ao ku Antiokeya anawasonyeza mwa kuwatumizila thandizo.

3. (a) Kodi anthu a Mulungu masiku ano amatsatilabe bwanji citsanzo ca Akristu a ku Antiokeya? Pelekani citsanzo. (Onani bokosi lakuti “Nchito Yathu Yaikulu Yoyamba Yopeleka Thandizo Masiku Ano.”) (b) Ndi mafunso ati amene tikambilane m’nkhani ino?

3 Zimenezi zinacitika m’nthawi ya atumwi, ndipo iyi ndi nthawi yoyamba imene Baibulo limafotokoza za Akristu amene anatumiza thandizo kwa Akristu anzao okhala m’dela lina. Masiku ano, timatsatila citsanzo ca abale athu a ku Antiokeya. Tikamva kuti ngozi yacitikila abale athu m’dela lina kapena akuzunzidwa, timawathandiza.a Kuti tidziŵe mmene nchito yopeleka thandizo imakhudzila utumiki wathu, tiyeni tikambilane mafunso atatu awa okhudza utumikiwu: N’cifukwa ciani timaona kuti nchito yopeleka thandizo ndi utumiki? Kodi colinga ca nchito yopeleka thandizo n’ciani? Nanga timapindula bwanji ndi utumiki wopeleka thandizo umenewu?

Nchito Yopeleka Thandizo Ndi “Utumiki Wopatulika”

4. N’ciani cimene Paulo anauza Akorinto ponena za utumiki wacikristu?

4 M’kalata yake yaciŵili yopita kwa Akorinto, Paulo ananena kuti utumiki wacikristu uli ndi mbali ziŵili zofunika. Ngakhale kuti kalatayi analembela Akristu odzozedwa, mau ake amakhudzanso “nkhosa zina” za Kristu. (Yoh. 10:16) Mbali yoyamba ya utumiki wathu ndi “utumiki wokhazikitsanso mtendele,” kapena kuti nchito yolalikila ndi kuphunzitsa. (2 Akor. 5:18-20; 1 Tim. 2:3-6) Mbali ina ndi utumiki umene timacita pothandiza okhulupilila anzathu. Paulo anakamba momveka bwino kuti umenewu ndi “utumiki wothandiza” ena. (2 Akor. 8:4) M’Baibulo muli mau akuti “utumiki wokhazikitsanso mtendele” ndi akuti “utumiki wothandiza” oyelawo. M’mau onsewa, liu lakuti “utumiki” linamasulidwa kucokela ku liu limodzi lacigiriki lakuti di·a·ko·niʹa. N’cifukwa ciani zimenezi n’zocititsa cidwi?

5. N’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kuti Paulo anakamba kuti nchito yopeleka thandizo ndi utumiki?

5 Mwa kugwilitsila nchito liu lacigiriki lofanana ponena za mautumiki aŵiliwo, Paulo anaonetsa kuti nchito yopeleka thandizo ndi yofanana ndi mautumiki ena amene anali kucitika mumpingo wacikristu. Asanakambe za mautumiki amenewa, iye anati: “Pali mautumiki osiyanasiyana, koma Ambuye ndi mmodzi. Palinso nchito zosiyanasiyana, . . . Koma nchito zonsezi, mzimu umodzimodziwo ndiwo umazicita.” (1 Akor. 12:4-6, 11) Paulo anasonyeza kuti mautumiki osiyanasiyana amene amacitika pampingo ndi “utumiki wopatulika.”b (Aroma 12:1, 6-8) Ndiye cifukwa cake iye anagwilitsila nchito nthawi yake ‘kutumikila oyela.’—Aroma 15:25, 26.

6. (a) Malinga ndi mau a Paulo, n’cifukwa ciani nchito yopeleka thandizo ndi mbali ya kulambila kwathu? (b) Fotokozani mmene nchito yathu yopeleka thandizo imacitikila padziko lonse masiku ano. (Onani chati cakuti “Pakacitika Ngozi,” patsamba 214.)

6 Paulo anathandiza Akristu a ku Korinto kuzindikila kuti nchito yopeleka thandizo ndi mbali ya kulambila Yehova, ndiponso kuti ndi mbali ya utumiki wao kwa Iye. Onani kuti iye anakamba kuti Akristu amene amapeleka thandizo amacita zimenezo cifukwa ‘cogonjela uthenga wabwino wonena za Kristu.” (2 Akor. 9:13) Conco, cimene cimalimbikitsa Akristu kuthandiza anzao ndi mtima wao wofuna kutsatila zimene Kristu anaphunzitsa. Paulo ananena kuti zinthu zabwino zimene Akristu amacitila abale ao zimaonetsa “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (2 Akor. 9:14; 1 Pet. 4:10) Conco, ponena za nchito yothandiza abale athu amene akuvutika, magazini ya Nsanja ya Olonda ya December 1, 1975 inati: “Tisakaikile kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Kristu amaona utumikiwu kukhala wofunika kwambili.” Zoonadi, nchito yopeleka thandizo ndi mbali yofunika kwambili ya utumiki wopatulika.—Aroma 12:1, 7; 2 Akor. 8:7; Aheb. 13:16.

Zolinga za Nchitoyi N’zodziŵikilatu

7, 8. Kodi colinga coyamba ca utumiki wathu wopeleka thandizo n’ciani? Fotokozani.

7 Kodi colinga ca utumiki wathu wopeleka thandizo pa nthawi yamavuto n’ciani? Paulo anayankha funso limenelo m’kalata yake yaciŵili yopita kwa Akorinto. (Ŵelengani 2 Akorinto 9:11-15.) Palembali, Paulo anafotokoza zolinga zitatu zimene timakwanilitsa tikamacita “utumiki wothandiza anthu” panthawi ya mavuto. Tiyeni tikambilane zolinga zimenezi.

8 Coyamba, utumiki umenewu umalemekeza Yehova. Onani kuti pa mavesi asanu a pa 2 Akorinto 9:11-15, Paulo anagwilitsila nchito mau angapo othandiza abale kuona mmene utumiki wopeleka thandizo umakhudzila Yehova Mulungu. Iye anawakumbutsa kuti utumikiwu umacititsa “anthu kuyamika Mulunguyo” ndiponso “kupeleka mapemphelo oculuka oyamika Mulungu.” (vesi 11 ndi 12) Anafotokozanso kuti nchito yopeleka thandizo imalimbikitsa Akristu ‘kulemekeza Mulungu’ ndi kuyamikila ‘kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.’ (vesi 13 ndi 14) Ndiyeno Paulo anamaliza nkhani yake yonena za kupeleka thandizo ndi mau akuti: “Tikuyamika Mulungu.”—Vesi 15; 1 Pet. 4:11.

9. Kodi nchito yopeleka thandizo ingathandize anthu kukhala ndi maganizo otani? Pelekani citsanzo.

9 Mofanana ndi Paulo, atumiki a Mulungu lelolino amaona nchito yopeleka thandizo kukhala mwai wao wolemekeza Yehova ndi kukometsela ciphunzitso cake. (1 Akor. 10:31; Tito 2:10) Ndipo nchitoyi imathandiza kwambili kucotsa maganizo olakwika amene anthu ena ali nao ponena za Yehova ndi Mboni zake. Mwacitsanzo, m’dela lina limene linakhudzidwa ndi cimphepo camkuntho, munali kukhala mai wina amene anali ataika cikwangwani pa citseko ca nyumba yake colembedwa kuti: “Pano Sitifuna a Mboni za Yehova.” Tsiku lina, maiyo anaona anthu opeleka thandizo pakacitika ngozi zacilengedwe akukonza nyumba ina pafupi ndi nyumba yake. Kwa masiku angapo, iye anali kuona anthuwo akugwila nchito limodzi mogwilizana. Kenako anapita pamalowo kukafunsa kuti anthuwo anali ndani. Atadziŵa kuti anali a Mboni za Yehova, anacita cidwi kwambili ndipo anati: “Sindinali kudziŵa kuti anthu inu ndinu otele.” Kodi maiyo anacita ciani pambuyo pake? Anacotsa cikwangwani cija pa citseko ca nyumba yake.

10, 11. (a) Ndi zitsanzo ziti zimene zikuonetsa kuti timakwanilitsa colinga caciŵili ca nchito yathu yopeleka thandizo? (b) Ndi kabuku kati kamene kamathandiza ogwila nchito yopeleka thandizo? (Onani kabokosi kakuti “Cida Cina Cothandiza Ogwila Nchito Yopeleka Thandizo.”)

10 Caciŵili, timapatsa okhulupilila anzathu “zinthu zoculuka zimene akufunikila.” (2 Akor. 9:12a) Ndife okonzeka kupatsa abale ndi alongo athu zosoŵa zao ndi kucepetsa mavuto ao. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anthu onse mumpingo amapanga ‘thupi limodzi,’ ndipo “ciwalo cimodzi cikavutika, ziwalo zina zonse zimavutikila naco limodzi.” (1 Akor. 12:20, 26) Cifukwa cokonda abale ndi alongo athu ndi kuwamvela cifundo, timacitapo kanthu mwamsanga tikamva kuti io akumana ndi vuto. Mofulumila, timatenga zida zofunika ndi kuthamangila kumene kwacitika ngozi kuti tikathandize Akristu anzathu. (Yak. 2:15, 16) Mwacitsanzo, mu 2011 pamene ku Japan kunacitika tsunami, ofesi ya nthambi ku United States inalembela kalata Makomiti Omanga Nyumba za Ufumu m’dzikolo. M’kalatayo, ofesiyo inapempha makomitiwo kuti apeze “abale ocepa oyenelela” amene angakonde kukathandiza pa nchito yomanganso Nyumba za Ufumu ku Japan. Kodi n’ciani cinacitika? Pa milungu yoŵelengeka cabe, abale ndi alongo odzipeleka pafupifupi 600 anapempha kuti akathandize, ndipo analipila okha ndalama zoyendela ku Japan pa ndeke. Ofesi ya nthambi ku United States inati: “Tasangalala kwambili ndi zimene abalewa acita.” M’bale wina ku Japan anafunsa mmodzi mwa ogwila nchito yopeleka thandizo amene anacokela ku dziko lina cifukwa cake anabwela kudzathandiza m’dzikolo. Iye anayankha kuti: “Abale athu kuno ku Japan ndi mbali ya ‘thupi lathu.’ Iwo akamavutika, ifenso timavutika.” Cifukwa ca cikondi codzimana, abale ndi alongo ogwila nchito yopeleka thandizo nthawi zina amaika moyo wao pangozi kuti athandize abale ao.c—1 Yoh. 3:16.

Wa Mboni za Yehova ku Switzerland akusonkhanitsa katundu wotumizila abale ake acikristu omwe ali kudela kumene kwagwa tsoka mu 1946

Ku Switzerland, mu 1946

NCHITO YATHU YAIKULU YOYAMBA YOPELEKA THANDIZO MASIKU ANO

MU September 1945, patapita miyezi yocepa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha ku Ulaya, M’bale Knorr analengeza za kuyamba kwa nchito yaikulu yotumiza “thandizo kwa abale osoŵa m’cigawo capakati ku Ulaya.”

Patapita milungu ingapo kucokela pamene anapeleka cilengezoco, a Mboni za Yehova ku Canada, ku United States, ndi ku maiko ena anayamba kulongedza zovala ndi cakudya zoti atumize kwa abale ao. Kuyambila mu January 1946, abale anayamba kutumiza katunduyo kwa Akristu anzao a ku Austria, Belgium, Bulgaria, China, Czechoslovakia, Denmark, England, Finland, France, Germany, Greece, Hungary, Italy, Netherlands, Norway, Philippines, Poland, ndi ku Romania.

Nchito yotumiza thandizo imeneyi sinacitike kwa masiku oŵelengeka cabe, koma inatenga zaka ziŵili ndi hafu. Panthawiyo, abale ndi alongo pafupifupi 85,000 anatumiza cakudya colemela makilogalamu oposa 300,000, zovala zolemela makilogalamu oposa 450,000, ndi nsapato zoposa 124,000 kwa abale ndi alongo ao m’madela amene zinthu zambili zinaonongeka cifukwa ca nkhondo. Pofika mu August 1948, nchito yaikulu yopeleka thandizo imeneyi inatha. Nsanja ya Mlonda ina yacingelezi ya mu 1949 inati: “Abale anaonetsanadi cikondi. Tikudziŵa kuti abale onse anacita zimenezi kuti Ambuye alemekezedwe. Iwo anazindikila kuti thandizo limeneli lidzacititsa ena kupitilizabe kulambila Mulungu. Conco, io anaona kuti ndi mwai waukulu kuthandiza abale ao mwanjila imeneyi.” Nchito yopeleka thandizo imeneyi inapangitsa kuti Yehova atamandidwe, inathandiza abale pa zosowa zao, ndiponso inalimbitsa mgwilizano pakati pa abale padziko lonse.

11 Naonso anthu amene si Mboni amayamikila nchito yathu yopeleka thandizo. Mwacitsanzo, pamene m’dela la Arkansas, ku United States kunacitika ngozi mu 2013, nyuzipepala ina inafotokoza mmene Mboni za Yehova zodzipeleka zinathandizila pangoziyo. Nyuzipepalayo inati: “Mboni za Yehova zimacita zinthu mwadongosolo kwambili ndiponso mofulumila.” Ndithudi, monga mmene mtumwi Paulo ananenela, timapeleka “zinthu zoculuka” kwa abale athu amene akuvutika.

12-14. (a) N’cifukwa ciani kukwanilitsa colinga cacitatu ca nchito yopeleka thandizo n’kofunika? (b) Ndi mau ati amene anthu ena anakamba oonetsa kufunika kopitilizabe kucita zinthu za kuuzimu?

12 Cacitatu, timathandiza ovutika kuyambanso kucita zinthu za kuuzimu. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika? Paulo anakamba kuti anthu amene alandila thandizo ngozi ikacitika amasonkhezeledwa “kupeleka mapemphelo oculuka oyamika Mulungu.” (2 Akor. 9:12b) Kunena zoona, cinthu cabwino kwambili cimene okhudzidwawo angacite kuti ayamikile Yehova ndi kuyambanso kucita zinthu za kuuzimu mwamsanga. (Afil. 1:10) Mu 1945, Nsanja ya Mlonda ina yacingelezi inati: “Paulo anavomeleza . . . kuti abale azipeleka zopeleka cifukwa cakuti zinali kuthandiza . . . Akristu osauka kupeza zinthu zofunikila. Zimenezi zinathandiza Akristu osaukawo kugwila nchito ya Yehova yocitila umboni mwakhama ndi momasuka.” Colinga cathu n’cofanana ndi cimeneci. Abale athu akayambanso kugwila nchito yolalikila, amalimbikitsa anansi ao ovutika maganizo ndiponso amadzilimbitsa io eni.—Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.

13 Abale ndi alongo ena amene analandila thandizo ngozi itacitika, anayambanso nchito yolalikila, ndipo zimenezi zinalimbitsa cikhulupililo cao. Tamvani zimene io anakamba. M’bale wina anati: “Tinaona kuti unali mwai kuyenda mu ulaliki monga banja. Kutonthoza anthu mu ulaliki kunali kutithandiza kuiwalako za mavuto athu.” Mlongo wina anati: “Kucita zinthu za kuuzimu kunandithandiza kuiwalako za ngozi imene inaticitikila. Zinandithandizanso kukhala ndi mtendele wa m’maganizo.” Mlongo winanso anakamba kuti: “Ngakhale kuti zinali zovuta kukonza zinthu zina, kulalikila kunathandiza banja lathu kukhala ndi ciyembekezo. Kuuza ena za ciyembekezo cathu ca dziko latsopano, kunalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti zinthu zonse zidzakhala zatsopano.”

14 Kupezeka pa misonkhano ndi cinthu cina cimene Akristu ayenela kuyambilanso mwamsanga ngozi ikawacitikila. Ganizilani zimene zinacitikila mlongo wina amene anali ndi zaka pafupifupi 60, dzina lake Kiyoko. Iye anasowa mtengo wogwila pamene zinthu zonse zimene anali nazo zinaonongeka cifukwa ca tsunami, ndipo anangotsala ndi zovala zimene zinali m’thupi. Kenako mkulu wina amamuuza kuti msonkhano wina umene anali kukhala nao mlungu uliwonse adzacitila m’galimoyo yake. Mlongo Kiyoko anati: “Ine, mkuluyo ndi mkazi wake ndiponso mlongo wina tinakhala m’galimoyo. Msonkhanowo unali wacidule, koma zodabwitsa zinali zakuti pamsonkhanopo ndinaiwalako za tsunami, ndipo maganizo anga anakhala m’malo. Msonkhanowo unandithandiza kuona kuti kusonkhana pamodzi n’kofunika kwambili. Pofotokoza za msonkhano umene anacita pambuyo pa ngozi imene inacitika m’dela lao, mlongo wina anati: “Misonkhano inandithandiza kuti cikhulupililo canga cisafooke.”—Aroma 1:11, 12; 12:12.

Utumiki Wopeleka Thandizo Umabweletsa Madalitso Okhalitsa

15, 16. (a) Ndi mapindu otani amene Akristu a ku Korinto ndi kumadela ena anapeza cifukwa copeleka thandizo kwa abale ao? (b) Kodi ifenso timapindula bwanji ndi nchito yopeleka thandizo masiku ano?

15 Pofotokoza za utumiki wopeleka thandizo, Paulo anauzanso Akristu a ku Korinto za mapindu amene io ndi Akristu ena adzakhala nao cifukwa cocita utumikiwu. Iye anati: “Iwo amakupelekelani mapembedzelo kwa Mulungu ndiponso [Akristu aciyuda okhala ku Yerusalemu amene analandila thandizo] amakukondani kwambili cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wakusonyezani.” (2 Akor. 9:14) Akristu aciyuda anali kupemphelela abale ao a ku Korinto, kuphatikizapo anthu a mitundu ina cifukwa ca kuolowa manja kwa Akristu a ku Korintowo. Ndipo zimenezi zinapangitsanso kuti Akristu aciyuda azikonda kwambili abale ao a ku Korinto.

16 Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya December 1, 1945, inafotokoza mau a Paulo okhudza mapindu amene amabwela cifukwa ca nchito yopeleka thandizo masiku ano. Magaziniyo inati: “Anthu odzipeleka a Mulungu m’dela lina akathandiza abale ao osoŵa, onsewo amakhala ogwilizana.” Izi n’zimene zimacitikila amene amagwila nchito yopeleka thandizo pakacitika ngozi. Mwacitsanzo, mkulu wina amene anagwilako nchito yopeleka thandizo m’dela lina limene linasefukila madzi anati: “Kugwila nchito yopeleka thandizo kwa abale kunapangitsa kuti ubwenzi wanga ndi abalewo ulimbe kuposa ndi kale lonse.” Mlongo wina anayamikila kwambili atalandila thandizo pambuyo pa ngozi, ndipo anafokoza kuti: “Kukhala pakati pa abale n’cinthu camtengo wapatali cimene tili naco pamene tikuyembekezela Paladaiso.”—Ŵelengani Miyambo 17:17.

17. (a) Kodi nchito yopeleka thandizo imakwanilitsa bwanji mau a pa Yesaya 41:13? (b) Pelekani zitsanzo zoonetsa mmene nchito yopeleka thandizo imalemekezela Yehova ndi kulimbitsa mgwilizano. (Onani mutu wakuti “Anchito Odzipeleka Padziko Lonse Amathandiza Kwambili.”)

17 Opeleka thandizo akafika m’dela limene mwacitika ngozi, abale athu okhudzidwawo amaona kukwanilitsidwa kwapadela kwa lonjezo la Mulungu lakuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwila dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” (Yes. 41:13) Mlongo wina atapulumuka ngozi imene inacitika m’dela lao anati: “Ndinataya mtima nditaona mmene zinthu zinaonongekela. Koma Yehova anandithandiza. Abalenso anandithandiza kwambili moti sindingathe kufotokoza zonse zimene anandicitila.” Akulu aŵili okhala m’dela lina limene munacitika civomezi analemba kalata moimilako mipingo ya m’delalo. Iwo anati: “Civomezici cinabweletsa mavuto aakulu, koma Yehova anatithandiza kupyolela mwa abale athu. Tinali kungoŵelenga za nchito yopeleka thandizo, koma tsopano tadzionela tokha mmene zimakhalila.”

M’bale Peter Johnson akuthandiza kugwila nchito pa malo omanga nyumba yolambilila

NCHITO IMENE INASINTHA MOYO WAKE

KODI kugwila nchito yopeleka thandizo kungawathandize bwanji acinyamata? Onani zimene zinacitikila mbale Peter Johnson, amene anagwila nchitoyi kwa nthawi yoyamba ali ndi zaka 18. Iye anati: “Ndinakhudzidwa kwambili nditaona cisangalalo ca abale ndiponso cimwemwe cimene ndinali naco cifukwa cothandiza ena. Zimenezi zinandilimbikitsa kukhala ndi colinga cotumikila Yehova ndi mtima wanga wonse.” Ndiyeno Peter anayamba upainiya. Pambuyo pake anakatumikila pa Beteli, ndipo m’kupita kwa nthawi anayamba kutumikila m’Komiti Yoyang’anila Nchito Yomanga Nyumba za Ufumu. Peter anati: “Moyo wanga unasintha kuyambila mu 1974 pamene ndinagwila nao nchito yopeleka thandizo kwa nthawi yoyamba.” Ngati ndinu wacinyamata, kodi mungatengele citsanzo ca Peter? Mwina nchito yopeleka thandizo ingakuthandizeni kuti mugwilitsile nchito moyo wanu wonse kutumikila Yehova.

Kodi Mungagwile Nao Nchitoyi?

18. Mungacite ciani ngati mufuna kugwila nao nchito yopeleka thandizo? (Onani bokosi lakuti “Nchito Imene Inasintha Moyo Wake.”)

18 Kodi mukufuna kupeza cimwemwe cimene anthu amakhala naco cifukwa cogwila nchito yothandiza ena? Ngati n’conco, dziŵani kuti ogwila nchito yopeleka thandizo amasankhidwa pakati pa abale ndi alongo amene amagwila nchito yomanga Nyumba za Ufumu. Conco, uzani akulu mumpingo wanu kuti mukufuna fomu yofunsila utumikiwu. Mkulu wina amene wagwila nchito yothandiza anthu kwa nthawi yaitali anapeleka malangizo akuti: “Muyenela kupita ku dela limene kwacitika ngozi kokha ngati mwauzidwa kutelo ndi Komiti Yoyang’anila za Cithandizo.” Kutsatila malangizo amenewa kumathandiza kuti nchitoyo iziyenda mwadongosolo.

19. Kodi nchito yopeleka thandizo imaonetsa bwanji kuti ndife ophunzila oona a Kristu?

19 Kugwila nchito yopeleka thandizo pakacitika ngozi ndi njila yabwino kwambili yoonetsela kuti timamvela lamulo la Kristu lakuti ‘tizikondana.’ Kukhala ndi cikondi cotelo kumaonetsa kuti ndife ophunzila oona a Kristu. (Yoh. 13:34, 35) Ndi mwai waukulu kukhala ndi abale ambili odzipeleka amene amalemekeza Yehova mwa kugwila nchito yopeleka thandizo kwa anthu ocilikiza Ufumu wa Mulungu mokhulupilika.

a Nkhani ino ikamba za nchito yopeleka thandizo kwa Akristu anzathu. Koma nthawi zambili nchitoyi imapindulitsanso anthu amene si Mboni.—Agal. 6:10.

b Paulo anagwilitsila nchito liu loculukitsa locokela ku liu lakuti di·aʹko·nos (mtumiki) pokamba za “atumiki othandiza.”—1 Tim. 3:12.

c Onani nkhani yakuti “Kuthandiza Banja Lathu la Cikhulupililo mu Bosnia,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1994, tsamba 23 mpaka 27.

Kodi Mumaona Kuti Ufumu wa Mulungu ndi Weniweni?

  • Timadziŵa bwanji kuti nchito yopeleka thandizo pakacitika ngozi ndi mbali ya utumiki wathu wopatulika kwa Yehova?

  • Kodi zolinga zitatu zikuluzikulu za nchito yathu yopeleka thandizo n’ziti?

  • Ndi mapindu okhalitsa ati amene amakhalapo cifukwa ca nchito yopeleka thandizo?

  • Kodi nchito yopeleka thandizo imagwilizana bwanji ndi lamulo la Yesu la pa Yohane 13:34?

ANCHITO ODZIPELEKA PADZIKO LONSE AMATHANDIZA KWAMBILI

PAKATI NDI KUMADZULO KWA AFRICA

Mu 1994, anthu 800,000 kapena kuposelapo a ku Rwanda anaphedwa pa nkhondo ya mitundu. Cifukwa ca nkhondoyo, cipolowe cinafalikila m’maiko ena m’cigawo capakati mu Africa. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu aculuke m’misasa ya anthu othawa kwao. Mboni za Yehova ku Belgium, France, ndi ku Switzerland zinatumiza zovala, mankhwala, matenti, cakudya, ndi katundu wina ku delalo pofuna kuthandiza abale ao. Zinthu zonsezo zinali zokwanila matani 300. Patapita milungu yoŵelengeka, katunduyo anafika kwa abale athu amene anali kuvutika.

Kuonjezela pamenepo, madokotala ndi manesi 10 a Mboni ocokela ku France akhala akupeleka thandizo kwa abale athu amene akukumana ndi mavuto cifukwa ca nkhondo yapaciweniweni, njala, ndi matenda. Pa zaka ziŵili zapitazi, abale ndi alongo amenewa athandiza anthu oposa 10,000. Nchito yao imalemekeza Yehova ndi gulu lake. Mmodzi mwa manesiwo anati: “Tikafika m’dela kukathandiza abale ndi alongo athu, anthu amanena kuti: ‘Awa ndi a Mboni za Yehova. Abwela kudzathandiza abale ao.’” Atathandizidwa ndi mmodzi mwa manesiwo, mlongo wina anakamba mokweza mau kuti: “Zikomo kwambili mlongo wanga. Zikomo kwambili, Yehova.”

Nchito yopeleka thandizo imafunikanso pakacitika ngozi zina. Mwacitsanzo, mu 2012, abale ndi alongo 13 ku Nigeria anafa pa ngozi ya pamsewu, ndipo ena 54 anavulala kwambili. Onse anali a mumpingo umodzi waung’ono. Komiti yopeleka cithandizo inalinganiza zakuti munthu aliyense mwa ovulalawo azisamalidwa bwino nthawi zonse. Wodwala wina m’cipatalamo anadabwa ndi kuculuka kwa thandizo limene abale ndi alongo ovulalawo anali kulandila moti anatumila foni m’busa wake ndi kumuuza kuti: “Palibe aliyense wa kuchalichi cathu amene wabwela kudzandionako. Bwelani kuno ku cipatala mudzaone cikondi ceniceni pakati pa Mboni za Yehova.”

Abale athu mumpingo waung’onowo anavutika mtima kwambili cifukwa ca abale amene anafa pangoziyo, koma anatonthozedwa kwambili ndi Akristu anzao. Ndipo ena mumpingowo anaonjezela utumiki wao ataona kuti abale ao ovulala anasamalidwa ndi kuthandizidwa bwino pamene anali kuvutika. Ngoziyo isanacitike, mpingowo unali ndi ofalitsa 35. Koma patapita caka cimodzi, ciŵelengelo ca ofalitsa cinafika 60.

KU AUSTRALIA

Mu 2013, madela ena a m’mbali mwa nyanja ku Queensland munasefukila madzi, ndipo Mboni zokwana 70 zinalibe malo okhala. M’bale Mark ndi mkazi wake, Rhonda, ndiponso mwana wao wamkazi anasiya nyumba yao cifukwa ca madzi osefukilawo ndi kukakhala m’nyumba yopulumukilamo. M’nyumbayo munali anthu ambili, ndipo Rhonda anati: “Munalibe malo akuti munthu n’kukhala pansi.” Congo cogonthetsa m’khutu ca zipakapaka zimene zinali kubwela ndi kucoka pamalowo cinapangitsa kuti tonsefe tikhale ndi mantha. Cifukwa cothedwa nzelu, iye anafunsa mwamuna wake kuti, “Kodi tidzacita ciani tsopano?” Mark anapemphela kwa Yehova mocokela pansi pamtima kuti awathandize. Rhonda anakamba kuti: “Patapita mphindi pafupifupi 30, galimoto inafika pamalowo, ndipo munatuluka abale atatu. Pamene tinakumana nao, io anati: ‘Tabwela kudzakutengani. Mudzayamba kukhala ku nyumba kwa m’bale wina.’” Rhonda anaonjezela kuti: “Tinali ndi cisangalalo cosaneneka cifukwa cosamalidwa mwacikondi ndi gulu la Yehova.”

Abale odzipeleka oposa 250 anathamangila kumalowo kuti akathandize abale ao. M’bale wina wacikulile anati: “Mwadzidzidzi, gulu la abale linabwela ndi kuyamba kugwila nchito mwakhama yoyeletsa m’nyumba mwathu. Ine ndi mkazi wanga sitidzaiwila mmene abalewo anatithandizila.”

KU BRAZIL

Mu 2008, kusefukila kwa madzi ndi matope m’dela la Santa Catarina kunapangitsa kuti anthu pafupifupi 80,000 acoke ku nyumba zao. Munthu wina wa m’delalo anakamba kuti madziwo anali ngati “tsunami yokokolola nthaka, matupe, ndi mitengo.” Abale ena anathawila m’holo yocitila misonkhano ikuluikulu. M’bale Márcio, amene amayang’anila holoyo anati: “Abalewo analibe ciliconse kupatulapo zovala zam’thupi, ndipo anali matope okhaokha.” Mlongo wina ananena kuti: “Nyumba yathu inagwa.” Zinali zopweteka kwambili kuona nyumbayo ikugwa m’mphindi zocepa cabe. Koma sindidzaiwala mmene abale ndi alongo athu anatitonthozela. Iwo anationetsa cikondi m’njila zosiyanasiyana. Cocitikaci cinandithandiza kuzindikila kuti ndi nzelu kuona zinthu za kuuzimu kukhala zofunika kwambili.”

Mboni za Yehova ku Brazil zikukonza ndi kutumiza zinthu zimene zapelekedwa kuthandiza anthu amene ali kumalo kumene kwagwa tsoka

Holo yocitila misonkhano ikuluikulu ku Santa Catarina, ku Brazil, anaigwilitsila nchito monga malo opelekela thandizo, mu 2009

Kusefukila kwa matope ocoka m’phili kunaononga midzi ya m’mbali mwa phili m’dela lina pafupi ndi mzinda wa Rio de Janeiro. Popeza kuti vutoli limacitika kaŵilikaŵili m’delalo, abale anakhazikitsa Komiti Yoyang’anila za Cithandizo n’colinga cakuti ngozi ikacitika, thandizo lizipelekedwa mwamsanga. Ngati zikuoneka kuti vutoli latsala pang’ono kucitika, abale ena okhala m’dela lokhudzidwalo amafotokozela komitiyi za vutolo. Mwamsanga, abale ndi alongo odzipeleka amabwela pa mathilaki olembedwa kuti “Thandizo la Mboni za Yehova.” Aliyense mwa abale ndi alongo ophunzitsidwa bwino nchito yopulumutsa anthu, amadziŵilatu nchito imene afunika kugwila pakacitika ngozi. Iwo amavala zovala zapadela zowadziŵikitsa kuti ndi Mboni za Yehova. Mogwilizana ndi abale a m’Makomiti Okambilana ndi Acipatala, io amapeleka thandizo kwa abale ndi alongo amene avulala. Ogwila nchito yopeleka thandizo amabwela ndi cakudya, madzi, mankhwala, zovala, sopo ndi zinthu zina zoyeletsela m’nyumba. Nchito yocotsa matope m’nyumba ndi yovuta kwambili. Posacedwapa, matope atasefukilanso m’delalo, panafunika abale ndi alongo 60 kuti acotse matope odzala mathilaki anai m’nyumba imodzi cabe.

KUKONZEKELA ZAKUGWA MWADZIDZIDZI

Bungwe Lolamulila linalangiza maofesi a nthambi onse kuti apeleke malangizo okhudza kukonzekela zakugwa mwadzidzidzi kwa akulu ndi oyang’anila oyendela. Mwacitsanzo, akulu anauzidwa kuti afunika kukhala ndi maadiresi kapena manambala a foni a m’bale ndi mlongo aliyense mumpingo ngakhale ngozi isanacitike.

PAKACITIKA NGOZI

  1. Mkulu wacikristu wafikila ofalitsa kuti adziŵe za umoyo wao

    Akulu amafufuza ofalitsa onse ndi kudziŵa mmene alili

  2. Akulu amapeleka lipoti kwa mgwilizanitsi wa bungwe la akulu

  3. Kulankhulana kumene kumacitika pakati pa agwilizanitsi a mabungwe a akulu, Oyang’anila Oyendela ndi akulu ena, komanso abale a ku ofesi ya nthambi

    Mgwilizanitsi wa bungwe la akulu amapeleka lipoti kwa woyang’anila woyendela ndi abale ena amene amatumikila mogwilizana ndi ofesi ya nthambi

  4. Cakudya ndi madzi

    Abale amapezela okhudzidwawo cakudya, madzi, pogona, ndi mankhwala. Amawatonthoza ndi kuwalimbikitsa mwa kuuzimu

  5. Kupenda malipoti okhudza zinthu zofunika kumene kwagwa tsoka

    Ofesi ya nthambi imapeleka lipoti ku Komiti ya Ogwilizanitsa ya Bungwe Lolamulila

  6. Kutumiza katundu wothandiza kumene kwagwa tsoka

    Komiti Yoyang’anila za Cithandizo imapanga makonzedwe opeleka thandizo loyenelela kwa abale ndi alongo okhudzidwawo

  7. Ndeke ikuuluka

    Komiti ya Ogwilizanitsa imafufuza mmene zinthu zilili, ndipo ngati m’poyenela imapeleka mwai kwa abale ndi alongo a ku maiko ena kuti akathandize

CIDA CINA CA OGWILA NCHITO YOPELEKA THANDIZO

Cikuto ca kabulosha ka mutu wakuti Jehovah’s Witnesses and Disaster Relief

MU June 2013, kunatuluka kabrosha kamutu wakuti Jehovah’s Witnesses and Disaster Relief (Nchito ya Mboni za Yehova Pakacitika Ngozi). Kabrosha kameneka kanakonzedwela akuluakulu a boma omwe amayang’anila nchito yopeleka thandizo pakagwa zamwadzidzidzi ku United States. Kabroshaka kamafotokoza za nchito imene takhala tikugwila pakagwa zamwadzidzidzi kuyambila ca m’ma 1940. Kalinso ndi mapu osonyeza kumene nchito yathu yopeleka thandizo yakhala ikucitika pa dziko lonse. Mkulu wina amene wakhala akugwila nchito imeneyi anati: “Abale amene amatumikila m’Makomiti Oyang’anila za Cithandizo amagwilitsila nchito kabroshaka kuti adziŵane pasadakhale ndi akuluakulu a boma a kumadela kumene kumacitika masoka kaŵilikaŵili. Akuluakulu a boma akadziŵilatu za nchito yathu, zimakhala zosavuta kwa ife kupempha cilolezo cokathandiza abale athu kumalo kumene kwacitika ngozi.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani